Kalata Yachitatu ya Yohane 1:1-14

  • Moni komanso pemphero (1-4)

  • Anayamikira Gayo (5-8)

  • Diotirefe wodzikuza (9, 10)

  • Demetiriyo anamuchitira umboni kuti ankachita zabwino (11, 12)

  • Kukonza zoti akawachezere; kuwapatsa moni (13, 14)

1  Ine monga munthu wachikulire,* ndikulembera mʼbale wokondedwa Gayo, amene ndimamukonda kwambiri. 2  Wokondedwa, ndikupemphera kuti zinthu zonse zipitirize kukuyendera bwino ndiponso kuti ukhale wathanzi monga mmene zilili panopa. 3  Ndinasangalala kwambiri abale atabwera nʼkundiuza za choonadi chomwe uli nacho, pamene ukupitiriza kuyenda mʼchoonadi.+ 4  Palibe chimene chimandisangalatsa kwambiri* kuposa kumva kuti ana anga akuyendabe mʼchoonadi.+ 5  Wokondedwa, ukusonyeza kuti ndiwe wokhulupirika pa chilichonse chimene ukuchitira abale, ngakhale amene sukuwadziwa nʼkomwe.+ 6  Abalewa afotokozera mpingo* za chikondi chako. Anthu oterewa akamachoka, uziyesetsa kuwathandiza mʼnjira imene Mulungu angasangalale nayo,+ 7  chifukwa anapita kukalalikira za dzina la Mulungu, ndipo sankayembekezera kulandira chilichonse+ kuchokera kwa anthu a mitundu ina. 8  Choncho, ndi udindo wathu kuwalandira bwino anthu amenewa+ komanso kuwachereza, kuti akhale antchito anzathu polengeza choonadi.+ 9  Mpingo wanu ndinaulembera kalata, koma Diotirefe amene amakonda kukhala woyamba pakati panu,+ salemekeza chilichonse chimene tanena.+ 10  Nʼchifukwa chake ndikadzabwera, ndidzaulula zimene akuchita pofalitsa mabodza onena za ife.+ Ndipo chifukwa chosakhutira ndi zimenezi, amakana kulandira abale+ mwaulemu. Komanso anthu amene amafuna kuwalandira, amayesa kuwatsekereza ndiponso kuwachotsa mumpingo. 11  Wokondedwa, usamatsanzire anthu ochita zoipa, mʼmalomwake uzitsanzira anthu amene amachita zabwino.+ Amene amachita zabwino amayendera maganizo a Mulungu.+ Koma amene amachita zoipa sadziwa Mulungu.+ 12  Anthu onse akhala akumuchitira umboni Demetiriyo. Komanso zochita zake zogwirizana ndi choonadi zimamuchitira umboni. Ifenso tikumuchitira umboni, ndipo ukudziwa kuti umboni umene timapereka ndi woona. 13  Ndinali ndi zambiri zoti ndikuuze, koma sindikufuna kuti ndipitirize kukulembera zimenezi ndi cholembera komanso inki. 14  Koma ndikuganiza kuti tionana posachedwapa ndipo tidzalankhulana pamasomʼpamaso. Mtendere ukhale nawe. Abale kuno akukupatsa moni. Iwenso undiperekere moni kwa abale kumeneko, aliyense payekhapayekha.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Ine monga mkulu.”
Mabaibulo ena amati, “Palibe chinthu chimene chimandichititsa kuyamikira.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Abalewa achitira umboni kumpingo.”