Salimo 68:1-35
Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo ndi nyimbo ya Davide.
68 Mulungu anyamuke, adani ake amwazike,Ndipo amene amadana naye athawe pamaso pake.+
2 Mofanana ndi mphepo imene imathamangitsa utsi, inunso muwathamangitsire kutali.Mofanana ndi phula limene limasungunuka pamoto,Anthu oipa awonongeke pamaso pa Mulungu.+
3 Koma olungama asangalale,+Asangalale kwambiri pamaso pa Mulungu,Adumphe ndi chisangalalo.
4 Imbirani Mulungu, muimbireni nyimbo zotamanda dzina lake.+
Imbirani Iye amene akudutsa mʼchipululu.*
Dzina lake ndi Ya.*+ Sangalalani pamaso pake.
5 Bambo wa ana amasiye komanso amene amateteza* akazi amasiye+Ndi Mulungu amene amakhala mʼmalo ake oyera.+
6 Anthu amene alibe wowathandiza, Mulungu amawapatsa nyumba kuti azikhalamo.+Amamasula akaidi nʼkuwathandiza kuti zinthu ziwayendere bwino.+
Koma anthu osamvera* adzakhala mʼdziko louma.+
7 Inu Mulungu, pamene munkatsogolera anthu anu,+Pamene munkadutsa mʼchipululu, (Selah)
8 Dziko lapansi linagwedezeka,+Kumwamba kunagwa mvula chifukwa cha inu Mulungu,Phiri la Sinai ili linagwedezeka chifukwa cha inu Mulungu, Mulungu wa Isiraeli.+
9 Inu Mulungu, munagwetsa mvula yokwanira.Munapatsa mphamvu anthu anu amene anali ofooka.*
10 Iwo ankakhala mʼmudzi wanu wamatenti.+Inu Mulungu, chifukwa chakuti ndinu wabwino, munapereka zinthu zofunika kwa anthu osauka.
11 Yehova wapereka lamulo* kwa anthu ake,Ndipo akazi amene akulengeza uthenga wabwino* ndi gulu lalikulu.+
12 Mafumu okhala ndi magulu a asilikali amathawa,+ ndithu amathawadi.
Mkazi amene amangokhala pakhomo, amalandira nawo zinthu zimene zalandidwa kunkhondo.+
13 Ngakhale anthu inu mutagona pambali pa moto mumsasa,Mudzalandira njiwa imene mapiko ake ndi okutidwa ndi siliva,Ndipo nthenga zakumapeto a mapiko ake ndi zagolide woyenga bwino.*
14 Pamene Wamphamvuyonse anamwaza mafumu amʼdzikomo,+Mu Zalimoni munagwa sinowo.*
15 Phiri la ku Basana+ ndi phiri la Mulungu.*Phiri la ku Basana ndi phiri lansonga zitalizitali.
16 Nʼchifukwa chiyani inu mapiri ansonga zitalizitali mumayangʼana mwansanjePhiri limene Mulungu wasankha* kuti azikhalamo?+
Ndithudi, Yehova adzakhala mʼphiri limenelo mpaka kalekale.+
17 Magaleta ankhondo a Mulungu ali mʼmagulu a masauzande osawerengeka, ali mʼmagulu masauzandemasauzande.+
Yehova walowa mʼmalo oyera kuchokera kuphiri la Sinai.+
18 Munakwera pamalo apamwamba.+Munatenga anthu ogwidwa ukapolo.Munatenga amuna kuti akhale mphatso,+Ndithu inu Ya,* Mulungu wathu, mwatenga ngakhale anthu osamvera+ kuti mukhale pakati pawo.
19 Atamandike Yehova, amene amanyamula katundu wathu tsiku ndi tsiku,+Mulungu woona amene amatipulumutsa. (Selah)
20 Mulungu woona ndi Mulungu amene amatipulumutsa.+Ndipo Yehova Ambuye Wamkulu Koposa amatipulumutsa ku imfa.+
21 Ndithudi, Mulungu adzaphwanya mitu ya adani ake,Adzaphwanya mutu wa aliyense amene akupitiriza* kuchita machimo.+
22 Yehova wanena kuti: “Ndidzawabweza kuchokera ku Basana,+Ndidzawatulutsa mʼnyanja yakuya,
23 Kuti mapazi anu aponde magazi a adani anu,+Ndiponso kuti malilime a agalu anu anyambite magazi a adani anu.”
24 Iwo aona magulu a anthu anu akuyendera pamodzi, inu Mulungu,Magulu a anthu oyendera pamodzi a Mulungu wanga, Mfumu yanga, akulowa kumalo opatulika.+
25 Oimba nyimbo akuyenda patsogolo, oimba zoimbira za zingwe akuyenda pambuyo pawo,+Pakati pali atsikana amene akuimba maseche.+
26 Pamisonkhano tamandani Mulungu,Tamandani Yehova, inu nonse amene moyo wanu ukuchokera mu Kasupe wa Isiraeli.+
27 Pali fuko lalingʼono la Benjamini+ limene likugonjetsa anthu,Pali akalonga a Yuda pamodzi ndi chigulu chawo chimene chikuchita phokoso,Palinso akalonga a Zebuloni komanso akalonga a Nafitali.
28 Mulungu wanu waganiza kuti akupatseni mphamvu.
Sonyezani mphamvu zanu, Inu Mulungu, amene mumatithandiza.+
29 Chifukwa cha kachisi wanu yemwe ali ku Yerusalemu,+Mafumu adzabweretsa mphatso kwa inu.+
30 Dzudzulani nyama zakutchire zimene zimakhala mʼmabango,Gulu la ngʼombe zamphongo+ limodzi ndi ana awo,Mpaka mitundu ya anthu itagwada nʼkubweretsa ndalama zasiliva.
Koma iye wabalalitsa mitundu ya anthu imene imasangalala ndi nkhondo.
31 Zinthu zopangidwa ndi kopa* zidzabwera kuchokera* ku Iguputo,+Mwamsanga, dziko la Kusi lidzapereka mphatso kwa Mulungu.
32 Inu maufumu a dziko lapansi, imbirani Mulungu,+Imbani nyimbo zotamanda Yehova, (Selah)
33 Imbirani iye amene wakwera pamwamba pa kumwamba,+ kumene kwakhalapo kuyambira kalekale.
Mawu ake amphamvu amamveka ngati bingu.
34 Vomerezani kuti Mulungu ndi wamphamvu zochuluka.+
Ulemerero wake uli pa Isiraeli,Ndipo amasonyeza mphamvu zake kuchokera kumwamba.*
35 Mulungu walamula kuti anthu amuope komanso amupatse ulemu mʼmalo ake opatulika aulemerero.+
Iye ndi Mulungu wa Isiraeli,Amene amapereka mphamvu ndi nyonga kwa anthu.+
Mulungu atamandike.
Mawu a M'munsi
^ Mabaibulo ena amati, “akudutsa mʼmitambo.”
^ “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “amaweruzira milandu.”
^ Kapena kuti, “opanduka.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “cholowa chanu chimene chinali chofooka.”
^ Limeneli ndi lamulo loti apite kunkhondo.
^ Umenewu ndi uthenga wonena za kupambana pankhondo.
^ Kapena kuti, “ndi zagilini wopitira kuyelo.”
^ Mabaibulo ena amati, “Zinali ngati matalala akugwa pa Zalimoni.” Kapena kuti, “chipale chofewa.”
^ Kapena kuti, “phiri laulemerero.”
^ Kapena kuti, “wafuna.”
^ “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.
^ Kapena kuti, “amene akuyenda mʼnjira yochimwa.”
^ Kapena kuti, “mkuwa.”
^ Mabaibulo ena amati, “Nthumwi zidzachokera ku.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmitambo.”