Salimo 90:1-17
Pemphero la Mose, munthu wa Mulungu woona.+
90 Inu Yehova, mwakhala malo athu okhalamo+ ku mibadwo yonse.
2 Mapiri asanabadwe,Kapena musanakhazikitse dziko lapansi komanso nthaka,+Inu ndinu Mulungu kuyambira kalekale mpaka kalekale.+
3 Mumabwezera munthu kufumbi,Mumanena kuti: “Bwererani kufumbi, inu ana a anthu.”+
4 Chifukwa kwa inu zaka 1,000 zili ngati dzulo lapitali,+Zili ngati ulonda umodzi wa usiku.
5 Mumawawononga+ ndipo amatha ngati tulo.Mʼmawa amakhala ngati msipu umene waphukira.+
6 Mʼmawa umaphuka ndipo umabiriwira,Koma madzulo umafota kenako nʼkuuma.+
7 Chifukwa ife tawonongedwa ndi mkwiyo wanu,+Ndipo tikuchita mantha kwambiri ndi ukali wanu.
8 Mumaika zolakwa zathu patsogolo panu,*+Zinsinsi zathu zaululika chifukwa cha kuwala kwa nkhope yanu.+
9 Moyo wathu ukutha chifukwa cha mkwiyo wanu.Timafa msanga ngati mpweya umene umatha mofulumira.
10 Masiku a moyo wathu amangokwana zaka 70Kapena 80+ ngati munthu ali ndi mphamvu zambiri.*
Koma zimakhala zodzaza ndi mavuto komanso chisoni.Zimatha mofulumira ndipo moyo wathu umachoka.+
11 Ndi ndani angadziwe kuchuluka kwa mphamvu za mkwiyo wanu?
Ukali wanu ndi waukulu mofanana ndi mantha amene tikuyenera kukusonyezani.+
12 Tiphunzitseni mmene tingagwiritsire ntchito bwino moyo wathu*+Kuti tikhale ndi mtima wanzeru.
13 Bwererani, inu Yehova!+ Kodi zinthu zikhala chonchi mpaka liti?+
Timvereni chisoni ife atumiki anu.+
14 Mʼmawa, muzitisonyeza chikondi chanu chokhulupirika,+Kuti tizifuula mokondwera komanso kukhala mosangalala+ masiku onse a moyo wathu.
15 Tichititseni kuti tisangalale kwa masiku ofanana ndi masiku amene mwatisautsa,+Kwa zaka zofanana ndi zaka zimene takumana ndi masoka.+
16 Atumiki anu aone ntchito zanu,Ndipo ana awo aone ulemerero wanu.+
17 Yehova Mulungu wathu atikomere mtima.Chititsani kuti ntchito ya manja athu iyende bwino.*
Inde, chititsani kuti ntchito ya manja athu iyende bwino.*+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “Mukudziwa zolakwa zathu.”
^ Kapena kuti, “zapadera.”
^ Kapena kuti, “mmene tingawerengere masiku athu.”
^ Kapena kuti, “Khazikitsani ntchito ya manja athu.”
^ Kapena kuti, “khazikitsani ntchito ya manja athu.”