Yesaya 39:1-8
-
Amithenga ochokera ku Babulo (1-8)
39 Pa nthawi imeneyo, Merodaki-baladani mwana wa Baladani mfumu ya Babulo, anatumiza makalata ndi mphatso kwa Hezekiya+ chifukwa anamva kuti amadwala ndipo wachira.+
2 Hezekiya analandira anthuwo mwansangala* ndipo anawaonetsa nyumba yake yosungiramo chuma.+ Anawaonetsa siliva, golide, mafuta a basamu, mafuta ena amtengo wapatali, nyumba yake yosungiramo zida zonse zankhondo ndiponso chuma chake chonse. Palibe chimene Hezekiya sanawaonetse mʼnyumba* yake ndi mu ufumu wake wonse.
3 Kenako mneneri Yesaya anapita kwa Mfumu Hezekiya nʼkuifunsa kuti: “Kodi anthu aja anena kuti chiyani, nanga anachokera kuti?” Hezekiya anayankha kuti: “Anachokera kudziko lakutali, ku Babulo.”+
4 Atatero Yesaya anafunsa kuti: “Aona chiyani mʼnyumba mwanu?” Hezekiya anayankha kuti: “Aona chilichonse chimene chili mʼnyumba mwanga. Palibe chimene sindinawaonetse pa chuma changa.”
5 Ndiyeno Yesaya anauza Hezekiya kuti: “Imva zimene Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena,
6 ‘Tamvera, masiku akubwera pamene zinthu zonse zimene zili mʼnyumba mwako ndiponso zonse zimene makolo ako akhala akusunga mpaka lero, anthu adzazitenga nʼkupita nazo ku Babulo. Palibe chidzatsale,’+ watero Yehova.+
7 ‘Ena mwa ana ako, amene iweyo udzabereke, adzatengedwa ndipo adzakhala nduna zapanyumba ya mfumu ya ku Babulo.’”+
8 Hezekiya atamva zimenezi anauza Yesaya kuti: “Mawu a Yehova amene mwanenawa ndi abwino.” Anapitiriza kuti: “Chifukwa mʼmasiku anga mukhala bata* ndi mtendere.”+
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “anasangalala.”
^ Kapena kuti, “nyumba yachifumu.”
^ Kapena kuti, “choonadi.”