Wolembedwa ndi Yohane 1:1-51
1 Pachiyambi, panali wina amene ankadziwika kuti Mawu,+ ndipo Mawuyo anali ndi Mulungu+ komanso Mawuyo anali mulungu.*+
2 Ameneyu anali ndi Mulungu kuyambira pachiyambi.
3 Zinthu zonse zinakhalako kudzera mwa iye+ ndipo palibe chinthu ngakhale chimodzi chimene chinakhalapo popanda iyeyo.
4 Moyo unakhalapo kudzera mwa iye ndipo moyowo unali kuwala kounikira anthu.+
5 Kuwalako kukuunika mumdima+ koma mdimawo sunagonjetse kuwalako.
6 Kunabwera munthu wina amene anatumidwa monga nthumwi ya Mulungu. Dzina lake anali Yohane.+
7 Munthu ameneyu anabwera ngati mboni, kuti adzachitire umboni za kuwala+ nʼcholinga chakuti anthu osiyanasiyana akhulupirire kudzera mwa iye.
8 Sikuti iyeyu anali kuwalako,+ koma anangobwera kudzachitira umboni za kuwalako.
9 Kuwala kwenikweni kumene kumaunikira anthu osiyanasiyana kunali kutatsala pangʼono kubwera mʼdziko.+
10 Iye anali mʼdziko+ ndipo dziko linakhalapo kudzera mwa iye,+ koma dzikolo silinamudziwe.
11 Anabwera kudziko lakwawo, koma anthu akwawo enieniwo sanamulandire.
12 Komabe onse amene anamulandira, anawapatsa mphamvu kuti akhale ana a Mulungu,+ chifukwa choti ankakhulupirira dzina lake.+
13 Iwowa sanabadwe kuchokera mwa anthu kapena chifukwa cha kufuna kwa anthu kapenanso chifukwa cha kufuna kwa munthu, koma anabadwa kuchokera kwa Mulungu.+
14 Choncho Mawu ameneyo anakhala ndi thupi la nyama+ ndipo ankakhala pakati pathu. Ife tinaona ulemerero wake, ulemerero wofanana ndi umene mwana wobadwa yekha+ amalandira kuchokera kwa bambo ake. Mulungu ankamukomera mtima kwambiri* komanso ankaphunzitsa choonadi.
15 (Yohane ankachitira umboni za iye, moti ankachita kufuula kuti: “Uyu ndi amene ndinkanena uja kuti, ‘Amene akubwera mʼmbuyo mwangamu ndi wamkulu kuposa ine, chifukwa anakhalapo ine ndisanabadwe.’”)+
16 Chifukwa chakuti anali ndi kukoma mtima kwakukulu, nthawi zonse tinkalandira kukoma mtima kwakukulu kosefukira.
17 Popeza Chilamulo chinaperekedwa kudzera mwa Mose,+ kukoma mtima kwakukulu+ komanso choonadi zinakhalako kudzera mwa Yesu Khristu.+
18 Palibe munthu amene anaonapo Mulungu ndi kale lonse,+ mulungu wobadwa yekha+ amene ali pambali pa Atate*+ ndi amene anafotokoza za Mulungu.+
19 Yohane anapereka umboni pamene Ayuda anatumiza ansembe ndi Alevi kuchokera ku Yerusalemu kukamufunsa kuti: “Kodi ndiwe ndani?”+
20 Iye anavomera ndipo sanakane. Ananena kuti: “Ine si Khristu.”
21 Iwo anamufunsa kuti: “Nanga ndiwe ndani? Ndiwe Eliya kapena?”+ Iye anayankha kuti: “Ayi.” “Kapena ndiwe Mneneri?”+ Iye anayankha kuti: “Ayi!”
22 Choncho iwo anamufunsa kuti: “Nanga ndiwe ndani? Tiuze kuti tikathe kupereka yankho kwa amene atituma. Mwiniwakewe umati ndiwe ndani?”
23 Iye anati: “Ndine mawu a winawake amene akufuula mʼchipululu kuti, ‘Wongolani njira ya Yehova,’*+ monga mmene mneneri Yesaya ananenera.”+
24 Anthuwo anatumidwa ndi Afarisi.
25 Choncho anamufunsa kuti: “Nanga nʼchifukwa chiyani umabatiza anthu ngati iweyo si iwe Khristu, Eliya kapena Mneneri?”
26 Yohane anawayankha kuti: “Ine ndimabatiza mʼmadzi. Pakati panu paimirira wina amene inu simukumudziwa.
27 Iye ndi amene akubwera mʼmbuyo mwangamu ndipo ine si woyenera kumasula zingwe za nsapato zake.”+
28 Zinthu zimenezi zinachitikira ku Betaniya, kutsidya la Yorodano, kumene Yohane ankabatiza anthu.+
29 Tsiku lotsatira anaona Yesu akubwera kwa iye, ndipo anati: “Taonani, Mwanawankhosa+ wa Mulungu amene akuchotsa uchimo+ wa dziko!+
30 Uyu ndi amene ndinkanena uja kuti: ‘Amene akubwera mʼmbuyo mwangamu ndi wamkulu kuposa ine,* chifukwa anakhalapo ine ndisanabadwe.’+
31 Inenso sindinkamudziwa, koma chifukwa chimene ndikubatizira anthu mʼmadzi nʼchakuti iyeyu aonekere kwa Isiraeli.”+
32 Yohane anachitiranso umboni kuti: “Ndinaona mzimu ukutsika ngati nkhunda kuchokera kumwamba ndipo unakhalabe pa iye.+
33 Inenso sindinkamudziwa, koma Mulungu amene anandituma kudzabatiza mʼmadzi anandiuza kuti: ‘Ukadzaona mzimu ukutsika nʼkukhazikika pamunthu wina,+ ameneyo ndi amene amabatiza ndi mzimu woyera.’+
34 Ine ndinaonadi zimenezo ndipo ndachitira umboni kuti iyeyu ndi Mwana wa Mulungu.”+
35 Tsiku lotsatira Yohane analinso ataima ndi ophunzira ake awiri,
36 ndipo ataona Yesu akuyenda, ananena kuti: “Onani, Mwanawankhosa+ wa Mulungu!”
37 Ophunzira awiriwo atamumva akunena zimenezi, anatsatira Yesu.
38 Kenako Yesu anacheuka, ndipo atawaona akumutsatira, anawafunsa kuti: “Kodi mukufunafuna chiyani?” Iwo anati: “Rabi, (dzina limeneli akalimasulira limatanthauza, “Mphunzitsi”) kodi mumakhala kuti?”
39 Iye anawauza kuti: “Tiyeni mukaoneko.” Choncho anapita kukaona kumene ankakhala ndipo anakhala naye tsiku limenelo. Apa nʼkuti nthawi ili cha mʼma 4 koloko madzulo.*
40 Andireya,+ mchimwene wake wa Simoni Petulo anali mmodzi wa awiriwo, amene anamva zimene Yohane ananena nʼkutsatira Yesu.
41 Choyamba iyeyu anakumana ndi mchimwene wake Simoni ndipo anamuuza kuti: “Ifetu tapeza Mesiya”+ (dzina limeneli akalimasulira limatanthauza, “Khristu”),
42 ndipo anapita naye kwa Yesu. Yesu atamuyangʼana anati: “Iwe ndiwe Simoni+ mwana wa Yohane, dzina lako likhala Kefa” (limene kumasulira kwake ndi “Petulo”).+
43 Tsiku lotsatira, Yesu anaganiza zoti apite ku Galileya. Ndiyeno anakumana ndi Filipo+ nʼkumuuza kuti: “Ukhale wotsatira wanga.”
44 Filipo anali wochokera ku Betsaida, mzinda umene kunkachokera Andireya ndi Petulo.
45 Kenako Filipo anakumana ndi Natanayeli+ nʼkumuuza kuti: “Ife tapeza Yesu, mwana wa Yosefe,+ wa ku Nazareti. Chilamulo cha Mose komanso zimene aneneri analemba zimanena za iyeyu.”
46 Koma Natanayeli anamufunsa kuti: “Kodi mu Nazareti mungatuluke munthu aliyense wabwino?” Filipo anamuuza kuti: “Tiye ukaone.”
47 Yesu ataona Natanayeli akubwera kumene iye anali, ananena kuti: “Onani Mwisiraeli ndithu, amene mwa iye mulibe chinyengo.”+
48 Natanayeli anamufunsa kuti: “Mwandidziwa bwanji?” Yesu anamuyankha kuti: “Filipo asanakuitane, ine ndinakuona uli pansi pa mtengo wamkuyu paja.”
49 Natanayeli anamuyankha kuti: “Rabi, ndinu Mwana wa Mulungu, ndinu Mfumu ya Isiraeli.”+
50 Yesu anamuyankha kuti: “Kodi wakhulupirira chifukwa choti ndakuuza kuti ndinakuona uli pansi pa mtengo wamkuyu? Udzaona zinthu zazikulu kuposa zimenezi.”
51 Kenako anamuuza kuti: “Ndithu ndikukuuzani anthu inu, mudzaona kumwamba kutatseguka, angelo a Mulungu akukwera ndi kutsika kupita kumene kuli Mwana wa munthu.”+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “anali ngati mulungu.”
^ Kapena kuti, “ankamusonyeza kukoma mtima kwakukulu.”
^ Kapena kuti, “pachifuwa cha Atate.” Izi zikusonyeza kuti ankakondedwa mwapadera.
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Kapena kuti, “mwangamu wandipitirira.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “ola la 10,” kuwerenga kuchokera mʼma 6 koloko mʼmawa.