FUNSO 18
Kodi Mungatani Kuti Mukhale pa Ubwenzi ndi Mulungu?
“Inu Wakumva pemphero, anthu a mitundu yonse adzabwera kwa inu.”
“Uzikhulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usamadalire luso lako lomvetsa zinthu. Uzimukumbukira mʼnjira zako zonse, ndipo iye adzawongola njira zako.”
“Moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ndi woona, komanso za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.”
“Kwenikweni [Mulungu] sali kutali ndi aliyense wa ife.”
“Ine ndikupitiriza kupemphera kuti chikondi chanu chipitirize kukula kwambiri, limodzi ndi kudziwa zinthu molondola komanso kuzindikira zinthu bwino kwambiri.”
“Ngati wina akusowa nzeru, azipempha kwa Mulungu ndipo adzamupatsa, chifukwa iye amapereka mowolowa manja kwa onse ndiponso amapereka mosatonza.”
“Yandikirani Mulungu ndipo iyenso adzakuyandikirani. Yeretsani manja anu ochimwa inu, ndipo yeretsani mitima yanu okayikakayika inu.”
“Kukonda Mulungu kumatanthauza kutsatira malamulo ake, ndipo malamulo akewo si ovuta kuwatsatira.”