Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingachite Chiyani Ngati Banja Lathu Ndi Losauka?

Kodi Ndingachite Chiyani Ngati Banja Lathu Ndi Losauka?

Mutu 20

Kodi Ndingachite Chiyani Ngati Banja Lathu Ndi Losauka?

Gregory, mnyamata yemwe amakhala m’dziko lina lakum’mawa kwa Ulaya sangakwanitse kugula zovala ndiponso zipangizo zamagetsi zimene achinyamata anzake a m’mayiko olemera ali nazo. Iye sakusangalala ndi moyo wakwawo ndipo akufuna kusamukira ku dziko la Austria. Kodi mukuganiza kuti Gregory ndi wosauka?

□ Inde □ Ayi

Mnyamata wina dzina lake Loyiso amakhala m’dera lakumidzi, m’dziko lina lakum’mwera kwa Africa, komwe ndi kutali kwambiri ndi kwawo kwa Gregory. Banja la Loyiso limakhala m’kanyumba kakang’ono kaudzu, ndipo iye amasirira achinyamata anzake amene amakhala m’tawuni yakufupi ndi kwawo. Achinyamata enawo amakhala m’nyumba zomwe zili ndi madzi ndiponso magetsi. Kodi mungati Loyiso ndi wosauka?

□ Inde □ Ayi

N’ZODZIWIKIRATU kuti “kusauka” kumatengera dera limene munthu akukhala. Mwachitsanzo, n’kutheka kuti Gregory amadziona kuti ndi wosauka kwambiri, koma tikamuyerekezera ndi Loyiso, Gregory ndi wolemera. N’zochititsa chidwi kudziwa kuti ngakhale munthu atakhala wosauka kwambiri, pamakhala enanso osaukitsitsa kuposa iyeyo. Komabe, ngati mulibe zovala zabwino za kusukulu kapena simukhala m’nyumba imene ili ndi madzi momwemo, mwina zingakuvuteni kuvomereza mfundo yakuti pali ena osaukitsitsa kuposa inuyo.

Achinyamata ena amene anakulira m’banja losauka amadziona ngati anthu opanda pake ndipo amayesa kuzemba mavuto awo pogwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo ndiponso kumwa mowa. Komabe kuchita zinthu ngati zimenezi kumangowonjezera mavutowo. Ndipo m’kupita kwanthawi, anthu amene amamwa mowa mwauchidakwa amazindikira kuti ‘umaluma ngati njoka, [ndiponso] umajompha ngati mamba.’ (Miyambo 23:32) Mtsikana wina wa ku South Africa dzina lake Maria, amene analeredwa ndi mayi ake okha anati, “Kuyesa kuzemba mavuto m’moyo sikuthandiza kuthetsa mavutowo koma kumangowawonjezera.”

Mwina inu simungayambe kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo kapena kumwa mowa poyesa kuzemba mavuto anu, komabe n’kutheka kuti mulibe chiyembekezo chilichonse choti zinthu zidzakhala bwino m’moyo wanu. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni? Malangizo a m’Baibulo akhoza kukuthandizani kuti mumasuke ku vuto lodziona ngati ndinu munthu wachabechabe. Tiyeni tione mmene Baibulo lingakuthandizireni.

Zindikirani Zinthu Zofunika Zimene Muli Nazo

Chimodzi mwa zinthu zofunika kwambiri chimene mungachite ndicho kuganizira za zinthu zimene muli nazo, osati zimene mulibe. Zinthu monga nyumba ndiponso makolo ndi achibale anu amene amakukondani ndi zofunika kwambiri kuposa ndalama. Mwambi wina wa m’Baibulo umati: “Kudya masamba, pali chikondano, kuposa ng’ombe yonenepa pali udani.” (Miyambo 15:17) Ndipo Akhristu achinyamata ali ndi chinthu china chofunika kwambiri chomwe ndi “gulu lonse la abale” limene likhoza kuwathandiza.—1 Petulo 2:17.

Chinanso chimene mungachite ndicho kuphunzira kukhala wokhutira ndi zimene muli nazo. Mwina mukukhala m’nyumba yosaoneka bwino, ndipo mumavala zovala zakale, zong’ambika ndiponso zazigamba. Mwinanso mumasirira zakudya zosiyanasiyana zapamwamba. Koma kodi kutumikira Mulungu kumafuna kuti mukhale ndi zinthu zapamwamba monga zovala kapena nyumba? Kodi mumafunika zakudya zapamwamba kuti mukhale ndi moyo komanso thanzi labwino? Ayi. Mtumwi Paulo anaphunzira mfundo yabwino kwambiri pankhani imeneyi, chifukwa pamoyo wake anakhalapo ndi zinthu zochuluka komanso zochepa. (Afilipi 4:12) N’chifukwa chake iye anati: ‘Pokhala ndi chakudya, zovala ndi nyumba, tizikhala okhutira ndi zinthu zimenezi.’—1 Timoteyo 6:8.

Eldred, amene amakhala ku South Africa, anakulira m’banja losauka kwambiri. Iye anati: “Tinangovomereza kuti ndife osauka basi ndipo sitingathe kugula zinthu zonse zimene tikufuna.” Eldred amakumbukira kuti thalauza lake la kusukulu likang’ambika, mayi ake ankangolisokerera zigamba. Iye anati: “Anzanga ankandiseka kwambiri, komabe kwa ine chofunika kwambiri chinali choti ndavala, komanso zovalazo n’zochapa bwino.”

Muzidziona Kuti Ndinu Wofunika

James ali ndi zaka 11 ndipo amakhala ndi mayi ake ndiponso mlongo wake m’dera lina la anthu osauka kwambiri pafupi ndi mzinda wa Johannesburg, ku South Africa. Iwo ndi osauka kwambiri moti alibe katundu aliyense. Komabe James ali ndi zinthu zofunika kwambiri, zomwe ndi nthawi ndiponso nyonga, ndipo amasangalala kuzigwiritsa ntchito pothandiza anthu ena. Loweruka ndi Lamlungu lililonse, James wakhala akuthandiza nawo pantchito yomanga Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova ya kwawoko. Ntchito imeneyi yamuthandiza kukhala ndi zochita zaphindu komanso kumva kuti ndi munthu wofunika. Iye anati: “Ndikamaweruka pantchito yomangayi ndimakhala wokhutira kuti ndachita zinthu zotamandika kwambiri.”

Ntchito inanso yaphindu kwambiri ndi yolalikira khomo ndi khomo. (Mateyo 24:14) Achinyamata ambiri a Mboni za Yehova amagwira nawo ntchito imeneyi nthawi zonse. Akamatero amathandiza ena kukhala ndi chiyembekezo choti m’tsogolo zinthu zidzakhala bwino, komanso zimathandiza achinyamatawa kudziona kuti ndi ofunika. N’zoona kuti salipidwa pantchitoyi, koma kumbukirani zimene Yesu anauza Akhristu a ku mpingo wa Simuna. Iwo anali osauka kwambiri koma anali anthu okonda zinthu zauzimu. Chifukwa cha zimenezi, Yesu anawauza kuti: “Ndikudziwa chisautso chako ndi umphawi wako, koma ndiwe wolemera.” M’kupita kwanthawi, Akhristu amenewa anadzakhala olemera kwambiri popeza analandira kolona wa moyo wosafa, chifukwa chakuti anakhulupirira magazi okhetsedwa a Yesu.—Chivumbulutso 2:9, 10.

Ganizirani za M’tsogolo

Kaya ndinu wosauka kapena wolemera mungathe kukhala ndi ubwenzi wabwino kwambiri ndi Yehova. Baibulo limati: “Wolemera ndi wosauka akumana, wolenga onsewo ndiye Yehova.” (Miyambo 22:2) Mfundo imeneyi yathandiza achinyamata ambiri a Mboni za Yehova kupirira umphawi. Iwo amadziwa kuti kukhala paubwenzi ndi Yehova Mulungu, yemwe amafuna kuti anthu onse azim’tumikira, n’komwe kumachititsa munthu kukhala wosangalala, osati kukhala ndi chuma. M’tsogolo muno, Mulungu adzabweretsa dziko lapansi latsopano lomwe lidzakhala lopanda umphawi.—2 Petulo 3:13; Chivumbulutso 21:3, 4.

Panopa muzigwiritsa ntchito mwanzeru zinthu zimene muli nazo. Komanso muziganizira za madalitso a m’tsogolo ndiponso yesetsani kukundika chuma kumwamba. (Mateyo 6:19-21) Dziwani kuti umphawi ndi vuto limene mungathe kupirira.

LEMBA LOFUNIKA

“Ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka chotani, moyo wake suchokera m’zinthu zimene ali nazo.”—Luka 12:15.

KODI MUKUDZIWA . . . ?

Ngakhale mutakhala wosauka, kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo kungakuthandizeni kukhala wokhutira ndi zimene muli nazo.—Afilipi 4:12, 13; 1 Timoteyo 6:8; Aheberi 13:5.

MFUNDO YOTHANDIZA

Pewani zinthu monga kutchova njuga, kusuta fodya ndiponso kumwa mowa mwauchidakwa. Ngati ena mwa abale anu amachita zinthu ngati zimenezi, inuyo asonyezeni chitsanzo chabwino mwa kupewa zinthu zimenezi.

ZOTI NDICHITE

Zinthu zofunika kwambiri zimene ndili nazo ndi izi: ․․․․․

Ndingathandize ena ndi zinthu zimenezi mwa kuchita izi: ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pankhaniyi ndi izi: ․․․․․

MUKUGANIZA BWANJI?

● N’chifukwa chiyani tinganene kuti kusauka kumasiyanasiyana malinga ndi dera limene munthu akukhala?

● N’chifukwa chiyani tinganene kuti n’kupanda nzeru kuyesa kuzemba mavuto pogwiritsa ntchito zinthu monga mankhwala osokoneza bongo ndiponso kumwa mowa?

● Kodi ndi zinthu ziti zimene mungachite kuti mupirire umphawi?

[Mawu Otsindika patsamba 168]

“Ngakhale kuti ndinkaona ngati umphawi sungandichoke, ndinazindikira kuti kulowa m’gulu la zigawenga kapena kuyamba kuba sikungathetse mavuto anga. Panopa, achinyamata ambiri amsinkhu wanga amene ankachita zinthu zimenezi amangoyendayenda chifukwa chosowa zochita, ndi zidakwa zotheratu, amagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo ndipo ena ali m’ndende.”—Anatero George

[Bokosi/Zithunzi patsamba 164]

Zimene Munalemba

Kodi Ndipite ku Dziko Lina?

Achinyamata ena amafuna kupita ku dziko lina kuti akapeze ndalama zoti azigwiritsa ntchito kapena kuthandizira mabanja awo. Ena amapita ku dziko lina n’cholinga choti akaphunzire chinenero cha dzikolo, akapitirize maphunziro kapena pofuna kuthawa mavuto kunyumba kwawo. Akhristu ena achinyamata amapita ku mayiko ena amene kukufunika olalikira Ufumu ambiri. Mufunikira kuganizira mofatsa musanapite ku dziko lina chifukwa imeneyi ndi nkhani yaikulu. Motero ngati mukufuna kupita ku dziko lina, werengani ndi kuganizira mofatsa malemba ali m’munsiwa. Dzifunseni mafunso amenewa ndi kulemba mayankho ake papepala lina. Ndipo kenako pempherani ndi kusankha chochita pankhaniyi.

◻ Kodi ndikufunika kutsatira malamulo ati a boma?—Aroma 13:1.

◻ Kuti ndipite kunja, kodi pangafunike ndalama zingati?—Luka 14:28.

◻ Kodi panopa ndikuchita chiyani chimene chikusonyeza kuti ndikatha kudzisamalira ndikapita ku dziko linalo?—Miyambo 13:4.

◻ Kodi anthu achikulire amene akhalapo kumayiko ena andipatsa malangizo otani?—Miyambo 1:5.

◻ Kodi makolo anga akuiona motani nkhaniyi?—Miyambo 23:22.

◻ Kodi cholinga changa chopitira ku dziko lina n’chiyani?—Agalatiya 6:7, 8.

◻ Ngati ndizikakhala ndi anthu ena, kodi azikandilimbikitsa kuchita zinthu zauzimu?—Miyambo 13:20.

◻ Kodi ndingakakumane ndi zinthu zotani zimene zingakawononge makhalidwe anga, thanzi langa ndiponso moyo wanga wauzimu?—Miyambo 5:3, 4; 27:12; 1 Timoteyo 6:9, 10.

◻ Kodi ndi zinthu ziti zimene ndikuganiza kuti ndikapeza ndikapita ku dziko lina?—Miyambo 14:15.

[Chithunzi patsamba 167]

Malangizo a m’Baibulo angakuthandizeni kuti mumasuke ku vuto lodziona ngati munthu wachabechabe