Lemba la Chaka cha 2015
“Yamikani Yehova, chifukwa iye ndi wabwino.” —Salimo 106:1
Yehova anapulumutsa Aisiraeli pa Nyanja Yofiira pamene Farao ndi asilikali ake ankawathamangira. Apa Aisiraeliwo anali ndi zifukwa zambiri zowachititsa kumuyamikira. Ifenso tiyenera kuyamikira Yehova. N’zoona kuti timakumana ndi mavuto komanso timakhumudwa. Koma izi zikachitika, kukumbukira madalitso amene tili nawo kukhoza kutilimbikitsa.
Sal. 46:1) Kukumbukira zimenezi kungatithandize kuti tipirire mavuto oopsa kwambiri. Choncho m’chaka chonse chikubwerachi, tiyeni tiziganizira madalitso athu ‘n’kumayamika Yehova chifukwa iye ndi wabwino ndipo kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.’—Sal. 106:1.
Posachedwapa Yehova adzatidalitsa kwambiri. Iye adzatimasula n’kuthetsa mavuto athu onse. Kaya tikumane ndi vuto lotani, tiyenera kudziwa kuti Yehova sadzatisiya. Iye amatipatsa zinthu zonse zotithandiza kuti tizimutumikira mokhulupirika. Nthawi zonse amakhala “pothawira pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezeka mosavuta pa nthawi ya masautso.” (