MUTU 8
Mulungu Amakonda Anthu Oyera
“Kwa munthu wokhalabe woyera, mudzadzisonyeza kuti ndinu woyera.”—SALIMO 18:26.
1-3. (a) Kodi n’chifukwa chiyani mayi amaonetsetsa kuti mwana wawo akuoneka bwino? (b) N’chifukwa chiyani Yehova amafuna kuti anthu amene amamulambira azikhala oyera, nanga n’chiyani chimatilimbikitsa kukhala oyera?
MAYI akamakonzekeretsa mwana wawo kuti apite naye kokayenda, amaonetsetsa kuti amusambitsa ndiponso wavala zovala zoyera. Mayiwo amadziwa kuti ukhondo ndi wofunika kwambiri pa thanzi la mwanayo. Amadziwanso kuti kaonekedwe ka mwana wawo kamanena zambiri za iwo.
2 Yehova, Atate wathu wakumwamba, amafuna kuti atumiki ake akhale aukhondo komanso oyera. Mawu ake amanena kuti: “Kwa munthu wokhalabe woyera, mudzadzisonyeza kuti ndinu woyera.” * (Salimo 18:26) Yehova amatikonda ndipo amadziwa kuti kukhala oyera kumatipindulitsa. Iye amayembekezeranso kuti ife monga Mboni zake tizisonyeza chithunzi chabwino cha mmene Mulunguyo alili. Zoonadi, tikamaoneka bwino komanso tikamasonyeza makhalidwe abwino timapewa kunyozetsa Yehova ndiponso dzina lake loyera, ndipo anthu ena amamulemekeza.—Ezekieli 36:22; werengani 1 Petulo 2:12.
3 Kudziwa kuti Mulungu amakonda anthu oyera kumatilimbikitsa kukhala oyera. Chifukwa chakuti timakonda Mulungu, timafuna kuti zimene timachita pa moyo wathu zizipangitsa anthu kumulemekeza. Timafunanso kuti iye apitirizebe kutikonda. Tsopano tiyeni tikambirane mafunso awa: Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kukhala oyera? Kodi kukhala oyera kumatanthauza chiyani? Kodi tingatani kuti tikhale oyera? Kukambirana zimenezi kungatithandize kudziwa ngati pali mbali zina zomwe tingafunike kusintha.
N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUKHALA OYERA?
4, 5. (a) Kodi chifukwa chenicheni chimene tiyenera kukhalira oyera n’chiyani? (b) Kodi zimene Yehova analenga zimasonyeza bwanji kuti ndi woyera?
4 Njira imodzi imene timaphunzirira kwa Yehova ndi kutsatira chitsanzo chake. N’chifukwa chake Mawu ake amatilimbikitsa kuti: “Muzitsanzira Mulungu.” (Aefeso 5:1) Kodi chifukwa chenicheni chimene tiyenera kukhalira oyera n’chiyani? Chifukwa chakuti Yehova, Mulungu amene timalambira, ndi woyera.—Werengani Levitiko 11:44, 45.
5 Mofanana ndi mmene timadziwira makhalidwe ambiri a Yehova tikaona chilengedwe, timadziwanso kuti iye ndi woyera tikaona zimene analenga. (Aroma 1:20) Dzikoli linakonzedwa kuti likhale malo oyera oti anthu azikhalamo. Yehova anakonza zoti chilengedwe chizitha kuyeretsa mpweya ndi madzi. Choncho, dziko lapansi lingathe kudziyeretsa lokha. N’zoonekeratu kuti Yehova amene “analenga dziko lapansi” amaona kuti kukhala oyera ndi nkhani yofunika kwambiri. (Yeremiya 10:12) Ifenso tiyenera kuona kuti kukhala oyera n’kofunika kwambiri.
6, 7. Kodi Chilamulo cha Mose chinatsindika bwanji kufunika koti olambira a Yehova azikhala oyera?
6 Chifukwa chinanso chimene tiyenera kukhalira oyera Levitiko 16:4, 23, 24) Ansembe amene ankatsogolera patsikuli ankafunika kusamba m’manja ndi m’mapazi asanapereke nsembe kwa Yehova. (Ekisodo 30:17-21; 2 Mbiri 4:6) Chilamulochi chinatchula zinthu zina zoposa 70 zimene zinkapangitsa munthu kukhala wodetsedwa ndiponso wosayenera kuchita zinthu zina zofunika pa kulambira. Kale ku Isiraeli, munthu akakhala wodetsedwa sankaloledwa kuchita chilichonse chokhudza kulambira, ndipo nthawi zina akapanda kutsatira malangizo amenewa, ankafunika kuphedwa. (Levitiko 15:31) Munthu aliyense wokana kutsatira zimene ankafunika kuchita kuti ayeretsedwe, zomwe zinkaphatikizapo kusamba ndi kuchapa zovala, ‘ankaphedwa kuti asakhalenso pakati pa mpingowo.’—Numeri 19:17-20.
n’chakuti Yehova, yemwe ndi Wolamulira Wamkulu Koposa, amafuna kuti olambira ake azikhala oyera. Chilamulo chimene Yehova anapatsa Aisiraeli chimasonyeza kuti kukhala oyera n’kofunika kwambiri pa kulambira. Chilamulocho chinanena kuti pa tsiku lochita Mwambo Wophimba Machimo, mkulu wa ansembe ankafunika kusamba kawiri, osati kamodzi kokha. (7 Ngakhale kuti masiku ano sititsatira Chilamulo cha Mose, chilamulochi chimatithandiza kudziwa maganizo a Mulungu pa nkhani zosiyanasiyana. Chilamulo chinatsindika kuti anthu olambira Mulungu ankafunika kukhala oyera. Yehova sanasinthe. (Malaki 3:6) Kuti kulambira kwathu kukhale kovomerezeka, kuyenera kukhala “koyera ndi kosaipitsidwa.” (Yakobo 1:27) Choncho, tiyenera kudziwa zimene Mulungu amafuna kuti tizichita pa nkhani imeneyi.
KODI KUKHALA OYERA PAMASO PA MULUNGU KUMATANTHAUZA CHIYANI?
8. Kodi Yehova amafuna kuti tikhale oyera m’mbali ziti?
8 M’Baibulo, mawu akuti “woyera” amatanthauza zambiri osati ukhondo wokha. Kukhala woyera kwa Mulungu kumakhudza mbali zonse za moyo wathu. Yehova amafuna kuti tizikhala oyera m’mbali 4 zofunika kwambiri izi: Mwauzimu, m’makhalidwe, m’maganizo ndiponso mwakuthupi. Tiyeni tikambirane mfundo zimenezi, iliyonse payokha.
9, 10. Kodi kukhala oyera mwauzimu kumatanthauza chiyani, nanga Akhristu oona amapewa chiyani?
Yesaya 52:11) Chifukwa chachikulu chimene Aisiraeli anabwererera kwawo chinali chakuti akabwezeretse kulambira koona. Kulambira kumeneku kunayenera kukhala kosadetsedwa, kosaphatikiza ziphunzitso ndi miyambo iliyonse yonyozetsa Mulungu ya chipembedzo cha ku Babulo.
9 Kukhala oyera mwauzimu. Kunena mwachidule, kukhala oyera mwauzimu kumatanthauza kusaphatikiza kulambira koona ndi konyenga. Aisiraeli atachoka ku Babulo kubwerera ku Yerusalemu, anafunika kutsatira malangizo a Mulungu awa: “Tulukani mmenemo! Musakhudze chinthu chilichonse chodetsedwa. . . . Khalani oyera.” (10 Masiku ano, ife Akhristu oona tiyenera kusamala kuti tisadetsedwe ndi kulambira konyenga. (Werengani 1 Akorinto 10:21.) M’pofunika kwambiri kusamala pa nkhani imeneyi chifukwa kulambira konyenga kuli paliponse. M’mayiko ambiri, miyambo ndi zochitika zambiri n’zokhudzana ndi ziphunzitso za chipembedzo chonyenga, monga chakuti munthu ali ndi chinthu chinachake chimene sichifa munthuyo akamwalira. (Mlaliki 9:5, 6, 10) Akhristu oona amapewa miyambo ndi zikhulupiriro za chipembedzo chonyenga. * Sitingagonje, ena akamatikakamiza kuti tisatsatire mfundo za m’Baibulo zokhudza kulambira koyera.—Machitidwe 5:29.
11. Kodi kukhala ndi makhalidwe abwino kumaphatikizapo chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani n’kofunika kukhala ndi makhalidwe amenewa?
11 Kukhala ndi makhalidwe abwino. Kuti tikhalebe ndi makhalidwe abwino tifunika kupewa chiwerewere cha mtundu uliwonse. (Werengani Aefeso 5:5.) Kukhala ndi makhalidwe abwino n’kofunika kwambiri. Monga tionere m’mutu wotsatira wa bukuli, kuti Mulungu apitirizebe kutikonda, tifunika ‘kuthawa dama.’ Anthu adama “sadzalowa mu ufumu wa Mulungu” ngati salapa. (1 Akorinto 6:9, 10, 18) Mulungu amaona anthu amenewa kuti ali m’gulu la anthu “odetsedwa amenenso amachita zinthu zonyansa.” Ngati sasintha ndi kukhala ndi makhali dwe abwino, “gawo lawo lidzakhala . . . imfa yachiwiri.”—Chivumbulutso 21:8.
12, 13. Kodi pali kugwirizana kotani pakati pa maganizo ndi zochita, ndipo tingatani kuti tikhalebe ndi maganizo abwino?
12 Kukhala ndi maganizo abwino. Timachita zinthu zimene timaganiza. Ngati timalola zinthu zoipa kukhazikika m’maganizo ndi mumtima mwathu, m’kupita kwa nthawi tidzachita zinthu zoipa. (Mateyu 5:28; 15:18-20) Koma ngati timaganizira zinthu zabwino ndi zoyera, zidzatithandiza kukhalabe ndi makhalidwe abwino. (Werengani Afilipi 4:8.) Kodi tingatani kuti tikhalebe ndi maganizo abwino? Chinthu chimodzi chimene tiyenera kuchita ndi kupewa zosangalatsa zonse zimene zingadetse maganizo athu. * Kuwonjezera pamenepo, tingakhale ndi maganizo abwino ngati timaphunzira Mawu a Mulungu nthawi zonse.—Salimo 19:8, 9.
13 Kuti Mulungu apitirize kutikonda, m’pofunika kwambiri kuti tikhale oyera mwauzimu, tikhale ndi makhalidwe abwino ndiponso maganizo abwino. Mbali zimenezi zafotokozedwa bwino kwambiri m’mitu ina m’bukuli. Koma panopo tiyeni tikambirane mbali yomalizira pa nkhani yokhala oyera, yomwe ndi ukhondo.
KODI TINGATANI KUTI TIKHALE AUKHONDO?
14. Kodi n’chifukwa chiyani nkhani ya ukhondo si nkhani yoyendera zimene munthu wakonda?
14 Kuti munthu akhale waukhondo afunika kusamalira thupi lake, malo okhala ndiponso katundu wake. Kodi nkhani ya ukhondoyi, ndi nkhani yoyendera zimene munthu wakonda? Ayi, si mmene olambira Yehova amaonera nkhani imeneyi. Monga taonera kale, Yehova amafuna kuti tizikhala aukhondo chifukwa ukhondowo ndi wabwino kwa ife, komanso tikakhala aukhondo timapangitsa ena kulemekeza Mulungu. Taganizirani chitsanzo chili kumayambiriro kwa nkhani ino. Mukaona mwana amene nthawi zonse amakhala wauve komanso wosaoneka bwino mumadabwa kuti, ‘Kodi makolo ake ndi otani?’ Sitikufuna 2 Akorinto 6:3, 4) Koma kodi tingatani kuti tikhale aukhondo?
kuti maonekedwe athu kapena zochita zathu zizipangitsa anthu kunyoza Atate wathu wakumwamba kapenanso kulepheretsa anthu kumva uthenga umene timalalikira. Mawu a Mulungu amati: “Sitikuchita chilichonse chokhumudwitsa, kuti utumiki wathu usapezedwe chifukwa. Koma tikusonyeza mwa njira ina iliyonse kuti ndife atumiki a Mulungu.” (15, 16. Kodi ukhondo umaphatikizapo chiyani, nanga zovala zathu zizioneka bwanji?
15 Kukhala aukhondo komanso ooneka bwino. Ngakhale kuti zikhalidwe ndiponso kupeza n’kosiyana kwambiri m’mayiko osiyanasiyana, n’zotheka kupeza sopo ndiponso madzi oti tizisamba nthawi zonse ndi kuonetsetsa kuti ifeyo ndi ana athu ndife aukhondo. Ukhondo umaphatikizapo kusamba m’manja ndi sopo tisanadye kapena tisanagwire chakudya, tikamachokera kuchimbudzi ndiponso tikasintha mwana thewera. Kusamba m’manja ndi sopo kumatiteteza ku matenda komanso imfa Deuteronomo 23:12, 13.
zobwera chifukwa cha matendawo. Kuchita zimenezi kumathandizanso kuti tizilombo toyambitsa matenda tisafalikire, ndipo zimenezi zimathandiza kupewa matenda otsegula m’mimba. Anthu amene pakhomo pawo palibe chimbudzi, angathe kukwirira zonyansazo, monga mmene ankachitira Aisiraeli kale.—16 Tiyeneranso kuchapa zovala zathu nthawi zonse kuti zikhale zaukhondo ndi zooneka bwino. Zovala za Mkhristu sizichita kufunika kukhala zodula kapena zamakono, koma ziyenera kukhala zaukhondo, zoyera ndiponso zopatsa ulemu. (Werengani 1 Timoteyo 2:9, 10.) Kaya timakhala kuti, tiyenera kuonetsetsa kuti maonekedwe athu ‘akukometsera chiphunzitso cha Mpulumutsi wathu Mulungu.’—Tito 2:10.
17. Kodi n’chifukwa chiyani nyumba, malo ndi katundu wathu ziyenera kukhala zaukhondo ndi zooneka bwino?
17 Nyumba, malo ndi katundu wathu. Ngakhale zitakhala kuti nyumba zathu si zapamwamba, tiyenera kuzisamala bwino mmene tingathere kuti zizioneka zaukhondo. Tiyenera kuchitanso zimenezi ndi katundu wathu, monga galimoto, njinga ndi zikwama zathu zonyamulira mabuku, makamaka ngati timazigwiritsa ntchito popita kumisonkhano komanso mu utumiki wakumunda. Tiyenera kukumbukira kuti nyumba, malo ndi katundu wathu zikakhala zaukhondo, anthu amalemekeza Mulungu amene timalambira. Tisaiwalenso kuti timaphunzitsa anthu kuti Yehova ndi Mulungu woyera, ndiponso kuti ‘adzawononga amene akuwononga dziko lapansi,’ komanso kuti Ufumu wake posachedwapa udzasintha dzikoli kukhala paradaiso. (Chivumbulutso 11:18; Luka 23:43) Choncho, nyumba zathu ndi katundu wathu zizisonyeza anthu ena kuti ndife anthu oyera, amene akuyembekezera kudzakhala m’dziko latsopano lomwe lidzakhalanso laukhondo.
18. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza Mulungu?
18 Malo athu olambirira. Timakonda Yehova, ndipo timamulemekeza posamalira Nyumba ya Ufumu ya m’dera lathu, chifukwa ndi malo amene timalambirira Mulungu woona. Anthu atsopano akabwera ku Nyumba ya Ufumu, timafuna kuti azikhala ndi chithunzi chabwino cha malo athu osonkhanira. 2 Mbiri 34:10) Tingachitenso zomwezi posamalira Malo a Misonkhano kapena malo alionse amene timachitirapo misonkhano ikuluikulu.
Kuti Nyumba ya Ufumu izionekabe bwino, tiyenera kuisamalira ndi kukonza malo onse owonongeka nthawi zonse. Timasonyeza kuti timalemekeza Nyumba ya Ufumu tikamachita zonse zimene tingathe kuti nyumbayo ikhalebe yaukhondo. Ndi mwayi wathu kugwiritsa ntchito nthawi yathu posamalira ndi ‘kukonza’ malo athu olambirira. (TIZIPEWA MAKHALIDWE ONSE ODETSA
19. Kuti tikhalebe oyera, kodi tiyenera kupewa chiyani, nanga Baibulo lingatithandize bwanji pa nkhani imeneyi?
19 Kuti tikhalebe anthu oyera, tiyenera kupewa makhalidwe onse odetsa monga kusuta, kuledzera ndiponso kugwiritsa ntchito mankhwala alionse osokoneza bongo. Baibulo silitchula makhalidwe onse odetsa ndi onyansa amene afala masiku ano omwe tiyenera kupewa, koma lili ndi mfundo zimene zimatithandiza kudziwa mmene Yehova amaonera makhalidwe amenewa. Popeza timadziwa mmene Yehova amaonera zinthu, timayesetsa kuchita zimene iye amavomereza chifukwa timamukonda. Tiyeni tione mfundo 5 za m’Malemba zokhudza nkhani imeneyi.
20, 21. Kodi Yehova amafuna kuti tipewe makhalidwe otani, ndipo kodi chifukwa chachikulu chimene tiyenera kupewera zimenezi n’chiti?
20 “Popeza talonjezedwa zinthu zimenezi, tiyeni tidziyeretse ndipo tichotse chinthu chilichonse choipitsa thupi kapena mzimu, kwinaku tikukwaniritsa kukhala oyera poopa Mulungu.” (2 Akorinto 7:1) Yehova amafuna kuti tisamachite zinthu zimene zimaipitsa thupi ndi mzimu wathu, kapena kuti maganizo athu. Choncho, tiyenera kupewa zizolowezi zoipa zimene zingawononge thanzi ndi maganizo athu.
21 Baibulo likufotokoza chifukwa chachikulu chimene tiyenera ‘kudziyeretsera ndi kuchotsa chinthu chilichonse chotiipitsa.’ Onani kuti lemba la 2 Akorinto 7:1 limayamba ndi mawu akuti: “Popeza talonjezedwa zinthu zimenezi.” Kodi talonjezedwa chiyani? Monga mmene mavesi a m’mbuyo mwa lembali akunenera, Yehova akulonjeza kuti: “Ndidzakulandirani. Ndidzakhala atate wanu.” (2 Akorinto 6:17, 18) Tangoganizani, Yehova akutilonjeza kuti adzatiteteza ndi kutikonda monga mmene bambo amakondera mwana wake. Kuti mudzaone malonjezo amenewa akukwaniritsidwa, muyenera kupewa zoipitsa ‘thupi ndi mzimu.’ Kunena zoona kungakhale kupusa kulola makhalidwe onyansa kutilepheretsa kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova.
22-25. Kodi ndi mfundo za m’Malemba ziti zimene zingatithandize kupewa makhalidwe oipa?
22 “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.” (Mateyu 22:37) Yesu ananena kuti lamulo limeneli ndi limene lili lalikulu pa onse. (Mateyu 22:38) Tiyenera kukonda Yehova m’njira imeneyi. Kuti timukonde Yehova ndi mtima wathu wonse, moyo wathu wonse, ndiponso ndi maganizo athu onse, tiyenera kupewa makhalidwe amene angawononge moyo wathu kapena amene angasokoneze luso lathu lotha kuganiza bwino limene Mulungu anatipatsa.
23 “[Yehova] amapatsa anthu onse moyo, mpweya, ndi zinthu zonse.” (Machitidwe 17:24, 25) Moyo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu. Timakonda amene anatipatsa moyo, choncho tizisonyeza kuti timalemekeza mphatso imeneyi. Komanso, timapewa makhalidwe alionse amene angawononge thanzi lathu, chifukwa timadziwa kuti kuchita zimenezi n’kusalemekeza mphatso imeneyi.—Salimo 36:9.
24 “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.” (Mateyu 22:39) Nthawi zambiri makhalidwe oipa amawononga thanzi la anthu amene amachita makhalidwewo ndiponso anthu amene amakhala nawo pafupi. Mwachitsanzo, utsi umene munthu amene akusuta amatulutsa, umawononga thanzi la anthu amene sasuta. Munthu amene amachita zinthu zoika moyo wa anzake pa ngozi, amaswa lamulo la Mulungu lakuti tizikonda anzathu. Komanso akamachita zimenezi, ndiye kuti amanama akamanena kuti amakonda Mulungu.—1 Yohane 4:20, 21.
25 ‘Gonjerani ndi kumvera maboma ndiponso olamulira.’ (Tito 3:1) M’mayiko ambiri, malamulo amaletsa kusunga kapena kugwiritsa ntchito mankhwala ena. Ife Akhristu oona, sitisunga kapena kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo oletsedwa ndi boma.—Aroma 13:1.
26. (a) Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti Mulungu apitirizebe kutikonda? (b) Kodi n’chifukwa chiyani kukhala oyera pamaso pa Mulungu n’kwabwino kwambiri?
26 Kuti Mulungu apitirize kutikonda, tiyenera kukhala oyera m’mbali zonse za moyo wathu. Kusiya ndi kupewa makhalidwe odetsa n’kovuta koma n’zotheka kuchita zimenezi. * Kunena zoona, kutsatira malangizo a Yehova n’kwabwino kwambiri, chifukwa Yehova nthawi zonse amatiphunzitsa zinthu zotipindulitsa. (Werengani Yesaya 48:17.) Koma chofunika kwambiri n’chakuti tikamakhala oyera timasangalala chifukwa timasonyeza kuti Mulungu amene timamukonda ndi woyera. Ndipo kuchita zimenezi kumatithandiza kuti iye apitirize kutikonda.
^ ndime 2 Mawu amene amasuliridwa kuti “woyera” amanena za kukhala aukhondo, kukhala ndi makhalidwe abwino komanso kukhala osadetsedwa mwauzimu.
^ ndime 10 Onani Mutu 13 m’bukuli, kuti mudziwe miyambo ndi zikondwerero zimene Akhristu oona ayenera kupewa.
^ ndime 12 Mutu 6 m’bukuli, ukufotokoza mmene mungasankhire zosangalatsa zabwino.
^ ndime 26 Onaninso mabokosi otsatirawa: “ Kodi Ndimayesetsa Kuchita Zabwino?” ndiponso “ Zinthu Zonse N’zotheka ndi Mulungu.”
^ ndime 67 Tasintha dzinali.