Kodi Inuyo Mumakhulupirira Zotani?
Anthu ena achipembedzo amakhulupirira kuti dziko lapansi ndiponso zinthu zonse zapadzikoli zinalengedwa m’masiku 6 enieni a maola 24, zaka masauzande ochepa zapitazo. Pomwe anthu ena amanena kuti kulibe Mulungu, kuti Baibulo ndi buku la nthano chabe komanso kuti zamoyo zonse zinangokhalapo zokha popanda kulengedwa ndi winawake.
Koma anthu ambiri sakudziwa kuti zoona zake ndi ziti. Popeza mukuwerenga kabukuka, mwina inunso muli m’gulu la anthu amene sakudziwa zoona zake pankhaniyi. N’kutheka kuti mumakhulupirira Mulungu ndiponso kulemekeza Baibulo koma mumalemekezanso zimene asayansi amakhulupirira zoti zamoyo sizinachite kulengedwa. Ngati muli ndi ana, mungafune kudziwa mmene mungawayankhire atakufunsani ngati zamoyo zinakhalapo zokha kapena kulengedwa.
Kodi Cholinga cha Kabukuka N’chiyani?
Cholinga chake si kunyoza anthu azipembedzo zina kapena amene sakhulupirira kuti kuli Mulungu. Koma tikufuna kuti kabukuka kakulimbikitseni kuti muzifufuza bwinobwino zimene mumakhulupirira. Kakufotokoza zimene Baibulo limanena pa nkhani ya kulengedwa kwa zinthu ndipo mwina mfundo zake simunaziganizirepo. Kakusonyezanso kuti zimene timakhulupirira pa nkhaniyi zimakhudza kwambiri moyo wathu.
Kodi muyenera kukhulupirira anthu amene amanena kuti kulibe Mulungu komanso kuti Baibulo silinena zoona? Kapena muyenera kufufuza zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi? Kodi mfundo zomveka ndi ziti, za m’Baibulo kapena za anthu amene amanena kuti zinthu zinangokhalapo zokha? (Aheberi 11:1) Mungachite bwino kwambiri kufufuza zoona zake.