Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

FUNSO 5

Kodi Ndi Nzeru Kukhulupirira Baibulo?

Kodi Ndi Nzeru Kukhulupirira Baibulo?

Kodi munauzidwapo zinthu zolakwika zokhudza munthu wina? Mwina munamva anthu ena akumunena kapena kufotokoza zimene munthuyo ananena. Mwina munaganiza kuti simungagwirizane naye koma kenako mutamudziwa munazindikira kuti anali wosiyana ndi zimene anthuwo ananena. Izi n’zimene zachitikira anthu ambiri pa nkhani ya Baibulo.

Anthu ambiri ophunzira sakhulupirira Baibulo. Kodi mukudziwa chifukwa chake? Anthu ambiri amasonyeza kuti Baibulo ndi lokhwimitsa zinthu, siligwirizana ndi sayansi komanso kuti silinena zoona. Koma kodi n’kutheka kuti anthu safotokoza zolondola zokhudza Baibulo?

Kodi mwina powerenga kabukuka munadabwa kuona kuti Baibulo limanena zinthu zolondola pa nkhani za sayansi? Ngati ndi choncho si inu nokha. Anthu ambiri amadabwanso kuona kuti Baibulo siliphunzitsa zinthu zina zimene anthu ambiri a zipembedzo amanena kuti zili m’Baibulo. Mwachitsanzo, anthu ena amanena kuti Baibulo limati Mulungu analenga zinthu zonse m’masiku 6 a maola 24. Koma Baibulo silinena zimenezi ndipo silinena chilichonse chotsutsana ndi zimene asayansi amanena pa nkhani ya nthawi imene dzikoli komanso zinthu zina zakhalapo. *

Zimene Baibulo limafotokoza mwachidule pa nkhani ya mmene Mulungu analengera zamoyo padzikoli sizitsutsananso ndi zambiri zimene asayansi amanena. Koma Baibulo limanena kuti Mulungu analenga zamoyo zonse komanso anazilenga “monga mwa mtundu wake.” (Gen. 1:11, 21, 24) Mwina zimenezi zikutsutsana ndi maganizo a asayansi ena, koma osati ndi mfundo za sayansi zimene zili ndi umboni wake. Mbiri ya sayansi imasonyeza kuti maganizo amene asayansi angakhale nawo angasinthe koma mfundo zimene zili ndi umboni wake sizingasinthe.

Anthu ambiri safuna kuphunzira Baibulo chifukwa choti amadana ndi zimene anthu ena a zipembedzo amachita. Iwo amaona anthu a m’zipembedzo akuchita zinthu zachinyengo komanso akulimbikitsa nkhondo. Koma kodi ndi bwino kudana ndi Baibulo chifukwa cha makhalidwe oipa a anthu amene amanena kuti amalitsatira? Asayansi ambiri adandaulapo kwambiri chifukwa cha mmene anthu ena ankhanza amagwiritsa ntchito mfundo yoti anthu anasintha kuchokera ku anyani pofuna kusonyeza kuti anthu a mitundu ina ndi achabechabe. Kodi zingakhale bwino kunena kuti mfundoyo si yolondola chifukwa cha zimene anthu ankhanzawo amachita? Ayi. Koma ndi nzeru kufufuza bwinobwino mfundoyi n’kuona ngati imagwirizana ndi umboni umene ulipo.

Tikukulimbikitsani kuti muchitenso zomwezo ndi Baibulo. Mukhoza kudabwa kuti mfundo zimene Baibulo limaphunzitsa ndi zosiyana kwambiri ndi zimene zipembedzo zambiri zimaphunzitsa. Mwachitsanzo, Baibulo sililimbikitsa nkhondo, koma limaphunzitsa kuti atumiki a Mulungu ayenera kupewa nkhondo komanso chidani chimene chimachititsa kuti anthu azimenyana. (Yes. 2:2-4; Mat. 5:43, 44; 26:52) Baibulo sililimbikitsa mtima wosalolera komanso kukhulupirira zinthu popanda umboni. M’malomwake limaphunzitsa kuti munthu sangakhale ndi chikhulupiriro chenicheni popanda kuona umboni wake komanso ayenera kugwiritsa ntchito luso lake loganiza kuti atumikire Mulungu. (Aroma 12:1; Aheb. 11:1) Baibulo sililimbikitsa anthu kuti asamafufuze zinthu koma limawalimbikitsa kuti azifufuza kwambiri kuti apeze mayankho a mafunso ovuta kwambiri amene anthu amakonda kufunsa.

Mwachitsanzo, kodi munayamba mwadzifunsapo kuti, ‘Ngati kuli Mulungu, kodi n’chifukwa chiyani amalola kuti tizivutika?’ Baibulo limayankha bwino funso limeneli komanso mafunso ena ambiri. * Tikukulimbikitsani kuti musasiye kufufuza mayankho olondola a mafunso anu mpaka mutawapeza. M’Baibulo mukhoza kupeza mayankho ochititsa chidwi, osangalatsa, omveka bwino komanso okhala ndi umboni wake. Ndipotu sizinachitike mwangozi kuti Baibulo likhalepo n’kumayankha mafunso athu.

^ ndime 5 Kuti mudziwe zambiri, onani kabuku kakuti Kodi Zamoyo Zinachita Kulengedwa? kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.