Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Maphunziro Othandiza kwa Moyo Wonse

Maphunziro Othandiza kwa Moyo Wonse

Maphunziro Othandiza kwa Moyo Wonse

“Baibulo [ndi] buku lamalangizo abwino kwambiri pamoyo wamunthu.”—Anatero Thomas Tiplady, m’chaka cha 1924.

SIKUKOKOMEZA kunena kuti maphunziro a Baibulo angasinthe moyo. Lachititsa anthu osungulumwa ndi otaya mtima kupeza chimwemwe komanso chiyembekezo. Kholo losakwatira la ku Namibia linalembera kalata nthambi ya Mboni za Yehova ku South Africa kuti:

“Ndili ndi zaka 29, ndipo ndinaŵerenga buku lakuti Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza m’masiku aŵiri okha. Linandigwira mtima kwambiri chifukwa ndine wosungulumwa kwabasi. Mwamuna amene anali chibwenzi changa anamwalira pangozi yagalimoto ndipo anandisiya ndi ana aŵiri. Tikuvutika kwambiri. Nthaŵi zina ndinkaganiza kuti kuli bwino ndiphe anawo kenako ndidziphe ndekha. Koma n’tangopeza buku limeneli, ndinasintha maganizo. Chonde ndithandizeni pochita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.”

Baibulo ndi buku lamalangizo limene lingathandize anthu kuchita bwino m’mbali iliyonse m’moyo. Lingawathandize kukhala bwino ndi mabanja awo, ndi ogwira nawo ntchito, ndiponso anthu ena onse. (Salmo 19:7; 2 Timoteo 3:16) Limapereka malangizo othandiza a mmene tingachitire chabwino ndi kupeŵa kuchita choipa. Ndi buku limene limakamba zochitika zenizeni m’moyo. Mukamaliŵerenga mungaone kuti lili ndi nkhani za anthu enieni zokhazokha. Mudzaona zimene zinapangitsa moyo wa anthu ena kukhala wosangalatsa ndi wopindulitsa, ndipo wa ena kukhala wopweteka ndi womvetsa chisoni. Mudzaona bwinobwino zinthu zimene zili zopindulitsa ndi zimene zili zachabe.

Maphunziro Othandiza kwa Moyo Wonse Tsopano Lino

Baibulo limagogomezera kufunika kwa nzeru zenizeni. Limati: “Nzeru ipambana, tatenga nzeru.” (Miyambo 4:7) Limanenanso kuti anthu nthaŵi zambiri amasoŵa nzeru, choncho limalimbikitsa kuti: “Wina wa inu ikam’soŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja.”—Yakobo 1:5.

Kodi Mlengi wathu, Yehova Mulungu, amapatsa motani nzeru modzala manja? Amapereka mwa Mawu ake, Baibulo, limene amatilimbikitsa kuti tiziŵerenga. Mulungu akupempha kuti: “Mwananga, ukalandira mawu anga, ndi kusunga malamulo anga; kutcherera makutu ako kunzeru . . . udzazindikira kuopa Yehova ndi kum’dziwadi Mulungu. Pakuti Yehova apatsa nzeru.” (Miyambo 2:1, 2, 5, 6) Tikagwiritsa ntchito uphungu wa m’Mawu a Mulungu n’kuona kuthandiza kwake, timazindikira kuti umasonyezadi nzeru ya Mulungu.

Mwachitsanzo, tiyeni tione, nkhani yothana ndi umphaŵi. Baibulo limalimbikitsa kugwira ntchito molimbika ndipo limaletsa mikhalidwe yowonongetsa zinthu. Choncho, mikhalidwe yoipa ngati kusuta fodya komanso uchidakwa n’zachidziŵikire kuti sizigwirizana ndi mfundo zachikhalidwe za m’Baibulo.—Miyambo 6:6-11; 10:26; 23:19-21; 2 Akorinto 7:1.

Nanga Baibulo limati chiyani pa nkhani ya mmene anthu amene timacheza nawo angasonkhezerere moyo wathu? Ilo limati: “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: koma mnzawo wa opusa adzaphwetekedwa.” (Miyambo 13:20) Kodi mwaona kuti chisonkhezero cha mabwenzi nthaŵi zambiri chapangitsa ana ndi akulu omwe—kuledzera, kumwa mankhwala osokoneza bongo, ndi kuchita chiwerewere? Inde, ngati timacheza ndi anthu amene amachita zinthu zimenezi, tidzafanana nawo, monga mmene Baibulo limanenera kuti: “Mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.”—1 Akorinto 15:33.

N’zoona kuti tonse timafuna kukhala achimwemwe. Koma kodi zimenezi zingatheke motani? Kodi mumadziŵa kuti Baibulo limati zimene zingatipatse chimwemwe si katundu koma malingaliro ndi mayanjano abwino, makamaka unansi wabwino ndi Mulungu? (1 Timoteo 6:6-10) Yesu Kristu, paulaliki wake wotchuka wa pa phiri, ananena kuti amene ali ndi chimwemwe chenicheni ndi amene ali “osauka mumzimu,” [‘ozindikira kusoŵa kwawo kwauzimu, NW] “akufatsa,” ‘akumva ludzu la chilungamo,’ “akuchitira chifundo,” “oyera mtima,” ndi “akuchita mtendere.”—Mateyu 5:1-9.

Mukalingalira mozama zimene Baibulo limaphunzitsa, mudzazindikira mmene zingathandizire kutsogolera moyo wathu. Pankhani yamalangizo, Baibulo ndi lapadera kwambiri. Uphungu wake n’ngopindulitsa nthaŵi zonse. Si nkhambakamwa chabe ayi ndipo sumativulaza. Nthaŵi zonse amene amagwiritsa ntchito malangizo a m’Baibulo amapindula.

Maphunziro Othandiza Kwa Moyo Wonse

Komanso, kuwonjezera pa kupindula pakalipano, Baibulo limanena za chiyembekezo chamoyo wa m’tsogolo. Limanena zakuti dziko lapansi lidzayeretsedwa ndi kusandutsidwa kukhala mudzi wokongola zedi wa anthu otumikira Mulungu. Onani mawu osangalatsa kwambiri otsatirawa onena za m’tsogolo akuti: “Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nawo, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.”—Chivumbulutso 21:3, 4; Miyambo 2:21, 22.

Tangoganizani: Sikudzakhalanso ana odwala, sikudzakhalanso kufa ndi njala, sikudzakhalanso matenda oopsa amene amafoola thupi, sikudzakhalanso kumva ululu! Kulira chifukwa chachisoni, kukhumudwa, ndiponso zovuta zidzatha, pakuti zinthu zimene zimapangitsa zimenezi zidzasinthidwa kapena kuchotsedwa. Pakuti anthu ochimwa mwadala adzakhala atawonongedwa ndi magulu ankhondo a angelo a Mulungu, mbala, zigaŵenga, akazitape, ndi onse amene amapangitsa moyo kukhala wovuta sadzakhalakonso. Anthu adzakhala ndi nyumba zawozawo ndi kusangalala nazo mopanda kuopa.—Yesaya 25:8, 9; 33:24; 65:17-25.

Kodi inuyo mukuona kuti zimenezi n’zosangalatsa? Kodi mungafune kuphunzira zambiri ponena za kugwiritsa ntchito mfundo zachikhalidwe za m’Baibulo kuti mupindule pakalipano ndiponso m’tsogolo? Ngati ndi choncho, chonde onanani ndi Mboni za Yehova, ndipo zidzasangala kukuikani inu ndi banja lanu m’ntchito yapadziko lonse ya “maphunziro othandiza kwa moyo wonse.”