Kodi Ndingatani ndi Mavuto Oleredwa ndi Makolo Osandibereka?
Achinyamata Akufunsa Kuti . . .
Kodi Ndingatani ndi Mavuto Oleredwa ndi Makolo Osandibereka?
“Makolo anga ondibereka sindiwadziŵa n’komwe, ndipo zimenezi zimandiwawa kwambiri.”—Anatero Barbara, yemwe ali ndi zaka 16.
“Sindidziŵa ngakhale pang’ono kumene ndinabadwira kapenanso makolo anga enieni. Nthaŵi zina usiku ndimangoganizira zimenezi.”—Anatero Matt, yemwe ali ndi zaka 9.
“Tikayambana ndi makolo amene akundisunga panopa, ndimangoti mwina akanakhala makolo anga enieni bwenzi akundimvetsa. Komatu ndimalakwa kwambiri kuganiza chonchi, ndipo sindinatchulepo ngakhale kamodzi kuti n’zimene ndimaganiza.”—Anatero Quintana, yemwe ali ndi zaka 16.
N’ZOONADI, munthu ukakhala mwana wa makolo amene sanakubereke umakumana ndi mavuto enaake ndithu. Achinyamata ochuluka amavutika ndi maganizo ofanana ndi amene afotokozedwa pamwambapa. Ambiri amaganiza zoti mwina afufuze kuti makolo awo owabereka ndani, kapenanso kuti mwina atamakhala nawo angamasangalale. Komatu si zokhazi zimene zimawavutitsa maganizo.
M’nkhani yotere yapitayo, tinafotokozamo maganizo ena olakwika amene achinyamata ena amene ali ndi makolo osawabereka amakhala nawo. * Kuthetsa maganizo olefula oterowo n’kofunika kwambiri kuti moyo muumve kukoma ngakhale muli m’manja mwa makolo osakuberekani. Nangano zovuta zina zimene zingabuke n’zotani, ndipo kodi mungatani kuti muthane nazo?
Ngati ndi Makolo Anga Enieni?
Mnyamata wina wa zaka 13, dzina lake Jake ananena kuti nthaŵi zambiri ankangoganizira kwambiri za amayi ake om’bereka. Zimenezo zinam’pangitsa kuti asamakhale bwinobwino
ndi makolo ake amene akum’sunga. Iye anati: “Ndikapsa mtima ndinkangoti, ‘Inutu siinu mayi anga enieni, ndiye simungandilange choncho ayi!’”Monga mwaoneramu, Jake ankafunika kumvetsa mfundo yoti: Akati amayi ako enieni amanena ndani? Ngati muli m’manja mwa makolo osakuberekani, mwina zimenezi n’zimene zikukuchitikirani, makamaka ngati mumaganiza kuti mwina makolo anu okuberekani akhoza kukhala nanu bwinopo kuposa makolo osakuberekeniwo. Koma kodi anthu akakhala anakubala anu ndiye kuti amakhaladi makolo enieni okukhazikani bwino?
Mayi om’lera Jake sanaone choncho. Jake anati: “Amayiwo ankandiyankha kuti, ‘mayi wako weniweni ndineyo kumene. Ngakhale kuti unali ndi amayi amene anakubereka, koma ineyo ndiye amayi ako enieni panopa.’” Anthu akatenga mwana winawake n’kumakhala naye panyumba pawo n’kuvomereza kuti am’patsa pogona, azim’dyetsa, ndiponso azim’lera, n’kumam’patsa zonse zofunika, ndiye kuti iwo amasandukadi makolo ake enieni. (1 Timoteo 5:8) N’kuthekanso kuti malamulo a dziko limene mukukhala amatero. Nanga Mulungu amaona bwanji zimenezi?
Taonani nkhani iyi ya Yesu Kristu imene mwina ndi nkhani yodziŵika kwambiri, ya kuleredwa ndi kholo losakubereka. Yesu sanali mwana woberekedwa ndi Yosefe, kalipentala uja, koma Yosefeyo analera mwanayo ngati wakewake. (Mateyu 1:24, 25) Pamene Yesu amakula, kodi anasiya kumvera Yosefe? Ayi sanasiye, koma anazindikira kuti Mulungu ndiye anachita kufuna kuti iye azimvera bambo ake osam’berekawo. Yesu ankadziŵa bwino kwambiri lamulo limene Yehova anauza ana a Aisrayeli. Kodi linali lamulo liti limenelo?
Lemekeza Atate ndi Amayi Ako
Malemba amauza ana kuti: “Lemekeza atate wako ndi amako.” (Deuteronomo 5:16) Mawu akuti ‘kulemekeza’ nthaŵi zambiri amatchulidwa m’Baibulo pofuna kusonyeza ulemu kapena kuganizira ena. Makolo amene akukusunganiwo mukhoza kuwalemekeza motere pochita zinthu mowakomera mtima, kuwapatsa ulemu wawo, kumvera zimene akunena, ndiponso kukhala wololera akafuna kuti muchite chilichonse chimene mungakwanitse.
Nanga bwanji mukaona kuti zimene makolo anuwo akufuna n’zoti simuzingakwanitse? Zimenezi zimachitika ndithu. Makolo onse ngopanda ungwiro, kaya akhale okuberekani kapenanso osakuberekaniwo. Akamalakwitsa zinthu, kuwamvera kungakhale kovuta kwambiri. Zimenezi zikamachitika, n’zosadabwitsa ngati inuyo mumangoyamba kuganizira zakuti ameneŵa si makolo anu okuberekani ndiponso n’kumaona kuti mwina si bwino kumangowamvera zilizonse. Koma kodi ndi bwinodi kusawamvera zilizonse?
Mwina kuganizira zimene zinachitikira Yesu kungakuthandizeni. Musaiwale kuti iye anali wangwiro. (Ahebri 4:15; 1 Petro 2:22) Koma bambo ake amene anam’lera ngakhalenso amayi ake om’bereka anali opanda ungwiro. Ndiyetu n’zotheka kuti nthaŵi zina Yesuyo ankaona kuti makolo ake alakwitsa zinthu. Kodi iye sankamvera bambo ake opanda ungwirowo, a Yosefe, kapena zinthu zinazake zimene Mariya ankalakwitsa pomulangiza monga mayi? Ayi, sankatero. Baibulo limatiuza kuti pamene Yesu anali kukula, anapitiriza ‘kuwamvera’ makolo ake.—Luka 2:51.
Ndiye inuyo mukasiyana maganizo ndi makolo amene sanakuberekeni, n’kutheka kuti mungamaone kuti iwowo ndiwo alakwitsa zinthu. Komano ndi bwino kukumbukira kuti nanunso ndinu wopanda ungwiro. Choncho n’zotheka ndithu kuti inuyo ndiye amene mungakhale wolakwa. Kaya wolakwa akhale inuyo kapena makolowo, kodi si chanzeru kutsatira chitsanzo cha Yesu? (1 Petro 2:21) Kutero kungakuthandizeni kuti muziwamvera. Koma palinso chifukwa china chachikulu choti muzimvera makolo anu.
Baibulo limati: “Ana inu, mverani akubala inu m’zonse, pakuti ichi Ambuye akondwera nacho.” (Akolose 3:20) N’zoonadi, mukamamvera makolo, Atate wanu wakumwamba amakondwera. (Miyambo 27:11) Ndipo amafuna kuti muphunzire kumvera chifukwa chakuti amafuna kuti inunso muzikhala okondwa. Mawu Ake amalimbikitsa ana kumvera ponenanso kuti, “kuti kukhale bwino ndi iwe, ndi kuti ukhale wa nthaŵi yaikulu padziko.”—Aefeso 6:3.
Kugwirizana Kwambiri ndi Makolo Anu Osakuberekani
Kugwirizana ndi makolo anu osakuberekani si kungowapatsa ulemu kapenanso kuwamvera basi. Tikukhulupirira kuti mumafuna kukhala pakhomo pamene anthu ake ndi ogwirizana ndiponso okondana. Makolo anu osakuberekaniwo ali ndi udindo woonetsetsa kuti zimenezi zitheke. Koma inunso mungathandizepo kwambiri. Mungathandizepo motani?
Choyamba, pezani njira zoti muzoloŵerane kwambiri ndi makolo anuwo. Afunseni za banja lawo, zimene akhala akuchita m’moyo mwawo, ndi zimene amakonda. Afunseni nzeru mukakhala ndi zinazake Miyambo 20:5) Chachiŵiri, pezani njira zoti muthandize kuti zinthu ziziyenda bwino pakhomopo, monga kugwira nawo ntchito zina ndi zina zapakhomo mosachita kukuuzani.
zimene zikukusautsani mumtima, ndipo muzitero panthaŵi imene akuoneka kuti ndi omasuka ndiponso osangalala. (Bwanji nanga za makolo anu okuberekani? Ngati mwaganiza zowafunafuna, kapena ngati iwowo aganiza zokufunafunani, kodi ndiye kuti zimenezi zingasokoneze kugwirizana kwanu ndi makolo anu osakuberekani? Kale, mabungwe opereka ana kwa makolo osawabereka ankakana kuululira makolo a anawo kumene kuli ana awo kapenanso kuululira anawo kumene kuli makolo awo owabereka. Masiku ano, malamulo a m’mayiko ena saletsa zimenezi, ndipo ana ambiri amene ali m’manja mwa makolo osawabereka akhala akuonana maso ndi maso ndi makolo awo owabereka koma osawakumbukira n’komwe. Komatu malamulo otere angakhale osiyana ndi akwanuko.
Mulimonse mmene zingakhalire, nkhani yoti mufunefune makolo anu okuberekani kapena ayi ndi ya kadziŵamwini, ndipo ndi yovuta. Achinyamata amene ali m’manja mwa makolo osawabereka amaganiza mosiyanasiyana kwambiri pankhaniyi. Ena amafunitsitsa kupeza makolo awo owabereka, ndipo ena safuna n’komwe kutero. Komabe tikukutsimikizirani kuti achinyamata ambiri amene ali m’manja mwa makolo osawabereka anapezana ndi makolo awo owabereka koma sanasiye kugwirizana ndi makolo awo osawaberekawo.
Funsirani nzeru kwa makolo anu osakuberekaniwo, mwinanso kwa anzanu okhwima nzeru mumpingo wanu wachikristu. (Miyambo 15:22) Yambani mwaganiza mozama musanachite china chilichonse chifukwa Miyambo 14:15 amanena kuti, “wochenjera asamalira mayendedwe ake.”
Ngati mwaganiza zoyesa kugwirizana ndi makolo anu okuberekani, yesetsani kuwatsimikizira makolo anu osakuberekaniwo kuti mupitiriza kuwakonda ndi kuwapatsa ulemu. Mukatero ndiye kuti mudzapitiriza kugwirizana ndi makoloŵa, amene akulerani ndi kukuphunzitsani, kwinaku mutayamba kuwadziŵa bwino makolo amene anakuberekaniwo n’kukuperekani m’manja mwa makolo ena mudakali mwana.
Muzikonda Kwambiri Atate Wanu Wakumwamba
Achinyamata ambiri oleredwa ndi makolo osawabereka amavutika mtima chifukwa choopa kusiyidwa. Amaopa kuti makolo osawaberekawo angawasiye monga anachitira makolo awo owabereka. N’zomveka ndithu kukhala ndi mantha oterowo. Komabe, osaiwala mawu anzeru aŵa: “Mulibe mantha m’chikondi; koma chikondi changwiro chitaya kunja mantha.” (1 Yohane 4:18) Musalole kufooledwa ndi mantha achabechabe akuti anthu amene mumawakonda akusiyani. M’malo mwake, limbikirani kwambiri kukonda ena, osaiwalanso onse a m’banja mwanu. Koma chofunika kwambiri n’chakuti muzikonda kwambiri Atate wanu wakumwamba, Yehova Mulungu. Iye ndi wodalirika kwathunthu, ndipo sasiya ana ake okhulupirika. Yehova akhoza kuthetsa mantha anuwo.—Afilipi 4:6, 7.
Catrina, yemwe anatengedwa ndi makolo osamubereka adakali mwana, ananena kuti kuŵerenga Baibulo ndiko kunam’thandiza kwambiri kukonda Mulungu ndiponso kuti moyo wake aziumva kukoma ndi kutinso ukhale waphindu. Iye ananena kuti kukondana kwambiri ndi Yehova “n’kwabwino kwambiri chifukwa Atate wathu wakumwambayu amadziŵa mmene timamvera.” Lemba limene Catrina amalikonda kwambiri ndi la Salmo 27:10, limene limati: “Pakuti wandisiya atate wanga ndi amayi wanga, koma Yehova anditola.”
Ngati mukufuna kudziŵa zambiri kapena ngati mukufuna kuti wina azibwera kudzachita nanu phunziro la Baibulo la panyumba kwaulere, tumizani dzina lanu ndi adiresi ya kumene mumakhala kwa Mboni za Yehova, Box 30749, Lilongwe 3, Malawi, kapena ku adiresi yoyenera pa maadiresi osonyezedwa patsamba 5.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 7 Onani nkhani yakuti “Kodi Ndinakhaliranji Mwana wa Makolo Amene Sanandibereke?” mu Galamukani! ya May 8, 2003.
[Chithunzi patsamba 32]
Pezani njira zoti muzigwirizana ndi makolo anu amene sanakuberekeni