Kodi Zinthu Zidzasintha?
Kodi Zinthu Zidzasintha?
MASIKU ano Bungwe Loona Zaumoyo Padziko Lonse ndiponso magulu ena amene amakhudzidwa ndi nkhaniyi akugwira ntchito zofufuza ndiponso kuchepetsa matenda. Mabungwe osiyanasiyana akufalitsa nkhani ndiponso kuthandiza kafukufuku wa mankhwala ndiponso njira zatsopano zochepetsera matenda ofalitsidwa ndi tizilombo ndipo akuchita zonsezi n’cholinga choti vuto la matendaŵa lisakule. Anthu paokhapaokha ndiponso magulu angathandizanenso kwambiri potsinana khutu komanso podziteteza. Komabe kuteteza anthu paokhapaokha n’kosiyana ndi kuthetsa vutoli padziko lonse.
Akatswiri ambiri amaona kuti, kuti matenda achepe m’pofunika kugwirizana ndiponso kudalirana padziko lonse. Laurie Garrett, mtonkhalani yemwe analandira mphotho yotchedwa Pulitzer, analemba m’buku lake lonena za matenda atsopano lakuti The Coming Plague—Newly Emerging Diseases in a World Out of Balance kuti: “Pakuti masiku ano anthu a m’mayiko osiyanasiyana akuchitira limodzi zinthu zambiri ndi bwino kuti kulikonseko anthu akamachita zinthu asamangoganizira za dera, dziko kapena chigawo chimene akukhalacho ayi. Majeremusi ndiponso tizilombo towafalitsa, sitidziŵa zoti apa anthu anayikapo malire ayi.” Matenda akabuka m’dziko lina sachedwa kuyamba kudetsa nkhaŵa anthu a m’mayiko oyandikana nalo komanso a padziko lonse.
Maboma ndiponso anthu ena amakayikirabe chithandizo chilichonse chochokera kunja, ngakhale cholinga chake chitakhala chofuna kuchepetsa matenda. Kuphatikizanso apo, nthaŵi zambiri chithandizo chochokera m’mayiko osiyanasiyana akunja sichiyenda bwino chifukwa chakuti maboma ena saganizira za mtsogolo ndiponso chifukwa cha umbombo pankhani za malonda. Kodi majeremusi ndi amene apambane pankhondo imene akumenyana ndi
anthuyi? Wolemba mabuku wina, Eugene Linden, amene akuona kuti majeremusi ndiwo apambane ananena kuti: “Panopo madzi ayeza kale m’khosi.”Cholimbitsa Mtima Chilipo
Kutsogola kwa zasayansi ndi zaumisiri sikungapikisane ngakhale pang’ono ndi kuchuluka kwa matenda. Ndiponsotu pali mavuto ena ambirimbiri angati ameneŵa, moti vuto la matenda ofalitsidwa ndi tizilombo ndi limodzi chabe mwa mavutoŵa. Koma chotilimbitsa mtima chilipo. Ngakhale kuti asayansi angoyamba kumene kumvetsa mgwirizano wovuta kuulongosola umene ulipo pakati pa zinthu zamoyo, iwo amadziŵa kuti dzikoli limatha kudzikonza lokha penapake pakalakwika. Dziko lathuli linapangidwa mwakuti lingathe kubwezeretsa mwakale mbali zimene zinawonongeka. Nthaŵi zambiri malo ena, monga malo amene anadulapo mitengo yonse, amamereranso nkhalango, ndipo m’kupita kwa nthaŵi, majeremusi osiyanasiyana, tizilombo, ndiponso zinyama zimayamba kukhala mmene zimayenera kukhalira.
Chofunikanso kwambiri n’chakuti chilengedwe chodabwitsachi chimatsimikizira kuti chinachita kulengedwa ndi Mulungu amene analipatsa dzikoli mphamvu zimenezi. M’gulu la asayansi enieniwo, muli asayansi ambirimbiri amene amavomereza kuti payenera kukhala winawake wanzeru amene analenga zinthu zimene zili padziko pano. Inde anthu amene amaganiza mozama sangakane zakuti kuli Mulungu. Baibulo limanena kuti Mlengiyo, yemwe ndi Yehova Mulungu, ngwamphamvuyonse ndiponso ngwachikondi. Iye amafunitsitsa kuti tizisangalala.
Baibulo limalongosolanso kuti, chifukwa chakuti munthu woyamba anachimwa mwadala, anthu anakhala opanda ungwiro, anayamba kumadwala ndiponso kumafa. Kodi ndiye kuti tizingovutika mpaka kalekale? Ayi ndithu! Mulungu akufuna kuti dzikoli lisanduke paradaiso woti anthu azikhalamo bwinobwino ndi zinyama zina, zazikulu ndi zazing’ono zomwe. Baibulo limanena zoti m’dzikoli cholengedwa chilichonse, kaya n’chilombo chachikulu kapena kachilombo kakang’ono, sichidzakhala choopsa kwa anthu m’njira ina iliyonse.—Yesaya 11:6-9.
Inde, anthu adzakhala ndi mbali yawo poonetsetsa kuti zinthu zipitirire kukhala choncho pakati pawo komanso pakati pa zachilengedwe. Mulungu analamula munthu kuti ‘aziyang’anira’ dziko. (Genesis 2:15) M’paradaiso amene akubwera mtsogolomu anthu adzachita ntchito imeneyi bwinobwino potsatira malangizo onse ochokera kwa mwiniwake Mlengi. Motero tingathe kuyembekezera mwachidwi nthaŵi imene “wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.”—Yesaya 33:24.