Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kukambirana ndi Katswiri wa Sayansi

Kukambirana ndi Katswiri wa Sayansi

Kukambirana ndi Katswiri wa Sayansi

MU 1996, Michael J. Behe, amene panopa ndi pulofesa wa sayansi ya zimene zimachitika m’kati mwa zinthu zamoyo pa yunivesite ya Lehigh ku Pennsylvania, m’dziko la United States, anatulutsa buku lake lotsutsana ndi chiphunzitso cha chisinthiko, lakuti Darwin’s Black Box—The Biochemical Challenge to Evolution. Galamukani! yachingelezi ya May 8, 1997 inali ndi nkhani zingapo zofotokoza mutu wapachikuto wakuti “Kodi Tinapezeka Bwanji Padziko Pano? Mwangozi Kapena Tinachita Kulengedwa?” Nkhani zimenezi zinatchulapo buku la Behe. Pa zaka pafupifupi teni zomwe zadutsa kuchokera pamene bukuli linatulutsidwa, asayansi okhulupirira chisinthiko akhala akutsutsa mfundo zomwe Behe analemba. Popeza Behe ndi Mkatolika, anthu otsutsana naye amunena kuti nzeru zake zasayansi zasokonekera chifukwa cha zikhulupiriro zake zachipembedzo. Ena akuti maganizo ake ndi osemphana ndi sayansi. Olemba Galamukani! analankhula ndi Pulofesa Behe ndipo anam’funsa kuti afotokoze chomwe chachititsa kuti mfundo zake zibutse mkangano waukulu choncho.

GALAMUKANI!: N’CHIFUKWA CHIYANI MUKUONA KUTI ZAMOYO ZIMAPEREKA UMBONI WOSONYEZA KUTI ZINACHITA KUPANGIDWA MWANZERU?

PULOFESA BEHE: Tikaona mbali zosiyanasiyana za chinthu chopangidwa mwaluso, timadziwa kuti zinachita kupangidwa ndi winawake. Mwachitsanzo, tangoganizirani makina amene timagwiritsa ntchito tsiku ndi tsiku monga makina otchetchera kapinga, kapena galimoto kapenanso zipangizo zina zosavuta kupanga. Chitsanzo chimene ndimakonda kugwiritsa ntchito pa nkhani imeneyi ndi msampha wa makoswe. Mumadziwa kuti unachita kupangidwa chifukwa mumaona mbali zosiyanasiyana zitakonzedwa n’cholinga chogwira ntchito yogwira makoswe.

Sayansi tsopano yapita patsogolo mokwanira moti yatulukira tinthu ting’onoting’ono tomwe timapanga zamoyo. Ndipo asayansi achita kaso kutulukira kuti tinthu ting’onoting’ono timeneti, n’topangidwa mwaluso kwambiri. Mwachitsanzo, m’kati mwa maselo amoyo muli tinthu ting’onoting’ono tomwe timakhala ngati timagalimoto, tomwe timanyamula zinthu kuchokera ku mbali imodzi ya selo kuzipititsa ku mbali ina. Mulinso tinthu tina tomwe timakhala ngati tizikwangwani, tomwe timauza timagalimoto timeneti kuti tikhotere kumanzere kapena kumanja. Maselo ena ali ndi tinthu tokhala ngati timainjini tomwe timakankha maselowo m’madzi. Zikakhala kuti ndi zinthu zina, anthu akaona zinthu zopangidwa mwaluso zoterozo amanena kuti zinachita kupangidwa. Popeza chiphunzitso cha Darwin sichikufotokoza bwinobwino mmene zinthu zochititsa kasozi zinayambira, palibe njira ina yofotokozera zimenezi. Popeza nthawi zonse takhala tikukhulupirira kuti zinthu zikakhala zokonzedwa bwino mwa njira imeneyi ndiye kuti zinachita kupangidwa, sitikulakwa pokhulupirira kuti tinthu timeneti natonso tinachita kupangidwa ndi winawake wanzeru.

GALAMUKANI!: KODI MUKUGANIZA KUTI N’CHIFUKWA CHIYANI ASAYANSI ANZANU AMBIRI SAGWIRIZANA NDI MFUNDO YANU YOTI ZINTHU ZINACHITA KUPANGIDWA NDI WINAWAKE WANZERU?

PULOFESA BEHE: Asayansi ambiri sagwirizana ndi mfundo yangayi chifukwa amaona kuti mfundo yoti zinthu zinachita kupangidwa imabutsa nkhani zina zosakhudzana ndi sayansi, zonena za zinthu zimene asayansi sangathe kuziona. Ambiri sasangalala ndi nkhani zimenezi. Komabe, kuyambira kale ine ndinaphunzitsidwa kuti sayansi imayenera kulondola kumene umboni ukupita. Ndikuona kuti n’kusalimba mtima kukana mfundo imene ikuchita kuonekeratu bwino ndi umboni umene ulipo, chifukwa choopa zotsatira zomwe zingakhalepo utaivomereza.

GALAMUKANI!: KODI MUMAWAYANKHA BWANJI OTSUTSA AMENE AMANENA KUTI KUVOMEREZA ZOTI ZAMOYO ZINACHITA KUPANGIDWA N’KULIMBIKITSA UMBULI?

PULOFESA BEHE: Si umbuli umene umachititsa munthu kufika pa mfundo yoti zinthu zinachita kupangidwa mwanzeru. Timafika pa mfundo imeneyi, osati chifukwa cha zinthu zomwe sitikudziwa, koma chifukwa cha zinthu zomwe tikudziwa. Panthawi imene Darwin anatulutsa buku lake lakuti The Origin of Species zaka 150 zapitazo, anthu sankadziwa zambiri zokhudza moyo. Asayansi ankaganiza kuti selo ndi kanthu kachabechabe koti kakanatha kungopangika kokha m’matope a pansi pa nyanja. Koma kuchokera pa nthawi imeneyo, asayansi atulukira kuti maselo ndi opangidwa mwaluso kwambiri, kuposeratu makina amene timagwiritsa ntchito m’zaka za m’ma 2000 zino. Mmene maselo amagwirira ntchito zawo, zimasonyezeratu kuti anapangidwa n’cholinga choti azigwira ntchito zimenezo.

GALAMUKANI!: KODI SAYANSI YATULUKIRA UMBONI ULIWONSE WOSONYEZA KUTI KUPULUMUKA KWA ZAMOYO ZAMPHAMVU ZOKHAZOKHA, NDIKO KUNACHITITSA KUTI MASELO AMENE MWANENA AJA APANGIKE?

PULOFESA BEHE: Mukafufuza m’mabuku a sayansi, mupeza kuti palibe amene watsimikizirapo momwe maselo anakhalirako, pogwiritsa ntchito njira zimene Darwin anafotokoza, kaya mwa kuchita kafukufuku kapena mwa kuzifotokoza ndi mfundo zasayansi. Zimenezi zili choncho ngakhale kuti pa zaka teni zomwe zadutsa kuchokera pamene ndinatulutsa buku langa, mabungwe ambiri asayansi, monga bungwe la National Academy of Sciences ndi la American Association for the Advancement of Science, akhala akuchenjeza anthu awo pafupipafupi kuti achite zonse zomwe angathe kuti afafanize mfundo yoti zamoyo zimapereka umboni wosonyeza kuti zinachita kupangidwa mwanzeru.

GALAMUKANI!: KODI MUMAWAYANKHA CHIYANI ANTHU AMENE AMATI MBALI ZINA ZA ZOMERA NDI ZINYAMA SIZINAPANGIGWE BWINO?

PULOFESA BEHE: Kulephera kudziwa ntchito imene mbali ina ya chinthu chamoyo imachita sikutanthauza kuti mbaliyo n’njosafunikira. Mwachitsanzo, ziwalo zimene kale ankazitcha zopanda ntchito, poyamba ankati zimasonyeza kuti thupi la munthu ndi zamoyo zina sizinapangidwe bwino. Mwachitsanzo, poyamba anthu ankaganiza kuti kachiwalo ka kumapeto kwa matumbo ndi tinthu tinatake ta kummero, n’ziwalo zopanda ntchito ndipo ankangozichotsa mwachisawawa. Koma kenaka anadzatulukira kuti ziwalo zimenezi zimathandiza thupi kulimbana ndi matenda, ndipo tsopano amaziona kuti n’zofunikira kwambiri.

Mfundo ina yofunika kukumbukira ndi yoti m’zinthu zamoyo, zinthu zina zimachitika mwangozi. Koma galimoto yanga ikapindika penapake kapena ikaphwa tayala, sizitanthauza kuti galimotoyo kapena tayalalo sizinachite kupangidwa. Mofanana ndi zimenezi, sitinganene kuti chifukwa zinthu zina m’zinthu zamoyo zimachitika mwangozi ndiye kuti zinthu zamoyozo sizinachite kupangidwa. Imeneyi si mfundo yomveka.

[Mawu Otsindika patsamba 12]

“Ndikuona kuti n’kusalimba mtima kukana mfundo imene ikuchita kuonekeratu bwino ndi umboni umene ulipo, chifukwa choopa zotsatira zomwe zingakhalepo utaivomereza”