Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndizitsatira Mfundo za M’Baibulo Chifukwa Chiyani?

Ndizitsatira Mfundo za M’Baibulo Chifukwa Chiyani?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Ndizitsatira Mfundo za M’Baibulo Chifukwa Chiyani?

YEREKEZERANI kuti muli ku sukulu ndi atsikana anzanu awiri ndipo mukudyera pamodzi nthawi yopuma. Ndipo mnzanu mmodzi akuyang’ana mwachidwi mnyamata yemwe wangobwera kumene pasukulupo.

Ndiyeno mtsikanayo akuti, “Ukudziwa, mnyamatayu akukufuna. Ndikuona mmene akukuyang’anira. Akuoneka kuti wadyerera maso pa iwe.”

Mtsikana winayo akukunong’onezani kuti, “Chinanso ukudziwa, mnyamatayutu alibe chibwenzi.”

Mnzanu woyamba uja akuti, “Zaipira kuti ndili ndi chibwenzi kale, ndikanam’kopa.”

Ndiyeno akukufunsani funso limene mumadana nalo kwambiri.

“N’chifukwa chiyani ulibe chibwenzi?”

Inu munadziwa kale kuti afunsa zimenezi. Zoona zake n’zakuti mumafuna mutakhala ndi chibwenzi, koma munalangizidwa kudikira kaye mpaka mutafika nthawi yokwatiwa. Koma chifukwa cha . . .

Ndiyeno mnzanu wachiwiriyo akunena zimene inuyo mukuganiza kuti, “Chifukwa cha chipembedzo chako, si choncho?”

Mukudzifunsa kuti, ‘Wadziwa bwanji zimenezi?’

Mnzanu woyamba uja akuti: “Iwe ndiye umangoganiza za Baibulo basi. Bwanji osamasangalalako nthawi zina?”

Kodi zinakuchitikiranipo zimenezi, anzanu kukunyozani chifukwa chotsatira mfundo za m’Baibulo? Kodi munachita chiyani?

Munawauza molimba mtima mfundo zanu za makhalidwe abwino.

Munayesetsa kuwauza zimene mumakhulupirira ngakhale kuti zinali zokuvutani.

Munaona kuti anzanuwo ankakuuzani zoona, moti munaganiza kuti mukumanidwa zinthu zabwino.

Kodi munadzifunsapo kuti, ‘Kodi kutsatira mfundo za m’Baibulo kuli ndi ubwino uliwonse?’ Mtsikana wina dzina lake Deborah anaganizirapo zimenezi. * Iye anati: “Anzanga ankachita zomwe akufuna. Zinkaoneka kuti panalibe aliyense wowaletsa. Ndinkaona ngati mfundo za m’Baibulo n’zopanikiza. Ndinkasirira moyo wa anzanga wongochita zomwe akufuna.”

Kodi N’kulakwa Kukayikira Ubwino wa Mfundo za M’Baibulo?

Wolemba Baibulo Asafu, panthawi ina ankakayikira ngati kutsatira malangizo a Mulungu kunali kwabwino. Iye anati: “Ndinachitira nsanje odzitamandira, pakuona mtendere wa oipa.” Mpaka anafika ponena kuti: “Indedi, ndinayeretsa mtima wanga kwachabe, ndipo ndinasamba m’manja mosalakwa.”—Salmo 73:3, 13.

N’zoonekeratu kuti Yehova Mulungu amadziwa kuti anthu nthawi zina angakayikire ubwino wotsatira malangizo ake. Ndipotu, iye ndiye anapangitsa kuti maganizo a Asafu alembedwe m’Baibulo. Koma kenako, Asafu anazindikira kuti palibe chinthu chabwino ngati kutsatira malamulo a Mulungu. (Salmo 73:28) Kodi n’chiyani chinam’thandiza kuzindikira zimenezi? Asafu anali wanzeru. Anazindikira zimenezi osati chifukwa chokumana ndi mavuto koma chifukwa chophunzira pa zolakwa za ena. (Salmo 73:16-19) Kodi inunso mungatero?

Ganizirani Zimene Zachitikira Ena

Mfumu Davide anazindikira kuti anthu omwe amanyalanyaza malangizo a Mulungu amakumana ndi mavuto. Koma mosiyana ndi Asafu, iye anazindikira zimenezi atakumana kale ndi mavutowo. Davide anachita chigololo ndi mkazi wa mmodzi wa anyamata ake ndipo kenako anayesetsa kubisa tchimo lakelo. Zimenezi zinakhudza kwambiri anthu ena ndi Mulungu yemwe, ndipo zochita zake zinam’bweretsera mavuto aakulu. (2 Samueli 11:1–12:23.) Davide atalapa, Yehova anamuuzira kulemba nyimbo yofotokoza mmene amamvera mu mtima mwake ndipo mawu a m’nyimboyo ali m’Baibulo kuti tiphunzirepo. (Salmo 51:1-19; Aroma 15:4) Choncho, ndi nzeru ndiponso n’zogwirizana ndi Malemba kuphunzira pa zolakwa za ena.

Kuti muthandizidwe kutengera Asafu ndiponso kupewa zolakwa za Davide, ganizirani zimene achinyamata ena a m’mayiko osiyanasiyana, amene panthawi ina analeka kutsatira malangizo a m’Baibulo, ananena atafunsidwa. Iwo anachitapo zachiwerewere. Koma mofanana ndi Davide, iwo analapa ndipo akutumikira Mulungu ndi chikumbumtima chabwino. (Yesaya 1:18; 55:7) Tamvani zimene ananena.

Galamukani!: Kodi n’chiyani chinakuchititsani kuyamba kuganizira zogonana mpaka kufika pochitadi zimenezo?

Deborah: “Kusukulu kwathu aliyense anali ndi chibwenzi ndipo ankaoneka kuti akusangalala. Pamene ndinkacheza nawo n’kuwaona akumpsopsonana ndi kukumbatirana ndinkasirira kwabasi, ndipo ndinkafuna nditakhala ndi chibwenzi. Nthawi zambiri ndinkangoganiza za mnyamata winawake yemwe ndinkamufuna. Zimenezi zinandichititsa kumangofuna tili limodzi ndiponso kuchita chilichonse kuti zomwe ndinkafunazo zitheke.”

Mike: “Ndinkawerenga ndi kuonera mapulogalamu olimbikitsa kugonana. Ndipo kukambirana ndi anzanga nkhani za kugonana kunandichititsa kufuna kudziwa kuti zimakhala bwanji. Ndiyeno, pamene tinali awiriwiri ndi mtsikana, ndinaganiza kuti ndingachite chilichonse ndi iye koma n’kudziletsa kuti ndisagonane naye.”

Andrew: “Ndinkakonda kuonera zithunzi zolaula pa Intaneti. Ndinayambanso kumwa mowa kwambiri. Ndipo ndinkapita ku zisangalalo ndi achinyamata omwe sankatsatira kwenikweni malangizo a m’Baibulo.”

Tracy: “Ndili ndi zaka 16, chinthu chofunika kwa ine chinali kukhala ndi chibwenzi changa basi. Ndinkadziwa kuti kugonana musanakwatirane n’koipa, koma sindinkadana nako. Ndinalibe maganizo ogonana ndi munthu ndisanakwatirane naye koma ndinalephera kudziletsa. Kwa nthawi ndithu, chikumbumtima changa sichinkagunda n’komwe, moti sindinkaonanso kuti ndikulakwa.”

Galamukani!: Kodi zochita zanuzo zinakubweretserani chisangalalo?

Deborah: “Poyamba ndinkaona kuti ndili ndi ufulu ndipo ndinali wosangalala kuti ndikuchita zomwe anzanga akuchita. Koma maganizo amenewa sanakhalitse. Ndinayamba kudzimva kuti ndine wolakwa, wa khalidwe loipa, ndiponso sindinkasangalala. Ndinkanong’oneza bondo chifukwa cholephera kudzisunga. Kuyambira nthawi imeneyo, ndakhala ndikudzifunsa kuti, ‘Kodi chifukwa chiyani ndinkaganiza kuti sindingakumane ndi zotsatirapo zoipa?’ Ndiponso kuti, ‘Chifukwa chiyani ndinanyalanyaza malangizo achikondi a Yehova?’”

Mike: “Ndinkaona ngati kuti mbali ina ya thupi langa yafa. Ndinayesetsa kunyalanyaza mmene zochita zanga zinkakhudzira ena, koma sizinandithandize. Zinkandiwawa kuona kuti ndinkakhumudwitsa anthu ena chifukwa chofuna kusangalala. Sindinkagona. M’kupita kwa nthawi, ndinasiya kusangalala ndi khalidwe logonana, ndipo kuganizira zomwe ndinkachita kunkandiwawa ndiponso kunkandichititsa manyazi.”

Andrew: “Pang’ono ndi pang’ono kuchita zoipa sikunkandivuta. Komabe, ndinkadziimba mlandu ndipo sindinkasangalala ndi zimene ndinkachita.”

Tracy: “Sipanatenge nthawi kuti ndikumane ndi zotsatirapo za zochita zanga. Kusadziletsa kunawononga unyamata wanga. Ndinkaganiza kuti ine ndi chibwenzi changa tizisangalala. Koma si mmene zinalili. M’malo mwake, tinali owawidwa mtima, osasangalala ndipo tinangokhumudwitsana. Usiku uliwonse ndinkangokhalira kulira, ndipo ndinkalakalaka ndikanatsatira malangizo a Yehova.”

Galamukani!: Kodi mungawauze chiyani achinyamata amene amaganiza kuti malangizo a m’Baibulo ndi opanikiza?

Deborah: “Simungakhale wosangalala ngati munyalanyaza malangizo a m’Baibulo. Ganizirani mmene Yehova amamvera mukatsatira malangizo ake. Ganiziraninso kwambiri zotsatirapo za kunyalanyaza malangizo ake. Kumbukirani kuti zochita zanu sizimangokhudza inu nokha. Zimakhudzanso anthu ena. Ndipo mukamanyalanyaza malangizo a Mulungu, mumadzipwetekeka.”

Mike: “N’zoona kuti zochita za anzanu zingaoneke zokopa. Koma ganizirani zotsatirapo zake. Ulemu ndi kudzisunga ndi zina za zinthu zamtengo wapatali kwambiri zimene Yehova wakupatsani. Kutaya mphatso zimenezi chifukwa cholephera kudziletsa n’kudzipeputsa. Muziuza makolo anu ndi anthu ena achikulire za mavuto anu. Mukalakwitsa, musamabise ndiponso muzikonza zolakwazo. Mukamachita zinthu motsatira malangizo a Yehova, mumakhala wosangalala.”

Andrew: “Chifukwa chosadziwa zambiri, munthu angaone ngati zochita za anzake n’zosangalatsa. Ndiyeno angatengere zochita zawo. Choncho, muzisankha bwino anzanu ocheza nawo. Muzikhulupirira Yehova, ndipo mudzapewa mavuto ambiri.”

Tracy: “Musamaganize kuti, ‘Ine sizingandichitikire.’ Mayi anga anakhala nane pansi n’kundiuza mwatchutchutchu kuti zochita zanga zingandibweretsere mavuto. Ndinakwiya kwambiri. Ndinkaganiza kuti palibe chimene akudziwa. Koma ineyo ndi amene sindinkadziwa. Muzitsatira malangizo a Yehova ndipo muzicheza ndi anthu amene amachitanso zimenezo. Mukamatero mumakhala osangalala.”

Kodi Malangizo a m’Baibulo Ali Ngati Nyakula Kapena Lamba wa m’Galimoto?

Anzanu akamakunyozani chifukwa chotsatira malangizo a m’Baibulo, muzidzifunsa mafunso awa: ‘Kodi n’chifukwa chiyani akukana kutsatira malangizo a m’Baibulo a makhalidwe abwino? Kodi iwowa awerengapo Baibulo n’kuona ubwino wotsatira malamulo a Mulungu? Kodi aganizirapo mwakuya zotsatirapo za kunyalanyaza malamulowo? Kapena, kodi amangotsatira zimene anthu ena akuchita?’

Muyenera kuti mukudziwa anthu amene ‘amangotsatira unyinji wa anthu.’ (Eksodo 23:2) Kodi simukufuna kuchita zosiyana ndi anthu amenewa? Kodi mungachite bwanji zimenezi? Mungatero mwa kutsatira malangizo a m’Baibulo akuti: “Muzindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino ndi chovomerezeka ndi changwiro.” (Aroma 12:2) Yehova ndi “Mulungu wa chisangalalo,” ndipo amafunanso kuti inu muzisangalala. (1 Timoteyo 1:11; Mlaliki 11:9) Malangizo amene analemba m’Baibulo ndi oti akupindulitseni. Mwina mungawaone ngati nyakula yokupherani ufulu. Koma kunena zoona, malangizo amenewa ali ngati lamba wa m’galimoto amene amateteza munthu kuti asavulale.

Ndithudi, mungakhulupirire zimene Baibulo limanena. Ndipo mukasankha kutsatira malangizo ake, mudzasangalatsa Yehova komanso inuyo mudzapindula.—Yesaya 48:17.

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.mt1130.com.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 17 Mayina mu nkhani ino tawasintha.

ZOTI MUGANIZIRE

▪ Kodi n’chifukwa chiyani zingakuvuteni kutsatira malangizo a m’Baibulo?

▪ Kodi n’chifukwa chiyani mukufunika kuzindikira kuti palibe chinthu chabwino kuposa kutsatira malangizo a Mulungu?