Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingapewe Bwanji Kuona Zithunzi Zolaula?

Kodi Ndingapewe Bwanji Kuona Zithunzi Zolaula?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Ndingapewe Bwanji Kuona Zithunzi Zolaula?

“Mnyamata wina kusukulu kwathu anamata chithunzi cha mtsikana wamaliseche kuseli kwa chitseko cha mosungira katundu wake. Malo osungira katundu akewa anali pafupi kwambiri ndi mosungira katundu wanga.”—Anatero Robert. *

“Nthawi ina ndikufufuza pa Intaneti ntchito imene anatipatsa kusukulu, ndinangozindikira kuti ndatsegula malo a zithunzi zolaula.”—Anatero Annette.

NTHAWI imene makolo anu anali achinyamata, zithunzi zolaula zinali zosowa kwambiri. Koma zikuoneka kuti masiku ano, zithunzi zolaula zangoti mbwee. N’kutheka kuti mungaone mosayembekezera zithunzi zolaula kwa anzanu a kusukulu, monga anachitira Robert amene tam’tchula pamwambayu. Kapenanso monga Annette, mungathe kungoona zithunzi zoterezi zikutulukira mwadzidzidzi mukamafufuza zinthu pa Intaneti. Mtsikana wina wa zaka 19 anati: “Nthawi zina ndikatsegula Intaneti ndimangozindikira kuti patulukira chithunzi cholaula, ngakhale kuti ndimakhala ndikufufuza zinthu zabwinobwino monga kuona mitengo ya zinthu kapena ndalama zimene zili mu akaunti yanga ya kubanki.” *

Zimenezi sizodabwitsa ngakhale pang’ono. Ofufuza ena anapeza kuti achinyamata 90 pa 100 aliwonse a zaka za pakati pa 8 ndi 16 ananena kuti nthawi ina akufufuza zinthu pa Intaneti, zithunzi zolaula zinangotulukira mwadzidzidzi, ndipo nthawi zambiri zimenezi zinachitika akufufuza zinazake zokhudza ntchito yakusukulu. Dziwani kuti pa Intaneti pali malo ambirimbiri amene amakhala ndi zithunzi zolaula zosawerengeka, motero masiku ano m’posavuta kuona zithunzi zolaula kuposa kale. Ngakhale pafoni mungathe kuona zithunzi zolaula. Mtsikana wina wa zaka 16 dzina lake Denise, anati: “Kusukulu kwathu imeneyi ndi nkhani yaikulu. Lolemba lililonse, anthu amangokhalira kufunsana kuti: ‘Bwanawe, dzana ndi dzulo walowetsa zithunzi zotani mu foni yako kuchoka pa Intaneti?’”

Podziwa kuti anthu ambiri amaona zithunzi zolaula, mwina mungadzifunse kuti, ‘Kodi palidi vuto lililonse kuona zithunzi zotere?’ Yankho la funso limeneli n’lakuti inde vuto lilipo, ndipo si vuto limodzi lokha ayi. Tatiyeni tionepo mavuto atatu okha.

Zithunzi zolaula zimachotsera ulemu anthu amene amazipanga komanso amene amaziona.—1 Atesalonika 4:3-5.

▪ Anthu omwe amasangalala ndi zithunzi zolaula amafanana ndi mizimu yoipa ya m’masiku a Nowa yomwe inali ndi chilakolako choipa pa nkhani ya kugonana.—Genesis 6:2; Yuda 6, 7.

Nthawi zambiri machimo okhudza kugonana amayambira pa khalidwe loona zithunzi zolaula.—Yakobe 1:14, 15.

Anthu amene amakodwa mumsampha woonera zithunzi zolaula amagwa m’mavuto aakulu zedi. Taganizirani zitsanzo ziwiri zokha izi:

“Ndinayamba kuona zithunzi zolaula ndili wamng’ono kwambiri, ndipo zinali zovuta kwambiri kusiya khalidweli. Tsopano patha zaka zambiri chisiyireni, koma zithunzizo sizinachokebe m’mutu mwanga. Zinthuzi zimenezi zimakanirira penapake m’mutumu moti nthawi zonse suona kuti chikumbumtima chako n’choyera. Zithunzi zolaula zimamuchotsera munthu ulemu wake n’kumuchititsa kuti azidziona ngati wonyansa ndiponso wachabechabe. Nthawi zonse chikumbumtima chimakupweteka.”—Anatero Erica.

“Kwa zaka 10, ndinali ndi chizolowezi chokonda kuona zithunzi zolaula, koma tsopano ndatha zaka 14 nditasiya khalidweli. Komabe panopa, tsiku lililonse ndimayenera kumenya nkhondo poyesetsa kudzigwira kuti ndisaone zithunzizi. Chilakolako chofuna kuona zithunzizi ndidakali nachobe ngakhale kuti chinachepa kwambiri. Mtima wanga umachitabe dyokodyoko ndithu. Ndimazionabe zithunzizo m’maganizo mwanga. Ndimanong’oneza bondo poganizira kuti ndinayambiranji khalidwe lonyansali. Poyamba sindinkaona kuti pali vuto ayi. Koma panopo palibe angandinamize. Ndithu, zithunzi zolaula zimaononga munthu, n’zoipa kwambiri, ndipo zimachotsera ulemu anthu amene amazipanga komanso amene amaziona. Ngakhale kuti anthu amene amalimbikitsa khalidweli amanena kuti zithunzizi n’zabwino, zoona zake n’zakuti zilibe ubwino uliwonse.”—Anatero Jeff.

Iganizireni Bwinobwino Nkhaniyi

Kodi mungatani kuti mupeweretu kuona zinthu zolaula ngakhale mwangozi? Choyamba, ganizirani bwinobwino za nkhaniyi.

Kodi zithunzi zolaula mumaziona kangati mwangozi?

Sindinazionepo Mwa apo ndi apo

Mlungu uliwonse Tsiku lililonse

Kodi nthawi zambiri zithunzi zolaulazo mumazionera kuti?

Pa Intaneti Kusukulu

Pa TV M’njira zina

Kodi mungathe kuoneratu patali?

Taganizirani zitsanzo izi:

Kodi muli ndi anzanu kusukulu amene amakonda kukutumizirani zithunzi zolaula, mwina pakompyuta kapena pafoni yam’manja? Mukaoneratu patali mungathe kungochotseratu zithunzizo musanazitsegule n’komwe.

Kodi pali mawu aliwonse amene amakonda kubweretsa zithunzi zolaula mukawalemba pa Intaneti pofufuza zinazake? Kudziwa zimenezi kungakuthandizeni kukhala osamala kuti pofufuza zinthu, muzisankha mawu ongogwirizana ndi zimene mukufufuzazo basi.

Lembani pamunsipa njira zina zimene zinachititsa kuti mwangozi muone zithunzi zolaula.

․․․․․

Poganizira njira zimenezi, kodi mungatani kuti muchepetse nthawi zimene mumaona mwangozi zithunzi zolaula? (Lembani maganizo anu apa.)

․․․․․

Kodi mumatani mukaona mwadzidzidzi chithunzi cholaula?

Nthawi yomweyo ndimayang’ana kumbali.

Ndimakopeka n’kuchiyang’ana pang’ono.

Ndimachiyang’anabe n’kuyambanso kufufuza zina.

Ngati mwachonga yankho lachiwiri kapena lachitatu, kodi mungakhale ndi zolinga zotani pofuna kuthetsa vuto lanuli?

․․․․․

Kuthetsa Vutoli

Anthu ena amene amaona mwangozi zithunzizi amakopeka mpaka kuyamba chizolowezi choona zithunzi zotere. Khalidwe limeneli n’lovuta kwambiri kulithetsa. Jeff, amene tam’tchula kumayambiriro uja anati: “Ndisanayambe kuphunzira Baibulo, ndinkaona zithunzi zolaula ndiponso ndinkagwiritsira ntchito kwambiri pafupifupi mankhwala alionse odziwika bwino osokoneza bongo. Koma pa zinthu zonsezi, palibe chinthu chimene chinali chovuta kwambiri kusiya kuposa zithunzi zolaula.”

Ngati muli ndi chizolowezi choona zithunzi zolaula, musataye mtima. N’zotheka kusiya. Zingatheke bwanji?

Zindikirani cholinga cha zithunzi zolaula. Zinthunzi zolaula ndi njira ya Satana yomwe cholinga chake ndicho kunyoza zinthu zimene Yehova anakonza kuti zikhale zolemekezeka. Mukamvetsa kuti cholinga cha zithunzi zolaula n’chimenechi mungathe kuyamba ‘kudana nacho choipa.’—Masalmo 97:10.

Ganizirani zotsatira zake. Zithunzi zolaula zimawononga mabanja. Zimachititsa anthu kusalemekeza akazi ndi amuna. Zimam’chotsera ulemu munthu amene akuzionayo. N’chifukwa chaketu Baibulo limati: “Wochenjera aona zoipa, nabisala.” (Miyambo 22:3) Pamunsipa lembanipo vuto limene lingakugwereni ngati mutakhala ndi chizolowezi choona zithunzi zolaula.

․․․․․

Tsimikizani mtima. Munthu wina wokhulupirika dzina lake Yobu, anenana mawu akuti: “Ndinapangana ndi maso anga, potero ndipenyerenji namwali?” (Yobu 31:1) Nanunso mungathe kutsimikiza mtima kuchita zotsatirazi:

Sindidzafufuzanso zinthu pa Intaneti ndili ndekhandekha m’chipinda.

Ngati chithunzi cholaula chitatulukira mwadzidzidzi, ndizichitseka nthawi yomweyo.

Ngati nditayambiranso khalidweli, ndiziuza munthu wina wachikulire amene ndimagwirizana naye.

Lembani chinthu chimodzi kapena ziwiri zimene mwatsimikiza kuchita kuti zikuthandizeni kuthetsa vuto loona zithunzi zolaula.

․․․․․

Pemphererani za nkhaniyi. Wamasalmo anapemphera kwa Yehova kuti: “Muchititse mlubza maso anga ndisapenye zachabe.” (Masalmo 119:37) N’zoona kuti mwina zingakuvuteni kusiya chizolowezi chimene thupi lauchimoli likulakalaka. Koma Yehova Mulungu akufuna kuti zinthu zikuyendereni bwino, motero angathe kukupatsani “mphamvu yoposa yachibadwa” kuti muchite zabwino.—2 Akorinto 4:7.

Uzaniko munthu wina. Kodi mumachita manyazi kuuza munthu wina? Mwina mumatero, koma taganizirani mmene mungamasukire mumtima mwanu mutaulula vuto lanulo. Munthu amene mungamuuzeyo angathe kukhala ngati “m’bale [amene] anabadwira kuti akuthandize pooneka tsoka.” (Miyambo 17:17) Nthawi zambiri njira yothandiza kwambiri kuthetsera vuto limeneli ndiyo kukhala ndi munthu womuuza zakukhosi.

Ngati muli ndi chizolowezi choona zithunzi zolaula, lembani pamunsipa dzina la munthu wachikulire amene mungamasuke kumuuza za vuto lanulo.

․․․․․

Zindikirani kuti mungathe kupambana nkhondo yolimbana ndi vuto loona zithunzi zolaula. Ndipotu, nthawi iliyonse mukakana kuona zithunzi zoterezi, ndiye kuti mwapambana mbali yaikulu ndithu ya nkhondoyi. Nthawi iliyonse imene mwachita zimenezi, muuzeni Yehova, ndipo muthokozeni pokupatsani mphamvu zochitira zimenezo. Nthawi zonse kumbukirani kuti mukapewa khalidwe loipa loona zithunzi zolaula, mumasangalatsa mtima wa Yehova.—Miyambo 27:11.

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.mt1130.com.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Mayina m’nkhani ino asinthidwa.

^ ndime 5 Mawu akuti zithunzi zolaula amatanthauza zithunzi zamaliseche zomwe cholinga chake ndicho kum’patsa munthu chilakolako chofuna kugonana. Nkhani zowerenga kapenanso mawu odzutsa chilakolalo angakhalenso m’gulu la zinthu zolaula.

ZOTI MUGANIZIRE

▪ Kodi zithunzi zolaula zimanyoza bwanji zinthu zimene Mulungu anakonza kuti zikhale zolemekezeka?

▪ Kodi ndi zinthu zotani zimene zingakutetezeni kuti musaone zithunzi zolaula?

▪ Kodi m’bale wanu amene ali ndi vuto loona zithunzi zolaula mungam’thandize bwanji?

[Chithunzi pamasamba 12, 13]

Kodi muli ndi anzanu kusukulu amene amakonda kukutumizirani zithunzi zolaula pafoni?