Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Mu 2006, “atolankhani 167 ndiponso anzawo akuntchito,” monga madilaivala ndi omasulira, “anafa ali pantchito yawo ya utolankhani kwinakwake.” Ambiri anali kulemba nkhani zokhudza umbanda, katangale, kapena zachiwawa zinazake zochitika kwawoko. Anthu okwana 133 anachita kuphedwa.—Zachokera ku bungwe la INTERNATIONAL NEWS SAFETY INSTITUTE, KU BELGIUM.

Chaka chilichonse amapanga zipolopolo pafupifupi 10 kapena 14 biliyoni. “Izi ndi zipolopolo zambiri zedi, zokwanira kuphera anthu ochuluka mowirikiza kawiri chiwerengero cha anthu onse a padziko pano.”—Zachokera ku bungwe la ROYAL MELBOURNE INSTITUTE OF TECHNOLOGY, KU AUSTRALIA.

Kodi Pali Zivomezi Zochita Kupanga?

Malingana ndi lipoti la m’nyuzipepala ina ya ku Germany, (yotchedwa Die Zeit) akuti kuyambira m’ma 1800, pachitika zivomezi zazikulu zoposa 200 chifukwa cha zochita za anthu. Ntchito za m’migodi zinachititsa theka la zivomezi zimenezi. Zina zinachitika chifukwa cha kukumba zitsime za mafuta, kapena za madzi; kuthira mankhwala m’zitsime zakuya, ndiponso kumanga madamu a madzi. Mu 1989, mzinda wa Newcastle, ku Australia, unawonongedwa ndi chivomezi chimene asayansi amati chinachitika chifukwa cha migodi ya malasha. Chivomezichi chinapha anthu 13, kuvulaza anthu 165, ndipo chinawononga zinthu zokwana madola 3 biliyoni ndi theka. Akuti chivomezichi chinawononga ndalama zochuluka kuposa ndalama zonse zimene anapeza pa malonda a malasha ku Newcastle, chiyambire malondawa zaka pafupifupi 200 zapitazo.

Chikatolika cha ku France Chafika Penapake

Mu 1994, anthu 67 pa 100 aliwonse ku France ankanena kuti ndi Akatolika. Koma malingana ndi magazini ina ya kumeneku (yotchedwa Le Monde des Religions), panopo ndi anthu 51 pa 100 aliwonse amene amati ndi Akatolika. Ofufuza anapeza kuti theka la Akatolika a ku France amapita ku tchalitchi pokhapokha ngati kukuchitika mwambo winawake wapadera, monga ukwati. Ngakhale kuti anthu 88 pa 100 aliwonse amanena kuti amadziwa Pemphero la Ambuye, anthu 30 pa 100 aliwonse sapemphera n’komwe. Pafupifupi theka la mabanja onse Achikatolika ali ndi Baibulo, koma zimenezi sizikutanthauza kuti amaliwerenga.

Ana Ovutika Kulankhula Bwino

Magazini ina ya ku Poland (yotchedwa Wprost) inati: “Ana ambiri amayamba mochedwa kulankhula ndipo sadziwa mawu ambiri, chifukwa choti anthu akuluakulu salankhula nawo.” Patsiku, amayi ambiri amakhala ndi ana awo kwa mphindi 30 zokha basi ndipo abambo ambiri amakhala ndi ana awo “kwa mphindi 7 zokha basi.” Chifukwa cha zimenezi, pafupifupi mwana mmodzi pa ana asanu aliwonse “amakhala ndi vuto linalake lokhudza kulankhula lobwera chifukwa chonyalanyazidwa ndi makolo.” Michał Bitniok, yemwe ndi katswiri wa chilankhulo komanso dokotala wa matenda okhudza kulankhula pa yunivesite ya Silesia, anachenjeza kuti: “Ana amenewa mukawalekerera, vuto lawolo lingachititse kuti adzavutike akayamba sukulu ndiponso akadzakula.”

Anthu ku Japan Adakali ndi Zikhulupiriro Zambiri

Ku Japan kuli vuto lalikulu lotaya zinyalala m’malo osaloledwa ndi boma. Apolisi amene amayendera mzinda masana akulephera kuthetsa vutoli chifukwa anthu anayamba kubweretsa zinyalala zawozo usiku. Podziwa zikhulupiriro za anthu a ku Japan, tsopano aboma achepetsa vutoli poika zinthu zofiira zokhala ngati zipata m’malowo. Zinthuzi zimaoneka ngati zipata zolowera ku kachisi wa chipembedzo chotchedwa Shinto. Nyuzipepala ina kumeneko (yotchedwa IHT Asahi Shimbun) inati: “Iyi ndi njira yachidule kwabasi yotetezera kutaya zinyalala. Anthu amaona kuti zipata zofiirazi n’zopatulika, motero amaopa kutaya zinyalala pafupi ndi zipatazi poopa kuitana masoka.” Anthu ambiri anasiyadi kutaya zinyalala pafupi ndi zipatazi. Koma nyuzipepalayo inanenanso kuti: “Anthuwo akutayabe zinyalalazo m’malo ena apafupi, omwe mulibe zipata zoterezi.”