Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Baibulo Limanena

Zimene Baibulo Limanena

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Kukhala Mutu Wabanja Kumatanthauza Chiyani Kwenikweni?

M’MAYIKO ambiri, anthu okwatirana amalumbira pamwambo wa ukwati wawo ndipo mkwatibwi amalonjeza kuti azidzamvera mwamuna wake. Komabe, akazi ambiri sasangalala ndi mfundo yoti mwamuna akhale mutu m’banja. Taonani zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhani imeneyi. Muona kuti zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi n’zoyenera ndiponso zothandiza.

Zimene Mulungu Amafuna pa Nkhani ya Umutu

Baibulo limafotokoza pa Aefeso 5:22-24 mmene umutu uyenera kukhalira. Lembali limati: “Akazi agonjere amuna awo monga kugonjera Ambuye, chifukwa mwamuna ndiye mutu wa mkazi wake monganso Khristu alili mutu wa mpingo . . . Ndipotu, monga mpingo umagonjera Khristu, akazinso agonjere amuna awo m’chilichonse.” Popeza “mwamuna ndiye mutu wa mkazi wake,” iye ayenera kutsogolera zochitika m’banja lake ndipo mkazi ayenera kutsatira zimenezi ndiponso kulemekeza mutu wake.—Aefeso 5:33.

Ulamuliro wa mwamuna ndi wocheperapo chifukwa iyenso afunikira kugonjera Mulungu ndi Khristu. Alibe mphamvu zouza mkazi wake kuti asamvere malamulo a Mulungu kapena kumuuza kuti asiye kumvera chikumbumtima chake malinga ndi zimene anaphunzira m’Baibulo. Ngakhale kuti ulamuliro wa mwamuna uli ndi malire amenewa, Mulungu anam’patsa mphamvu zoti azisankha chochita pa nkhani zikuluzikulu zokhudza banja lake.—Aroma 7:2; 1 Akorinto 11:3.

M’Baibulo muli malamulo oti amuna azichita umutu wawo mwachikondi ndipo aziika zofuna za mkazi wawo pamalo oyamba. Lemba la Aefeso 5:25 limati: “Amuna inu, pitirizani kukonda akazi anu, monga Khristu anakonda mpingo nadzipereka yekha chifukwa cha mpingowo.” Mwamuna amene amatsatira chitsanzo chabwino cha Khristu chosonyeza chikondi amapewa kuchita umutu wake modzikonda.

Ndipotu, Baibulo limalangizanso amuna kuti azikhala ndi akazi awo “mowadziwa bwino.” (1 Petulo 3:7) Izi sizimangotanthauza kudziwa chabe kuti zimene mkazi amafuna mwakuthupi ndiponso mwamaganizo n’zosiyana ndi zimene mwamuna amafuna. Koma mwamunayo ayenera kuzindikira bwinobwino zimene mkazi wake amafunikira.

‘Iye Ndiye Mnzanu’

Kodi mfundo yoti mkazi azigonjera mwamuna wake ikutanthauza kuti mkaziyo azingomvera zilizonse osanenapo maganizo ake? Taganizirani za Sara yemwe amatchulidwa m’Baibulo kuti ndi chitsanzo chabwino pankhani yomvera mwamuna wake Abulahamu. (1 Petulo 3:5, 6) Iye ankagonjera mwamuna wake pankhani zazikulu ndi zazing’ono zomwe. Mwachitsanzo, iye anasiya nyumba yake yabwino n’kuyamba moyo wosamukasamuka n’kumakhala m’mahema, komanso anavomera kukonzera alendo chakudya ngakhale kuti anauzidwa mwadzidzidzi. (Genesis 12:5-9; 18:6) Koma pankhani ina yaikulu, iye ananena mobwerezabwereza maganizo ake amene anali osiyana ndi a mwamuna wake. Iyi inali nthawi imene ankafuna kuti mdzakazi wake Hagara, pamodzi ndi mwana wake Ismayeli achoke pa nyumbapo. Mulungu sanadzudzule Sara, m’malo mwake anauza Abulahamu ‘kumvera mawu’ a mkazi wakeyo. Komabe, Sara anagonjerabe mwamuna wake chifukwa sanathamangitse yekha mdzakaziyo pamodzi ndi mwana wake, koma anadikira kuti Abulahamu achite zimenezi.—Genesis 21:8-14.

Zimene Sara anachitazi zikusonyeza kuti akazi asamangokhala chete koma azinena maganizo awo. Ndipo amuna aziona akazi awo kukhala ‘anzawo,’ ndiponso aziwapatsa ulemu. (Malaki 2:14) Monga anzawo, akazi angapereke maganizo othandiza pa nkhani zofunika m’banja ndipo alinso ndi udindo winawake m’banjamo. Iwo nthawi zambiri amasamalira ntchito zapakhomo ndiponso nkhani zina zokhudza ndalama. Komabe mwamuna monga mutu wa banja, ndi amene ali ndi udindo wosankha zochita zokhudza banjalo.—Miyambo 31:10-31; 1 Timoteyo 5:14.

Lemekezani Amene Anayambitsa Banja

Yehova Mulungu analenga mwamuna ndi mkazi ndipo anayambitsa banja lomwe ndi mgwirizano wopatulika. (Genesis 2:18-24) Ndipo aliyense anam’patsa udindo wakewake umene umathandiza banjalo kukhala losangalala kwambiri.—Deuteronomo 24:5; Miyambo 5:18.

Popeza Yehova ndiye anayambitsa banja, iye ndi woyenera kupereka malamulo oyendetsera banjalo. Mulungu amadalitsa ndi kuthandiza anthu okwatirana amene amasamalira bwino udindo wawo ndiponso amatsatira malangizo ake okhudza umutu. Makamaka ngati akuchita zimenezi osangoti chifukwa choti malangizowo ndi othandiza koma chifukwa cholemekeza ulamuliro wa Mulungu.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

▪ Kodi ndani amene anasonyeza chitsanzo chabwino kwambiri pankhani ya umutu?— Aefeso 5:25.

▪ Kodi Mulungu wapatsa mwamuna ulamuliro wopanda malire?—1 Akorinto 11:3.

▪ Kodi cholinga cha banja ndiponso umutu n’chiyani?—Miyambo 5:18.

[Chithunzi patsamba 28]

Anthu okwatirana amakhala ndi chimwemwe mwamuna akamachita umutu wake motsatira chitsanzo cha Khristu