Kulimbana ndi Matenda a Asperger
Kulimbana ndi Matenda a Asperger
YOLEMBEDWA KU BRITAIN
MUMAFUNA kukhala ndi anzanu koma kucheza ndi anthu kumakuvutani. Ngakhale zili choncho, mumatha kulankhula kwa maola ndithu pa zinthu zomwe mumakonda. Mumachita zinthu m’njira imene munazolowera ndipo zikasintha, mumasokonekera. Nthawi zambiri mumakhala ndi nkhawa, pena kukwiya, penanso kukhumudwa.
Anthu sakumvetsani. Amakudabwani, amati ndinu wovuta kapena wamwano kumene. Inunso zimakuvutani kumvetsa maganizo a anthu ena ndi mmene amamvera, makamaka chifukwa chakuti simutha kuzindikira kuti mmene nkhope yawo ilili, kapena mmene akuchitira ndi thupi lawo, akufuna chiyani. Anthu ambiri amene ali ndi matenda a Asperger amakumana ndi mavuto ngati amenewa.
Anthuwa saoneka mosiyana ndi wina aliyense, ndipo ambiri amakhala anzeru kwambiri. Komabe, amakhala ndi vuto linalake la muubongo limene limawalepheretsa kumvana ndi anthu ena. Matendawa ali ndi zizindikiro zosiyanasiyana, ndipo munthu aliyense amakhudzidwa mosiyanasiyananso. Ngakhale zili choncho, n’zotheka kulimbana ndi matenda a Asperger. Tamvani nkhani ya Claire.
Patapita Nthawi, Matenda Ake Anadziwika
Ali mwana, Claire anali waphee ndipo sankakonda kucheza ndi anthu. Ankapewa kuyang’anizana ndi anthu maso ndi maso ndipo ankachita mantha ndi gulu la anthu. Anaphunzira kulankhula ali wamng’ono kwambiri, koma ankalankhula mawu ochepa chabe ndiponso popanda kusintha mphamvu ya mawu. Ankachita zinthu m’njira yakeyake ndipo sankafuna kusintha. Zikasintha, ankada nkhawa.
Kusukulu, aphunzitsi sankamukomera mtima chifukwa iwo ankaganiza kuti Claire anangofuna kukhala wovuta ndipo ana ena a sukulu ankamuchitira nkhanza. Mayi ake nawonso ankavutika chifukwa anthu ena ankangothamangira kunena kuti sanamulere bwino Claire. Mapeto ake, zaka zomalizira za maphunziro ake, mayiwo anaganiza zongophunzitsira Claire kunyumba.
Kenako, Claire analowa ntchito zosiyanasiyana koma zonse zinatha. Chifukwa chake chinali chakuti zinthu zikasintha, ankavutika kuzolowera ndiponso zinkamuvuta kuchita zimene ena ankafuna kuti iye azichita. Ali pa ntchito yake yomaliza, imene ankagwira ku nyumba yosungirako okalamba ndi odwala, mayi wina yemwe anali mkulu wakumeneko anazindikira kuti Claire ali ndi vuto linalake lalikulu. Pamapeto pake ali ndi zaka 16, Claire anapezeka ndi matenda a Asperger.
Apa tsopano, m’pamene mayi a Claire anadziwa chifukwa chimene iye ankachitira zinthu zosiyana ndi anthu ena. Mnzawo wina anapeza mabuku ofotokoza za matendawa, ndipo Claire atawawerenga, anadabwa kuti: “Kodi ine ndimachitadi zimenezi? Kodi ndi mmene ndilili?” Dipatimenti ya boma yothandiza
anthu inamulangiza Claire kuti ndi bwino kuti iye azigwira ntchito inayake imene ingamuthandize pa matenda akewo. Chris, wa Mboni za Yehova, yemwe amadziwa kwambiri kuthandiza ana okhala ndi mavuto apadera, anakonza zakuti Claire, yemwenso ndi wa Mboni, azikagwira nawo ntchito yosamalira nyumba imene Mboni zimapembedzeramo.Kuphunzira Kukhala Bwino ndi Anthu
Poyamba, Claire zinkamuvuta kulankhula ndi anzake amene ankagwira nawo ntchito. Akakumana ndi vuto, ankalemba kakalata n’kumupatsa Chris, ndipo zimenezi zinali zosavuta kwa iye kusiyana ndi kunena maganizo ake. Pang’onopang’ono, Chris anamulimbikitsa kuti azikhala naye pansi n’kumakambirana bwinobwino. Chris anati, moleza mtima anaphunzitsa Claire kukhala bwino ndi anthu. Anamufotokozera kuti zimene amachitazo, zopewa anthu ndi kumangochita zimene akufuna, sikukhala bwino ndi anthu. Claire atathandizidwa, anayamba kugwirizana ndi anzake pogwira ntchito.
Chifukwa cha zovuta zimene anakumana nazo m’mbuyomo, Claire anali kudzikayikira. Choncho, akapemphedwa kugwira ntchito inayake, ankangofulumira kuyankha kuti: “Sindingakwanitse.” Kodi Chris anamuthandiza bwanji pa vuto limeneli? Ankamupatsa kantchito kakang’ono ndi kumuuza kuti, “Timatere,” kenako n’kuwonjezera kuti, “Ungathe kugwira ntchitoyi.” Ndipo Claire akamaliza kugwira ntchitoyo, ankasangalala. Chris ankamuyamikira kwambiri n’kumupatsanso ntchito ina. Claire ankavutika kukumbukira akapatsidwa malangizo ambiri ongonena ndi pakamwa, koma akamulembera sizinkamuvuta kutsatira. Pang’ono ndi pang’ono, anasiya kudzikayikira.
Popeza kuti Claire ankadana ndi gulu la anthu, zinali kumuvuta kwambiri kulankhula ndi ena amene abwera kudzapembedza pamisonkhano yachikhristu. Akabwera ku Nyumba ya Ufumu, ankakonda kukhala yekhayekha mpando wakutsogolo. Komabe anakonza zakuti misonkhano ikangotha, azipita mwamsanga kumbuyo kukalankhula ndi munthu mmodzi.
Patapita nthawi, Claire anapezeka kuti wayamba kulankhula ndi anthu ambiri. “Koma ndi zovutabe,” iye akutero. Ngakhale kuti amavutika kwambiri kucheza ndi anthu chifukwa cha matenda akewa, iye amakamba nkhani mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Pulogalamu imeneyi cholinga chake ndi kuthandiza Mboni za Yehova zonse kudziwa kulankhula bwino.
Kugonjetsa Vuto Lalikulu
Claire atayamba kulimba mtima kwambiri, Chris anamuuza kuti ayese kukhala mpainiya wothandiza, dzina limene Mboni za Yehova zimatchulira Mboni zobatizidwa zimene mwezi uliwonse zimathera maola 50 kapena kuposa zikuuza
ena mfundo za m’Baibulo zimene zimakhulupirira. Claire anayankha kuti: “Sindingakwanitse zimenezo.”Koma Chris anamulimbikitsa pomuuza kuti ngakhale asakwanitse maola 50 mwezi umenewo, Claire angasangalalebe kudziwa kuti anayesetsa. Chotero, iye anayesa kuchita zimenezo ndipo anasangalala kwambiri. Kenako anachitanso zimenezo maulendo angapo, ndipo chisangalalo chake chinawonjezereka. Zimenezi zinamulimbitsa mtima, makamaka atapeza anthu ambiri amene anali kufuna kudziwa zambiri za m’Baibulo.
Kumisonkhano yachikhristu, Claire anamva nkhani imene inamukhudza kwambiri. Nkhaniyi inamulimbikitsa kuona ngati pali chimene chikumuletsa kukhala mpainiya wokhazikika, kapena kuti mlaliki wanthawi zonse. Choncho, iye anakhala mpainiya wokhazikika. Zotsatira zake? Claire mwini wakeyo akuti: “Ntchitoyi ndi yabwino kwambiri.” Panopa akugwirizana kwambiri ndi anthu mumpingo wawo ndipo ali ndi mabwenzi ambiri. Ana amakonda kucheza naye ndipo iye amawathandiza akamalalikira limodzi.
Anthu Ena Angathandize
N’zoona kuti sikuti aliyense amene ali ndi matenda a Asperger angakhale mlaliki wanthawi zonse. Koma nkhani ya Claire ndi umboni wakuti anthu oterewa angachite zambiri kuposa zimene angaganize. Popeza kuti matenda akewa safuna kuti azisinthasintha zochita, pulogalamu yake yolalikira ndi imene imamuthandiza. Ndiponso khama ndi kudalirika kwake, zimamuthandiza kuchita bwino ntchito yakeyi.
Claire amaona kuti ndi bwino kuti anthu azidziwa kuti iye ali ndi matenda a Asperger, kuti azizindikira chifukwa chake iye amachita zinthu mosiyana ndi ena komanso mmene amavutikira. Iye akuti: “Popeza umalephera kufotokoza bwino maganizo ako, anthu amakuona ngati umaganiza moperewera.” Kukhala ndi munthu wina amene amakumvetsa n’kothandiza.
Kwa anthu amene ali ndi matenda ngati amenewa, Chris ndi Claire akupereka malingaliro akuti ndi bwino kukhala ndi zolinga zing’onozing’ono, kuchita zinthu zochepa panthawi imodzi. Zimakhala bwino kuthandizidwa ndi munthu amene amamvetsa matenda akowo. Zikatere, munthu amayamba kudziona kuti ndi wofunika ndipo amagonjetsa mavuto ake.
Nkhani ya Claire ikusonyeza kuti kuleza mtima ndi chilimbikitso, zingathandize kwambiri anthu amene ali ndi matenda a Asperger. Claire akuvomereza mfundo imeneyi kuti: “Zaka zochepa zapitazo, sindikanaganiza n’komwe kuti ndingachite zinthu zonse zimene ndikuchita panopa.”
[Mawu Otsindika patsamba 24]
Claire amaona kuti ndi bwino kuti anthu azidziwa kuti iye ali ndi matenda a Asperger
[Bokosi patsamba 22]
MATENDA A ASPERGER
Dzina la matendawa linachokera kwa Dr. Hans Asperger, amene anafotokoza za matendawa koyamba mu 1944. Koma ndi zaka zaposachedwapa pamene akatswiri afufuza kwambiri za matendawa, kuti azimvetsa ndi kuthandiza anthu amene akupezeka nawo. Akatswiri ofufuza za matenda sakudziwa ngati vutoli ndi mtundu wochepa mphamvu wa matenda a autism kapena ngati ndi matenda ena. Mpaka pano, palibe amene akudziwa chimene chimayambitsa matenda a Asperger. Koma si chifukwa cha kusowa chikondi kapena mmene mwana analeredwera.
[Bokosi patsamba 24]
KUTHANDIZA AMENE ALI NDI MATENDA A ASPERGER
Yesetsani kudziwa ndiponso kukonda anthu amene ali ndi matendawa. Ngakhale kuti iwo amavutika kulankhula ndi anthu, dziwani kuti anthu amenewa amafuna ndipo amafunikira mabwenzi. Si cholinga chawo kuti akhale ovuta kapena kuti azichita zinthu zachilendo.
Khalani oleza mtima ndipo yesetsani kumvetsa mavuto awo. Komanso, dziwani kuti mufunika kumafotokoza zinthu bwinobwino m’njira yosavuta kumva. Izi zili choncho chifukwa chakuti iwo angachite zimene inu simukutanthauza. Mukafuna kusintha njira yochitira zinthu, afotokozereni momveka bwino, mwina mpaka kuwasonyeza mmene angachitire chinthu chatsopanocho.
Mukaona kuti akuda nkhawa kwambiri chifukwa cha zinthu zimene aona kapena kumva, alimbikitseni kuchita zinthu zina monga kuyang’ana chithunzi chokongola kapena kumvetsera nyimbo zotsitsimula moyo.
[Chithunzi patsamba 23]
Claire anaphunzira kuyamba iyeyo kucheza ndi ena
[Chithunzi patsamba 23]
Chris akufotokozera Claire zomwe zingamuthandize kugwirizana ndi anzake pogwira ntchito