Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ana Akamagwiritsa Ntchito Intaneti Zimene Makolo Ayenera Kudziwa

Ana Akamagwiritsa Ntchito Intaneti Zimene Makolo Ayenera Kudziwa

Ana Akamagwiritsa Ntchito Intaneti Zimene Makolo Ayenera Kudziwa

KWA nthawi yaitali, zinkaoneka kuti kuteteza ana ku mavuto a pa Intaneti kumadalira malo amene mungaike kompyuta. Anthu ankaganiza kuti kuika kompyuta pamalo oonekera kungathandize kuti ana asamagwiritse ntchito Intaneti molakwika. N’zoona kuti kusaika kompyuta m’zipinda za ana n’kothandiza, koma sikokwanira poteteza anawo. Masiku ano zipangizo zoyenda nazo zimathandiza ana kugwiritsa ntchito Intaneti kulikonse kumene angapite. Ngakhale foni zam’manja zambiri zili ndi Intaneti. Komanso pali malo monga malaibulale, nyumba za anzawo ndi malo ena olipiritsa kumene ana angagwiritse ntchito Intaneti. Pokhala ndi njira zambiri zimenezi, n’zovuta kuti makolo adziwe zimene ana awo akuchita pa Intaneti.

Nazi zinthu zina pa Intaneti zimene ana amakopeka nazo ndiponso mavuto ake.

IMELO

Kodi n’chiyani? Mauthenga amene amalembedwa ndi kutumizidwa pakompyuta.

N’chifukwa chiyani ana amawakonda? Imelo ndi njira yachangu ndi yotchipa yolankhulira ndi mabwenzi komanso achibale.

Zimene muyenera kudziwa. Munthu amatha kulandira maimelo kuchokera kwa anthu osawadziwa. Maimelo amenewa, omwe amatchedwanso spam, amasowetsa mtendere ndiponso amakhala ndi zoipa kapena zolaula. Zina zimene zimaikidwamo zingachititse amene akugwiritsa ntchito Intaneti, kuphatikizapo mwana yemwe sayembekeza kuti angalowe m’mavuto, kuulula za iyeyo, ndipo akatero ena angamubere zolembedwa pa chitupa chake. Kuyankha maimelo oterowo, ngakhale kungonena kuti asiye kutumiza, kungachititse otumizawo kudziwa kuti adiresi ya imeloyo ndi yokhazikika, ndipo angamatumizebe maimelo oterowo ambirimbiri.

WEBU SAITI

Kodi n’chiyani? Masamba a pa Intaneti omwe amapangidwa ndi kuwonjezeredwa ndi mabungwe, sukulu zosiyanasiyana, a zamalonda, ndi anthu wamba.

N’chifukwa chiyani ana amawakonda? Pali masamba ambirimbiri amene amapereka mwayi kwa ana wogula zimene akufuna, kufufuza zinthu, kucheza ndi anzawo ndiponso kusewera ndi kukopera magemu kapena nyimbo.

Zimene muyenera kudziwa. Anthu opanda khalidwe apezerapo mwayi pa masamba amenewa. Masamba ambiri amasonyeza anthu akugonana, ndipo n’zosavuta kwa munthu wosadziwa kutsegula masamba amenewa. Mwachitsanzo, ku United States, 90 peresenti ya ana azaka za pakati pa 8 ndi 16 ananena kuti mosadziwa anatsegula zithunzi zolaula pa Intaneti, ndipo nthawi zambiri zimenezi zinkachitika akufufuza za homuweki.

N’zosavutanso kupeza masamba amene amalimbikitsa ana kutchova juga. Ku Canada, pafupifupi mnyamata mmodzi pa anyamata anayi alionse a fomu 2 ndi 3 anavomera kuti anatsegulapo masamba amenewa, ndipo m’pake akatswiri kuda nkhawa chifukwa chakuti n’zosavuta kuti juga za pa Intaneti zimulowerere munthu. Ndiyeno palinso masamba amene amalimbikitsa atsikana kuti asamadye kwambiri kuti azikhala oonda. * Komanso, pali masamba ena amene amalimbikitsa anthu kudana ndi zipembedzo zazing’onozing’ono ndiponso mafuko a anthu ena. Masamba ena amaphunzitsa anthu kupanga mabomba, poizoni, ndi uchigawenga. Magemu a pa Intaneti amasonyeza ziwawa zoopsa monga anthu akukhapana.

TCHATI LUMU

Kodi n’chiyani? Malo ochezerapo a pa Intaneti amene anthu amatha kutumizirana mauthenga. Mauthengawa nthawi zambiri amakhudza nkhani inayake yochititsa chidwi.

N’chifukwa chiyani ana amawakonda? Mwana wanu angathe kulankhula ndi anthu ambiri amene sakuwadziwa koma omwe zokonda zawo n’zofanana ndi za mwana wanuyo.

Zimene muyenera kudziwa. Anthu ogona ana amakonda kugwiritsa ntchito malo amenewa n’cholinga chofuna kukopa ana kuti azigona nawo pa Intaneti pomwepo, ngakhale kupangana kuti akakumane ndi munthuyo ndi kukagonana. Taganizirani zimene zinachitika pamene mmodzi wa olemba buku lakuti What in the World Are Your Kids Doing Online? anali kufufuza za chitetezo cha pa Intaneti. Pakufufuzako, mayiyo ananamizira kuti ali ndi zaka 12. Bukuli linati: “Nthawi yomweyo, munthu wina anamuuza kuti achoke pa malo ochezera amene analipowo n’kupita malo achinsinsi. Mayiyu anamunamiza munthuyo kuti sakudziwa mmene angapitire kumeneku, ndipo mnzake watsopanoyu anamuthandiza mmene angachitire. Kenako munthuyo anafunsa mayiyu ngati akufuna kugonana [pa Intaneti pomwepo].”

INSITANTI MESEJI

Kodi n’chiyani? Kucheza kwa anthu awiri kapena kuposa kolemberana mawu pa Intaneti. Wolandirayo amaona zimene mnzakeyo akulemba nthawi yomweyo.

N’chifukwa chiyani ana amawakonda? Ndi njira imeneyi, munthu angathe kusankha amene akufuna kucheza nawo pa mndandanda wa mabwenzi ake umene amapanga. N’zosadabwitsa kuti pa kafukufuku amene anachitika ku Canada, anapeza kuti 84 peresenti ya achinyamata azaka 16 ndi 17 amacheza ndi anzawo mwanjira imeneyi ndipo amatero kupitirira ola limodzi patsiku.

Zimene muyenera kudziwa. Kucheza kumeneku kungasokoneze mwana wanu ngati akufunika kuwerenga kapena ngati akuchita zinthu zina zofuna kuikirapo mtima. Komanso, simungadziwe munthu amene mwana wanu akucheza naye. Ndipotu, simungamve zimene akukambirana.

BULOGI

Kodi n’chiyani? Madayale a pa Intaneti.

N’chifukwa chiyani ana amawakonda? Amapereka mwayi kwa achinyamata wolemba maganizo awo, zokonda zawo ndi zimene amachita. Ambiri amakhala ndi malo oti owerenga alembepo ndemanga zawo, ndipo ana ambiri amasangalala kudziwa kuti winawake wayankha zimene iwo analemba.

Zimene muyenera kudziwa. Munthu aliyense amatha kuwerenga madayalewa. Ana ena mosasamala amaulula zinthu zokhudza banja lawo, sukulu kapena kumene akukhala. Chinthu china ndi chakuti madayalewa angathe kuwononga mbiri ya munthu, kuphatikizapo mwiniwakeyo. Mwachitsanzo, olemba ntchito ena amafufuza dayale ya munthu amene akufunsira ntchito akamaganiza zomulemba ntchito.

ONILAINI SOSHO NETIWEKI

Kodi n’chiyani? Malo amene ana amatha kutsegula tsamba lawolawo ndi kuikapo zithunzi, mavidiyo ndi mabulogi.

N’chifukwa chiyani ana amawakonda? Kutsegula tsamba ndi kuikapo zimene akufuna kumam’thandiza mwana kuti ena amudziwe. Ana amatha kudziwana ndi anthu ambirimbiri.

Zimene muyenera kudziwa. Mtsikana wina, dzina lake Joanna, ananena kuti: “Malo amenewa ali ngati phwando la pa Intaneti. Pakhoza kutulukira anthu osawadziwa komanso oopsa.” Zinthu zokhudza inuyo zimene mungaike pa malowa zingagwiritsidwe ntchito molakwika ndi achinyamata komanso achikulire ena opanda khalidwe. M’pake kuti Parry Aftab, katswiri wa za chitetezo cha pa Intaneti, ananena kuti malo amenewa ali ngati “masitolo akuluakulu komwe anthu ogona ana amapitako.”

Ndiponso, ubwenzi wa pa Intaneti sukhala weniweni. Pamasamba amene iwo amakonza, ana ena amasonyeza kuti ali ndi mabwenzi ambirimbiri koma omwe sanaonanepo n’komwe, ndipo amachita zimenezi kungofuna kuti aoneke ngati otchuka kwa anthu amene amawerenga masamba awo. M’buku lake lakuti Generation MySpace, Candice Kelsey analemba kuti: “Zimene zikuchitika n’zakuti ana amaganiza kuti munthu akakhala wodziwika kwambiri, ndiye wofunika kukhala bwenzi lako.” Iye anawonjezeranso kuti: “Kuona kuti munthu ndi wofunika malinga ndi kuchuluka kwa anthu omudziwa kumachititsa ana athu kukhala ngati katundu, ndipo iwo amakakamizika kuchita chilichonse kuti akhale ndi mabwenzi ambiri.” Motero m’pomveka kuti buku la What in the World Are Your Kids Doing Online? limafunsa funso lakuti: “Kodi munthu angawauze bwanji ana kuti afunika kukhala oganizira ena ndi achifundo pamene Intaneti ikuwalola kukhala ndi mabwenzi kenako n’kuwanyanyala?”

Zinthu 6 zimenezi ndi zina mwa zinthu zimene ana amakopeka nazo pa Intaneti masiku ano. Ngati ndinu kholo, kodi mungatani kuti muteteze ana anu?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 12 Ambiri mwa masamba amenewa ndiponso mabungwe ambiri amanena kuti salimbikitsa atsikana kuti asamadye kwambiri kuti azikhala oonda. Koma ena amasonyeza kuti moyo umenewu si vuto ndipo munthu amachita kusankha yekha. Mafomu opezeka pamasamba amenewa amafotokoza mmene munthu angabisire kwa makolo ake kulemera kwake kwenikweni komanso vuto lake la kadyedwe.

[Mawu Otsindika patsamba 4]

Ku India, chiwerengero cha anthu ogwiritsa ntchito Intaneti chinakwera ndi 54 peresenti chaka china, makamaka chifukwa cha ana

[Mawu Otsindika patsamba 7]

“Kholo lingaganize kuti kamera ya pakompyuta ndi njira yosavuta komanso yotchipa kuti mwana azilankhula ndi anzake kapena achibale, koma pamene kwa munthu wogona ana umakhala mwayi woonera m’chipinda cha mwanayo.”​—Robert S. Mueller III, director of the Federal Bureau of Investigation