Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Maganizo a Mulungu Ndi Otani pa Zinthu Zothandiza Popemphera?

Kodi Maganizo a Mulungu Ndi Otani pa Zinthu Zothandiza Popemphera?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Maganizo a Mulungu Ndi Otani pa Zinthu Zothandiza Popemphera?

Kugwiritsa ntchito zinthu zothandiza popemphera n’kofala kwambiri m’zipembedzo za Chibuda, Chihindu, Chisilamu, Chiyuda, Chikatolika ndi Tchalitchi cha Eastern Orthodoxy. Choncho anthu ambiri, pafupifupi m’mayiko onse, amakhulupirira kuti zinthu zimenezi zimawathandiza popemphera kwa Mulungu ndiponso kuti iye aziwakonda ndi kuwadalitsa. Koma kodi Baibulo limaphunzitsa chiyani pankhani imeneyi?

KUGWIRITSA ntchito zinthu zothandiza popemphera kunayamba kale kwambiri. Mwachitsanzo, pamene panali mzinda wakale wa Nineve, akatswiri ofukula za m’mabwinja anapezapo chosema cha “anthu awiri aakazi okhala ndi mapiko akupemphera pa mtengo wopatulika; . . . atanyamula kolona [kudzanja] lamanzere.”—The Catholic Encyclopedia.

Kodi ntchito ya kolona n’chiyani? Buku lomwe taligwira mawu pamwambapa linati: “Nthawi zonse ngati pemphero likufunika kulibwereza maulendo ambiri, anthu amapeza chipangizo china kuti chiziwathandiza kuwerenga maulendo omwe abwereza pempherolo m’malo mogwiritsa ntchito zala zawo.”

Mapemphero olembedwa pa mawilo amapangitsa kubwereza mapemphero kukhala kosavuta. Wilo limeneli akalizunguliza kamodzi kaya ndi dzanja, mphepo, madzi kapena magetsi, amaona kuti n’chimodzimodzi ndi kupemphera. Nthawi zambiri mawilo olembedwapo mapemphero amawagwiritsa ntchito limodzi ndi mawu enaake opatulika. Onani mmene Mulungu amaonera zinthu zimenezi.

‘Musanene Zinthu Mobwerezabwereza’

Yesu Khristu amene amadziwika ndi anthu ambiri, ngakhale omwe si Akhristu, kuti anali mneneri wa Mulungu, anafotokoza maganizo a Mlengi pankhani yopemphera mobwerezabwereza. Iye anati: “Popemphera, usanene zinthu mobwerezabwereza, muja amachitira amitundu, chifukwa iwo amaganiza kuti akanena mawu ambirimbiri awamvera.” *Mateyo 6:7.

Motero, ngati Mulungu amaletsa ‘kunena zinthu mobwerezabwereza,’ kodi iye angavomereze zinthu zimene anthu amagwiritsa ntchito popemphera mobwerezabwereza? Ndipotu Baibulo silitchula mtumiki aliyense wokhulupirika wa Mulungu amene anagwiritsapo ntchito kolona, mapemphero olembedwa pa mawilo, kapena zinthu zina popemphera. Zifukwa zimene Mulungu savomerezera mapemphero oterewa tingazidziwe bwino kwambiri tikamvetsa tanthauzo komanso cholinga cha pemphero.

Mapemphero Amene Mulungu Amavomereza

Mu pemphero la Ambuye, Yesu anatchula Mulungu kuti “Atate Wathu.” Choncho, Mlengi wathu si wopanda chikondi komanso si mphamvu inayake yosadziwika bwino imene imasangalala ndi mawu amatsenga, miyambo inayake kapena mawu ena opatulika. M’malo mwake, Iye ndi Atate wachikondi amene amafuna kuti tiziona kuti amatikonda ndipo ifenso tizimukonda. Yesu anati: “Ndimakonda Atate.” (Yohane 14:31) Kalekalelo mneneri wina ku Isiraeli anati: “Yehova, Inu ndinu Atate wathu.”—Yesaya 64:8.

Kodi tingayandikire bwanji kwa Atate wathu wa kumwamba Yehova? (Yakobe 4:8) Monga mmene zilili ndi ubwenzi uliwonse, timayandikira kwa Mulungu mwa kulankhula naye. Mulungu “amalankhula” nafe kudzera m’Baibulo, lomwe ndi Mawu ake. Ndipo m’buku limeneli amafotokoza ntchito zake, makhalidwe ake ndiponso zimene akufuna kutichitira. (2 Timoteyo 3:16) Ifenso timalankhula ndi Mulungu kudzera m’pemphero. Ndipo mapemphero amenewa ayenera kukhala ochokera pansi pa mtima ndiponso azisonyeza kuti tili naye paubwenzi wabwino. Sayenera kukhala mapemphero amwambo.

Taganizirani izi: M’banja losangalala ndiponso lachikondi, kodi ana abwinobwino ndiponso anzeru zawo amatani akamalankhula ndi makolo awo? Kodi amagwiritsa ntchito mawu amodzimodzi mobwerezabwereza ndipo mwina kufika pogwiritsa ntchito chipangizo china kuti chiziwathandiza kuwerenga maulendo omwe abwereza mawuwo? N’zoonekeratu kuti sachita zimenezi. M’malo mwake, amalankhula momveka bwino ndi mwaulemu komanso mochokera pansi pa mtima.

Tiyeneranso kuchita chimodzimodzi tikamapemphera kwa Mulungu. Tingamuuze chilichonse chimene chikutidetsa nkhawa. Lemba la Afilipi 4:6, 7 limati: “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, limodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatero, mtendere wa Mulungu . . . udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu.” N’zodziwikiratu kuti ngati pali nkhani inayake imene ikutidetsa nkhawa, timapempherera nkhaniyo nthawi zambiri. Koma zimenezi n’zosiyana ndi kubwereza mawu omweomwewo nthawi zonse.— Mateyo 7:7-11.

M’Baibulo muli zitsanzo zambiri za mapemphero amene Mulungu amavomereza. Ena mwa mapemphero amenewa ndi masalmo komanso mapemphero a Yesu. * (Salmo 17 ndi 86, timawu tapamwamba; Luka 10:21, 22; 22:40-44) Limodzi mwa mapemphero a Yesu amenewa lili m’chaputala 17 cha buku la Yohane. Pezani kanthawi kuti muwerenge pemphero limeneli. Pamene mukuwerenga, onani mmene Yesu anafotokozera kwa Mulungu zimene zinali mu mtima mwake. Onaninso mmene anasonyezera kuti sanali wodzikonda koma kuti ankakonda kwambiri ophunzira ake. Iye anapempha “Atate Woyera” kuti ‘awayang’anire kuopera woipayo,’ Satana.—Yohane 17:11, 15.

Kodi inuyo mumaona kuti mawu a m’pemphero la Yesu ndi amwambo kapena ongoloweza? Ayi ndithu. Chimenechi ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa ife. Anthu onse amene akufuna kuyandikira kwa Mulungu woona ayenera kumudziwa bwino kwambiri. Ndiyeno, chifukwa cha zimene akudziwazo amamukonda ndipo amapewa miyambo ya chipembedzo imene Mulungu amadana nayo. Kwa anthu otero Yehova amati: “Ndidzakhala atate kwa inu, ndipo inu mudzakhala ana anga aamuna ndi aakazi.”—2 Akorinto 6:17, 18.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 M’pemphero la Ambuye, Yesu sananene kuti: “Choncho inu muzipemphera pemphero ili,” zimene zikanatsutsana ndi zomwe anali atangonena kumene. M’malo mwake iye anati: “Choncho inu muzipemphera motere.” (Mateyo 6:9-13) Kodi ankafuna kutiphunzitsa chiyani pamenepa? Malinga ndi zimene pemphero la Ambuye likusonyeza, tikamapemphera tiyenera kuganizira kwambiri zinthu zauzimu kuposa zofunika pamoyo wathu.

^ ndime 15 Ngakhale kuti anthu ankaimba masalmo pazochitika zosiyanasiyana, sanali kuwabwerezabwereza ngati mmene anthu amachitira ndi kolona kapena ndi mapemphero olembedwa pa mawilo.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

▪ Kodi mawu a Yesu oletsa mapemphero obwerezabwereza akukhudzanso kolona ndi mapemphero olembedwa pa mawilo?—Mateyo 6:7.

▪ Kodi mapemphero athu azisonyeza kuti timamuona bwanji Mulungu?—Yesaya 64:8.

▪ Kodi Mulungu adzationa bwanji tikamapewa kupembedza konyenga?—2 Akorinto 6:17, 18.