Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Sitima Yopanda Mateyala

Sitima Yopanda Mateyala

Sitima Yopanda Mateyala

YOLEMBEDWA KU HONG KONG

ANTHU akaona sitima imeneyi ku Shanghai, m’dziko la China, ngakhale asanakwere amadziwa kuti imeneyi si sitima wamba. Sitimayi ikangonyamuka pa siteshoni, anthu amagoma nayo chifukwa imathamanga kwambiri. Imathamanga makilomita 430 pa ola limodzi moti ndi sitima yotenga anthu yothamanga kwambiri padziko lonse. Mphindi 8 zokha, sitima imeneyi imayenda mtunda wa makilomita 30 kukafika ku bwalo la ndege la ku Pudong. Komanso chinthu china chapadera ndi sitima imeneyi n’chakuti ilibe mateyala.

Padziko lonse lapansi, ndi kuno kokha kumene sitima za mtundu umenewu zimanyamula anthu. Sitimazi zimayenda pakati pa mzinda wa Shanghai ndi Pudong. Sitimayi sikhala ndi woyendetsa komanso siiyendera mateyala achitsulo koma imayendera mphamvu ya maginito. Ili ndi kompyuta imene imasonyeza malo amene yafika ndipo imatumiza mauthenga amenewa ku siteshoni za sitimazi. Kumeneko kumakhala anthu amene amaona kayendedwe ka sitimayi pogwiritsa ntchito makompyuta.

Kusiyana kwa Sitimayi ndi Sitima Wamba

Popanga sitima yapadera imeneyi ndi njanji yake panali mavuto ambiri. Mwachitsanzo, pakati pasitimayo ndi njanji yake pamakhala mpata waung’ono kwambiri. Choncho, popeza nthaka ya ku Shanghai ndi yofewa kwambiri, njanji ya sitimayi anaikonza moti azitha kuitukula ngati nthaka italowa pansi pang’ono. Anachitanso zimenezi poganizira kuti zipilala za konkire za njanjiyi zimatha kusintha malinga ndi mmene kunja kwatenthera.

Komabe, sitima imeneyi ndi yabwino m’njira zambiri. Mwachitsanzo, siichita phokoso komanso siitulutsa utsi. Sitimayi ndi njanji yake sizifunika kukonza pafupipafupi. Ndalama zimene amagwiritsira ntchito ponyamula anthu m’sitimayi n’zochepa kwambiri. Mwachitsanzo, poyerekezera ndi sitima imeneyi, galimoto imawononga ndalama zowirikiza katatu ndipo ndege kasanu. Komanso, sitimayi imayendera magetsi ochepa kwambiri poyerekezera ndi magetsi a makina otenthetsa kapena oziziritsa m’sitimamo. Chinanso n’chakuti poyerekeza ndi sitima wamba, sitimayi siivutika kukwera zitunda zazitali kapena kudutsa m’makona. Zimenezi zimathandiza kuti pomanga njanji yake pasafunike kusintha kwambiri malo achilengedwe.

Tikaona ubwino wa sitimayi, tingadabwe kuti n’chifukwa chiyani palibe njanji zambiri za sitimayi. Chifukwa chimodzi n’chakuti zimafuna ndalama zambiri kuti zimangidwe. Mwachitsanzo, akuluakulu a boma ku China asiya kaye zomanga njanji pakati pa Shanghai ndi Beijing. Achita izi chifukwa kuti amange njanji imeneyi, angafunike kuwononga ndalama zokwanira kumanga njanji ziwiri za sitima wamba. Komanso njanjizi sizingalumikizidwe ndi njanji za sitima wamba.

Kuti apange njanji ya sitima yoyendera maginito mu mzinda wa Shanghai anatengera luso la ku Germany. Akatswiri a ku Germany, Japan ndiponso m’mayiko ena akufufuzabe zambiri za sitima imeneyi. Mu December 2003, ku Japan ankayesa sitima ina yotereyi ndipo inathamanga kwambiri liwiro la makilomita 581 pa ola limodzi, ndipo palibe sitima iliyonse imene inathamangapo chonchi. Komabe mpaka panopa, sitima ya ku Shanghai ndi sitima yokhayi ya mtundu umenewu imene imanyamula anthu.

Sitimayi ikangonyamuka ku Pudong popita ku Shanghai, anthu amangokhalira kuyang’ana chipangizo chosonyeza liwiro, kuti aone liwiro limene sitimayi ilekezere. Chifukwa cha liwiro lake, paulendo woyamba anthu saona zambiri, moti amadzaikweranso. Munthu akakwera sitimayi amamvetsa chifukwa chimene anaipatsira dzina lakuti “ndege yopanda mapiko.”

[Bokosi/Zithunzi patsamba 24]

KODI SITIMAYI IMAYENDA BWANJI?

Maginito oyendera magetsi (1) amene ali kunsi kwa bogi iliyonse, amakankhana ndi maginito amene ali kunsi kwa njanji ya sitimayo (2), ndipo zimene zimachititsa kuti sitimayo ikwere m’mwamba. Maginito ena (3) amathandiza sitimayo kuti isapendekeke. Palinso maginito ena (4) mu njanji amene amakankhira sitimayo kutsogolo.

Poti njanjizi zimayendera magetsi, a ku siteshoni ya sitimayi amangoyatsa malo amene (5) sitimayo ikudutsapo basi. Sitimayi ikamathamanga kapena ikamakwera chitunda, mphamvu ya magetsiyi amaichulutsanso kwambiri. Ngati akufuna kuti sitimayi ichepetse liwiro kapena ibwerere m’mbuyo, amangotembenuza kayendedwe ka mphamvu ya maginito a m’njanji ija.

KODI SI YOIKA MOYO PACHISWE?

Ngakhale kuti sitimayi imathamanga kwambiri, ili ndi zitsulo kunsi kwake (6) zimene zimagwira njanji, moti n’zovuta kwambiri kuti sitimayo isiye njanji. Okwera sitimayi safunika kumanga malamba ndipo amatha kuyendayenda m’sitimamo ngakhale ikuthamanga kwambiri. Ngati magetsi azima, sitimayi ili ndi zoimitsira zapadera zoyendera mabatire, zimene zimapangitsa kuti ichepetse liwiro n’kufika pa mtunda wa makilomita 10 pa ola limodzi ndipo kenako imaimiratu.

Kodi mphamvu ya maginito ya sitimayi ingavulaze anthu ena, monga amene kuchipatala anawaika kachitsulo mu mtima mwawo? Zimene ofufuza apeza zasonyeza kuti mphamvu imeneyi siingawavulaze. Ndipotu mkati mwa sitimayi, mphamvu ya maginito ndi yochepa kwambiri poyerekezera ndi ya sitima wamba.

[Zithunzi pamasamba 24, 25]

Imathamanga makilomita oposa 426 pa ola limodzi!

[Mawu a Chithunzi patsamba 24]

Masamba 24 ndi 25: All photos and diagrams: © Fritz Stoiber Productions/Courtesy Transrapid International GmbH & Co. KG