Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’zotheka Ndithu Kuchepetsa Vuto la Kuiwala

N’zotheka Ndithu Kuchepetsa Vuto la Kuiwala

N’zotheka Ndithu Kuchepetsa Vuto la Kuiwala

“Kukumbukira zinthu kumathandiza kwambiri pamoyo wathu. Popanda kukumbukira zinthu, m’povuta kudziwa zimene zikuchitika ndipo tsiku lililonse tikadziyang’ana pa kalilole tingamadzidabwe tokha. Sitingathe kugwirizanitsa zinthu zimene zikuchitika tsiku lililonse, sitingaphunzirepo kanthu pa zimene zinachitika kale ndipo sitingathe kuganiza zam’tsogolo.”—LINATERO BUKU LAKUTI “MYSTERIES OF THE MIND.”

MBALAME zina zimakumbukira bwinobwino malo amene zinasunga zakudya zawo ngakhale patapita miyezi ingapo. Agologolo nawonso amadziwa pamene anakwirira mtedza wawo. Koma n’chifukwa chiyani anthufe timaiwala pamene tasiya makiyi athu mwina patangopita ola limodzi? Ambirife timadandaula kuti timaiwalaiwala. Komatu ngakhale kuti kuiwala kulibe mankhwala, ubongo wathu ungathe kuphunzira zinthu zambirimbiri n’kumazikumbukira bwinobwino. Chofunika ndi kungougwiritsa ntchito mokwanira.

Ubongo Wathu Ungathe Kuchita Zambiri

Ubongo wa munthu umalemera pafupifupi kilogalamu imodzi ndi theka ndipo ndi waukulu ngati nyumwa. Koma uli ndi timinyewa toposa 100 biliyoni tomwe tinalumikizana m’njira yodabwitsa kwambiri. Mnyewa umodzi umalumikizana ndi ina yokwana pafupifupi 100,000. Kulumikizana kumeneku kumathandiza kuti ubongo uphunzire zinthu zambiri ndi kuzisunga. Koma chimene chimavuta ndi kukumbukira zinthuzo. Pali anthu ambiri amene amakumbukira kwambiri zinthu ngakhale amene sanapite ku sukulu.

Mwachitsanzo, kumadzulo kwa Africa kuli akatswiri ena odziwa kukumbukira nkhani zimene zinachitika kalekale amene amatha kukumbukira mayina a makolo awo akale kwambiri ngakhale kuti sadziwa n’komwe kuwerenga. Anthu amenewa anathandiza wolemba mabuku wina wa ku America dzina lake Alex Haley. Munthuyu anapatsidwa mphoto yapamwamba chifukwa cholemba buku (lotchedwa Roots) lofotokoza mbiri ya makolo ake ku Gambia. M’bukuli iye analembamo za mibadwo 6 ya makolo ake. Haley anati: “Ndikuthokoza kwambiri akatswiri a ku Africa amenewa. Mpake kuti masiku ano mmodzi wa anthu amenewa akamwalira zimakhala ngati kuti laibulale yathunthu yapsa.”

Taganiziraninso za munthu wina wotchuka wa ku Italy, dzina lake Arturo Toscanini. Iyeyu anali wotsogolera nyimbo. Anthu anadziwa kuti iye ali ndi luso atamuitana kuti adzalowe m’malo mwa wotsogolera wina ndipo apa n’kuti ali ndi zaka 19. Ngakhale kuti anali ndi vuto la maso iye anatsogolera bwinobwino nyimbo ya zisudzo yotchedwa Aida popanda kuonera paliponse.

Luso ngati limeneli n’logometsa kwambiri. Komatu mfundo imene ambirife sitidziwa ndi yakuti tingathe kukumbukira kwambiri zinthu. Kodi inuyo mukufuna kuchepetsa vuto loiwalaiwala zinthu?

Mmene Mungachepetsere Vutoli

Kuti munthu akumbukire zinthu, pali zinthu zitatu zimene zimafunika. Choyamba ndi kulowetsa zinthu mu ubongo, chachiwiri kuzisunga ndipo chachitatu ndi kukumbukira zinthuzo panthawi imene zikufunikira. Mukaona chinachake chimalowa mu ubongo. Ndiyeno ubongowo umachisunga kuti mudzathe kuchikumbukira. Munthu amaiwala ngati chimodzi mwa zinthu zitatuzi chasokonezeka.

Akuti anthufe timakumbukira zinthu zimene tinamva, tinaziona, tinazikhudza kapenanso zimene tinamva fungo lake. Timathanso kukumbukira zinthu zimene zangochitika kumene kapena zinthu zimene zinachitika kale kwambiri. N’chifukwa chake timatha bwinobwino kuphatikiza manambala m’mutu, kukumbukira nambala ya foni imene munthu akutiuza mpaka kudina manambala onse popanda kufunsanso. Komanso n’chifukwa chake timatha kukumbukira mbali yoyamba ya chiganizo kwinaku tikuwerenga kapena kumvetsera mbali yomaliza. Koma monga tikudziwira, zinthu zimene timazikumbukira m’njira imeneyi sitichedwa kuziiwala.

Kuti tisaiwale zinthu tiyenera kuzikhomereza m’mutu mwathu. Kodi mungatani kuti mukhomereze zinthu m’mutu mwanu? Mfundo zotsatirazi zingathe kukuthandizani.

Chidwi Khalani ndi chidwi pankhani imene mukufuna kukumbukira, ndipo musaiwale zifukwa zimene mukufunira kukumbukira nkhaniyo. N’kutheka kuti mwaonapo kale kuti nkhani ikakukhudzani kwambiri mumatha kuikumbukira mosavuta. Mfundo imeneyi ndi yothandiza kwambiri kwa anthu ophunzira Baibulo. Kuti azikumbukira zinthu akamaphunzira Baibulo ayenera kukhala ndi zolinga ziwiri. Choyamba, kuti ayandikire kwa Mulungu ndipo chachiwiri kuti aphunzitse ena za iye.—Miyambo 7:3; 2 Timoteyo 3:16.

Kuika maganizo pa zinthu Buku lina linati: “Nthawi zambiri timaiwala zinthu chifukwa choti sitinaike maganizo pa chinthucho.” Kodi n’chiyani chimene chingatithandize kuika maganizo pa zinthu? Muzikhala ndi chidwi ndi chinthucho, ndipo ngati n’kotheka lembani notsi. Zimenezi zimathandiza kuika maganizo pa nkhaniyo komanso mungathe kudzaiona panthawi ina mukaiwala.—Mysteries of the Mind.

Kumvetsa Lemba la Miyambo 4:7 limati: “M’kutenga kwako konseko utenge luntha.” Mukapanda kumvetsa zinthu zinazake, zimakhala zovuta kuti muzikumbukire. Kumvetsa kumatanthauza kuona mbali zosiyanasiyana za nkhaniyo, n’kuzilumikiza m’maganizo mwathu kuti tipange chithunzithunzi cha nkhani yonseyo. Mwachitsanzo, munthu amene akuphunzira umakaniko akamvetsa mmene injini imagwirira ntchito, n’zosavuta kuti akumbukire mbali zosiyanasiyana za injiniyo.

Dongosolo Ikani zinthu kapena mfundo zofanana m’gulu limodzi. Mwachitsanzo, ngati mukukagula zinthu monga ndiwo, mukhoza kuzigawa m’gulu la ndiwo zankhuli, zamasamba, zipatso kapena magulu ena. Ngati m’gulu limodzi muli zinthu zingapo gawaninso zinthuzo m’timagulu tina ting’onoting’ono. Manambala a foni amagawidwa m’magawo atatu kuti munthu asamavutike kukumbukira. Pomaliza mukhoza kusanja zinthu kapena mfundo zanu motsatira ndondomeko inayake kapena motsatira zilembo za afabeti.

Kubwereza mokweza Kubwereza mokweza zinthu zimene mukufuna kuzikumbukira (kaya ndi mawu a chilankhulo china) n’kothandiza kuti ubongo usunge bwino mawuwo. N’chifukwa chiyani tikutero? Choyamba, kutchula liwu kumakuthandizani kuika maganizo anu pa liwulo. Chachiwiri, mukatchula liwu wokuphunzitsaniyo amakuuzani ngati mwakhoza kapena mwalakwitsa. Chachitatu, mukamamvetsera ngakhale zimene mwanena inu nomwe mbali zina za ubongo wanu zimagwira ntchito.

Kuona zinthu m’maganizo Ganizirani mmene zinthu zimene mukufuna kukumbukirazo zingaonekere. Mwina mungajambule papepala zinthuzo. Mofanana ndi kubwereza mokweza, kuganizira maonekedwe a zinthu kumathandiza kuti mbali zosiyanasiyana za ubongo wanu zigwirenso ntchito. Zinthu sizivuta kukumbukira ngati mukuzimva, kuziona komanso kuzigwira.

Kugwirizanitsa zinthu Pophunzira zinthu ndi bwino kuzigwirizanitsa ndi zinthu zina zimene mukuzidziwa. Kugwirizanitsa zinthu zimene mukuphunzira ndi zinthu zina zimene mukuzidziwa kale kumathandiza kuti zikhazikike m’mutu mwanu komanso kuti mudzazikumbukire mosavuta. Mwachitsanzo, kuti muthe kukumbukira dzina la munthu, muyenera kugwirizanitsa dzinalo ndi maonekedwe ake amene amamusiyanitsa kwambiri ndi anthu ena kapena zinthu zina zimene zingakuthandizeni kum’kumbukira. M’posavuta kukumbukira bwino zinthu ngati mwazigwirizanitsa ndi zinthu zoseketsa kwambiri. Mwachidule, tingati muyenera kuganizira za anthu komanso zinthu zimene mukufuna kuti muzikumbukire.

Buku lina linati: “Tikamachita zinthu popanda kuganizira bwino zinthu zotizungulira, zimene zikutichitikira komanso zimene zinatichitikira kale, sitingakumbukire bwinobwino zochitika zambiri za pamoyo wathu.”—Searching for Memory.

Kukhomereza Ndi bwino kulola kuti mfundo zimene mwaphunzira zilowerere bwinobwino m’maganizo mwanu. Njira imodzi yochitira zimenezi ndiyo kubwereza zimene mwaphunzirazo mwina mwa kuuza munthu wina. Ngati mwaona kapena kumva zinthu zina zosangalatsa, kapena ngati mwawerenga nkhani ina yolimbikitsa m’Baibulo kapenanso m’mabuku ofotokoza Baibulo muyenera kuuza ena. Mukatero inuyo ndi munthu amene mukumuuzayo mumapindula, chifukwa inu mumakhomereza m’mutu mwanu zinthuzo pomwe mnzanuyo amalimbikitsidwa. Pajatu mphini yobwereza imawala.

Njira Inanso Yothandiza Kukumbukira

Kalekale, anthu ena a ku Greece ndi ku Rome ankatha kulankhula nthawi yaitali pagulu la anthu popanda kuonera papepala. Kodi ankatha bwanji zimenezi? Iwo anali ndi njira yawo yowathandiza kusunga zinthu m’mutu kuti adzazikumbukire ngakhale patapita nthawi yaitali.

Munthu wina wolemba ndakatulo dzina lake Simonides wa ku Ceos anafotokoza za njira imeneyi mu 477 B.C.E. Iwo amaganizira malo amene zinthu zachitikira kuti adzazikumbukire. Amagwiritsa ntchito njira zonse zimene takambirana zija koma mogwirizana ndi malo enaake mumsewu kapena m’nyumba zawo. Anthu amene amagwiritsa ntchito njira imeneyi amaganizira malo kapena zinthu zowazungulira n’kumazigwirizanitsa ndi zinthu zimene akufuna kuzikumbukira. Akafuna kukumbukira zinthuzo amangoganizira malo ndi zinthu zowazungulirazo basi.—Onani bokosi lakuti  “Yendani Ulendo wa M’maganizo.”

Chaka ndi chaka kumachitika mpikisano wofuna kudziwa anthu amene amakumbukira kwambiri zinthu pa dziko lonse (Word Memory Championships). Ndipo atapanga kafukufuku pa anthu amene anapambana pa mpikisanowu anapeza kuti sanali ndi nzeru zinazake zapadera. Komanso ambiri mwa anthuwa anali a zaka za pakati pa 40 ndi 50. Kodi chinsinsi chawo chagona pati? Ambiri ananena kuti amatha kukumbukira kwambiri chifukwa amagwiritsa ntchito njira zimene talongosola m’nkhaniyi.

Ngati mukufuna kukumbukira mawu angapo njira yabwino ndi yotenga chilembo choyambirira cha liwu lililonse n’kupanga liwu limodzi latsopano. Mwachitsanzo, tayerekezerani kuti mukufuna kukumbukira mayina otsatirawa; Mateyo, Aroma, Luka, Agalatiya, Yakobe ndi Aefeso. Zimene mungachite ndizo kungotenga chilembo choyambirira cha dzina lililonse n’kupanga liwu lakuti “MALAYA.” Aheberi akale ankagwiritsiranso ntchito kwambiri njira ina yofanana ndi imeneyi. Mwachitsanzo, m’masalmo ambiri ngati mawu oyambirira a vesi ayamba ndi chilembo choyambirira cha afabeti ya Chiheberi, vesi lotsatira limayamba ndi chilembo chachiwiri. Zimateronso ndi ndime zina. (Anachita izi mu Salmo 25, 34, 37, 111, 112 ndi 119.) Zimenezi zinathandiza oimba ambiri kukumbukira mavesi 176 onse a mu Salmo 119.

N’zotheka ndithu kuthetsa vuto loiwalaiwala. Ofufuza apeza kuti ubongo wathu umasunga bwino zinthu n’kumazikumbukira patadutsa nthawi yaitali ngakhale mpaka titakalamba. Chofunika ndi kuugwiritsa ntchito kwambiri.

[Bokosi patsamba 27]

MFUNDO ZINA ZOWONJEZERA

▪ Chepetsani vuto la kuiwala mwa kuphunzira luso linalake, chinenero china kapena chipangizo chinachake choimbira.

▪ Muziika maganizo anu pa zinthu zofunika kwambiri.

▪ Gwiritsani ntchito njira zimene tafotokoza m’nkhaniyi.

▪ Muzimwa madzi okwanira. Kuperewera kwa madzi m’thupi kumasokoneza ubongo.

▪ Muzigona mokwanira. Ubongo wanu umasunga zinthu zofunika kukumbukira panthawi imene mukugona.

▪ Muzikhala ndi nthawi yopuma mukamaphunzira. Mukapanikizika thupi limatulutsa timadzi tina timene timasokoneza minyewa.

▪ Pewani kumwa mowa kwambiri komanso kusuta. Mowa umachititsa kuti munthu asamakumbukire zinthu zimene zangochitika kumene ndipo anthu amene satha kukhala osamwa mowa amaiwalaiwala zinthu chifukwa choti m’thupi mwawo simukhala mavitamini othandiza kukumbukira. Ndipo kusuta kumachititsa kuti mpweya wofunika usafike wokwanira ku ubongo. *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 36 Mfundozi zachokera m’magazini ina ya pa Intaneti yotchedwa Brain & Mind.

[Bokosi/Zithunzi pamasamba 28, 29]

 YENDANI ULENDO WA M’MAGANIZO

Kodi mungatani kuti mukumbukire zinthu zimene mukufuna kukagula monga buledi, mazira, mkaka ndi batala. Yerekezerani kuti mukuzungulira m’nyumba mwanu ndipo mukuona zinthuzo.

Onani m’maganizo anu buledi ali pampando

mazira ali pansi pa nyale

nsomba ikusambira mu chitini cha mkaka

batala atapakidwa pa galasi la TV

M’posavuta kukumbukira zinthu ngati mukuziyerekezera ndi zinthu zoseketsa kwambiri kapena zoti sizingachitike. Mukafika ku msika muyenera kungoganizira ulendo wa m’maganizowo basi.

[Bokosi patsamba 29]

KUIWALA KULI NDI UBWINO WAKE

Kodi mukuganiza kuti mukanakhala kuti mumakumbukira chilichonse, kaya chikhale chofunika kapena chosafunika, mukanakhala munthu wotani? M’mutu mwanu mukanakhala zinthu tho. Magazini ina inafotokoza za mayi wina amene anali ndi vuto lokumbukira china chilichonse chimene chinachitika pamoyo wake. Mayiyo anati moyo wake “unali wotopetsa kwambiri chifukwa sankatha kudziletsa pankhani yokumbukira zinthu ndipo chinali chipsinjo.” Koma ubwino wake ndi wakuti ambirife tilibe vuto limeneli. Akatswiri ena apeza kuti izi zili choncho chifukwa chakuti ubongo wathu umafufuta zinthu zosafunika kwenikweni. Magaziniyo inanenanso kuti: “Kuiwala zinthu zina n’kofunika kuti ubongo wathu uzitha kukumbukira zinthu bwino. Tikaiwala zinthu zina zofunika . . . ndiye kuti zangochitika mwatsoka panthawi imene ubongo unali kufufuta zinthu zina zosafunika.”–New Scientist.