Zochitika Padzikoli
Zochitika Padzikoli
▪ “Gulu la akatswiri asayansi ofufuza zinthu za kuthambo linagwiritsa ntchito makina apamwamba kwambiri ounikira zinthu zakutali omwe ali pa phiri lalitali la ku Hawaii lotchedwa Mauna Kea ndipo iwo anaona milalang’amba yaikuluikulu kwambiri moti pangadutse zaka 200 miliyoni kuti kuwala kochokera mbali imodzi kukafike mbali ina ya milalang’ambayi. Aka n’koyamba kupeza milalang’amba yaikulu chonchi.”—SUBARU TELESCOPE WEB SITE, JAPAN.
▪ Ofesi ya za kalembera ya ku United Kingdom inanena kuti “chiwerengero cha maukwati ovomerezeka [ku England ndi ku Wales] m’chaka cha 2006 chinali chotsika kwambiri poyerekezera ndi zaka 110 za m’mbuyomo. Anthu ambiri amangotengana popanda kumangitsa ukwati wovomerezeka.”—THE GUARDIAN WEEKLY, BRITAIN.
▪ Bungwe lina limene limaona mmene chipembedzo chimakhudzira moyo wa anthu linanena kuti, “anthu 44 pa 100 alionse akhala akusinthasintha maganizo awo pankhani ya chipembedzo. Ena asamukira m’zipembedzo zina ndipo ena amene sanali m’chipembedzo chilichonse, ayamba kupembedza, komanso ena asiyiratu kupembedza.”—U.S.A.
Chiwerewere Chatenga Malo M’makoleji
Mayi wina wachikatolika, dzina lake Donna Freitas, yemwe ndi pulofesa wa maphunziro a zachipembedzo, anachita kafukufuku pankhani ya chiwerewere komanso chipembedzo m’makoleji a ku America. Ponena zimene anapeza pa kafukufukuyu, iye anati: “Kupatulapo makoleji a matchalitchi ena ochepa chabe, m’makoleji aboma, achikatolika komanso a anthu ena mukuchitika chiwerewere kwabasi, moti wophunzira mmodzi amagonana ndi anthu osiyanasiyana, ndipo zimenezi zimachitikira kumakoleji komweko. M’nyuzipepala ina yachikatolika, mayi Freitas anati kulephera kwa zipembedzo kuthetsa mchitidwewu kukusonyeza kuti “ophunzira ochuluka m’makoleji amatengeka kwambiri ndi kugonana kwachisawawaku” ndipo kukusonyezanso kuti “zipembedzo zikulephera kuthandiza anthu kusiya mchitidwe woipawu.”—National Catholic Reporter.
Makolo Akulipidwa Kuti Alere Atsikana
Wailesi ya BBC inalengeza kuti dziko la India lalonjeza kuti lizipereka ndalama pafupifupi madola 3,000 kwa makolo osauka kuti ziwathandize polera ana awo aakazi. Mabanja azilandira mphoto ya ndalama mwana wa mkazi akangobadwa ndipo azilandirabe ndalamazi mwanayu akamakula mpaka atakwanitsa zaka 18. M’chaka cha 1994, dzikoli linakhazikitsa malamulo oletsa kupondereza akazi komanso kutaya mimba akaona kuti mwanayo adzakhala wamkazi. Komatu mpaka pano anthu sanasiye makhalidwe oipawa. Moti apeza kuti pa zaka 20 zapitazi, mimba za ana aakazi pafupifupi 10 miliyoni zinatayidwa ndipo zimenezi zachititsa kuti m’madera ena am’dzikoli chiwerengero cha atsikana chikhale chotsika kwambiri poyerekezera ndi cha anyamata. Kalembera amene anachitika m’dzikoli m’chaka cha 2001 anasonyeza kuti m’madera ena pali atsikana 927 a zaka zosapitirira 6 pa anyamata 1,000 alionse. Koma chiwerengero cha atsikana m’madera ena chinali chotsika kwambiri. Mwachitsanzo, mu mzinda wina anapeza kuti pakabadwa ana aakazi 793 pamabadwa ana aamuna 1,000.
Mbalame Zimadana ndi Phokoso
Mbalame zina zimayesetsa kuimba mokweza kwambiri kuti zizimveka kuposa phokoso limene limamveka m’mizinda. Magazini ina inanena kuti anthufe sitisangalala ndi phokoso la m’matawunimu, komatu kwa mbalame limeneli ndi “vuto lalikulu kwambiri,” chifukwa mbalame zazimuna zimayimba “pofuna kukopa zazikazi komanso kutetezera malo okhala.” Popeza kuti m’mizinda mumakhala phokoso lochuluka mbalame zimayesetsa mmene zingathere kuti zimveke. Zimayesa kuyimba usiku kapena kuimba mokweza kwambiri. Komanso si mbalame za m’tawuni zokha zimene zimachita zimenezi. Nazonso mbalame zokhala m’malo oyandikana ndi “mathithi kapena mitsinje zimaimba mokweza kwambiri.”—New Scientist.