Khungu la Shaki
Panagona Luso!
Khungu la Shaki
● Khungu la shaki limaoneka ngati ndi losalala kwambiri, koma mukaligwira kuyambira kumchira kupita kumutu limamveka kuti ndi lokhakhala. *
Taganizirani izi: Shaki ili ndi mamba okhala ndi tingalande ndipo tingalande timeneti ndi timene timapangitsa kuti ikhale yokhakhala. Mamba amenewa amathandiza shakiyo m’njira ziwiri. Choyamba, shaki ikamasambira, madzi amayenda m’tingalandeto ndipo zimenezi zimachititsa kuti shakiyo izisambira mosavuta. Chachiwiri, mambawo amayendayenda shakiyo ikamasambira ndipo zimenezi zimathandiza kuti pakhungu pake pasamakhale tizilombo toyambitsa matenda.
Asayansi aphunzira zambiri kuchokera pa khungu la shaki. Mwachitsanzo, iwo apanga kale zovala zosambirira zokhala ndi mamba ngati a shaki zimene zimathandiza kuti munthu azisambira mofulumirirapo. Ndipo akuona kuti potengera mmene mambawo amachitira, akhoza kupanga magalimoto ndi sitima zam’madzi zothamanga kwambiri.
Akatswiri ena akuganizira zopanga penti yopakira sitima zam’madzi yoti isamasunge tizilombo toyambitsa matenda komanso yosawononga zachilengedwe. Zinthu zina zomwe akuganiza kuti angapange potengera khungu la shaki ndi mankhwala ndiponso zipangizo zogwiritsa ntchito kuchipatala, zomwe zingathandize kuti anthu asamatenge matenda m’chipatala.
Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi khungu la shaki lomwe limathandiza kuti shaki izithamanga kwambiri komanso kuti isamagwidwe ndi tizilombo toyambitsa matenda linakhalapo mwangozi kapena linachita kulengedwa?
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 3 Khunguli limamveka losalala mukaligwira kuyambira kumutu kupita kumchira.
[Chithunzi patsamba 10]
Mamba a Shaki
[Mawu a Chithunzi patsamba 10]
Scales: © Eye of Science/Photo Researchers, Inc.; shark: © Image Source/age fotostock