Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungatani Kuti Muzigwiritsa Ntchito Nthawi Mwanzeru?

Kodi Mungatani Kuti Muzigwiritsa Ntchito Nthawi Mwanzeru?

Kodi Mungatani Kuti Muzigwiritsa Ntchito Nthawi Mwanzeru?

“Kanthu kali konse kali ndi nthawi yake.”—Mlaliki 3:1.

KUTI muzikhala ndi nthawi yochita zinthu zofunika kwambiri, muyenera kudziwa kaye kuti zinthu zimenezi ndi ziti. Kuchita zimenezi kungakhale kosavuta ngati mukudziwa bwinobwino zolinga zanu ndiponso zinthu zimene mungachite kuti mukwaniritse zolingazo.

Choyambirira, ganizirani zinthu zofunika kwambiri pamoyo wanu monga kugwira ntchito molimbika, maphunziro, achibale anu ndiponso anzanu, kukhala ndi luso pa ntchito kapena masewera enaake, kuoneka bwino, kupeza ndalama, kukhala wosangalala, banja, kukoma mtima, kukhala wathanzi ndiponso kupembedza Mulungu. Kenako, dzifunseni kuti, ‘Pazinthu zimenezi, kodi ndi chinthu chiti chimene chili chofunika kwambiri kwa ine?’

Mukatero, ganizirani zolinga zimene mukufuna kukwaniritsa. Kodi pali kusiyana kotani pakati pa zinthu zofunika kwambiri ndi zolinga? Zinthu zofunika kwambiri zimakhalapo mpaka kalekale, pamene zolinga ndi zinthu zimene mukufuna kuchita pamoyo wanu, ndipo mukangozikwaniritsa basi zimathera pomwepo.

Kodi inuyo muli ndi zolinga zotani? Kodi muli ndi cholinga choti muzikhala ndi nthawi yokwanira yocheza ndi banja lanu? Chopeza ntchito yabwinopo? Chokhala ndi luso pa masewera enaake? Choyesetsa kukhala ndi khalidwe linalake? Chopita kutchuthi? Chowerenga kapena kulemba buku linalake?

Ndiyeno pa zolinga zimenezi, kodi zofunika kwambiri kwa inuyo ndi ziti? Onetsetsani kuti zolinga zanu zikugwirizana ndi zinthu zimene mumaona kuti ndi zofunika pamoyo wanu. Mwachitsanzo, ngati muli ndi cholinga chokhala munthu wachuma kwambiri, ndiye kuti mungamapanikizike kwambiri.

Tsopano, mogwirizana ndi zolinga zimene muli nazo, ganizirani zinthu zimene mungachite kuti mukwaniritse zolingazo. Mwachitsanzo, ngati cholinga chanu china n’chakuti mukhale ochepa thupi, ndiye kuti muyenera kumachita masewera olimbitsa thupi oyenerera.

Kodi Kudziwa Zinthu Zitatu Takambiranazi Kungakuthandizeni Bwanji?

Ngati zolinga zanu zikugwirizana ndi zinthu zofunika kwambiri pamoyo wanu ndipo mukuyesetsa kuchita zinthu zomwe zingakuthandizeni kukwaniritsa zolinga zanuzo, dziwani kuti zonse zidzakuyenderani bwino. Ndipo nthawi yanu yambiri idzathera pa zinthu zofunika kwambiri. Koma zimenezi sizikutanthauza kuti muzinyalanyaza zofuna za ena. (Afilipi 2:4) Koma zikutanthauza kuti muzitha kudziwa ndiponso kupewa kuchita zinthu zosafunika zimene zingakuwonongereni nthawi yanu.

Komabe, ngakhale mutayesetsa kutsatira njira zimenezi, pakhoza kukhalabe mavuto ena ndi ena. Zinthu zina zikhoza kukhala zosafunika kwenikweni koma mungafunikebe kuti muzichite. Ndipo zimenezi zingachititse kuti mupanikizike moti simungakhale ndi nthawi yochita zinthu zofunika kwambiri kwa inu. Nthawi zinanso pangachitike zinthu zamwadzidzidzi. Ndiponso kusintha kwa zinthu zina pamoyo wanu kungachititse kuti muzilephera kuchita zinthu zimene munakonza kuti muchite? Koma kutsatira njira zimene takambiranazi, kungakuthandizeni kuti muzigwiritsa ntchito nthawi yanu mwanzeru.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 6]

KODI ZIPANGIZO ZAMAKONO ZIMATHANDIZA KUTI MUSAWONONGE NTHAWI?

Ena zimawathandiza kuti asawononge nthawi koma enanso zimawadyera nthawi. Mwachitsanzo, kakompyuta kam’manja kamakhala ndi zinthu monga kalendala, malo olemba manambala a foni, maadiresi, malo omwe mungalembepo zinthu zimene mukufuna kuchita, malo omwe mungalembe kalata kapena zinthu zina, kamera komanso kamakhala ndi Intaneti. Chipangizo chimenechi chikhoza kukuthandizani kuti musawononge nthawi. Komabe, chipangizo chimenechi chikhozanso kumakudyerani nthawi ngati mumangokhalira kuchita masewera a pa kompyuta kapena kufufuza zinthu zina m’malo mocheza ndi anzanu kapena kuchita zinthu zina zofunika kwambiri.

Mfundo yothandiza: Muzifufuza kaye musanagule chipangizo chinachake chifukwa ngati chipangizo chimene mwagula chimawonongekawonongeka, mungamawononge nthawi yaitali mukuchikonza. Komanso dziwani kuti chipangizo chilichonse chimakhala chothandiza malinga ndi mmene mukuchigwiritsira ntchito. Choncho, ngati muli ndi chipangizo chinachake, muzionetsetsa kuti mukuchigwiritsa ntchito mwanzeru.

[Chithunzi pamasamba 4, 5]

Muyenera kupeza nthawi yochita zinthu zofunika kwambiri