Mafunso Amene Anthu Amakonda Kufunsa
Mafunso Amene Anthu Amakonda Kufunsa
N’chifukwa chiyani anthu ena amanena zoipa zokhudza Mboni za Yehova?
Anthu ena amanena zoipa zokhudza Mboni za Yehova chifukwa chakuti anauzidwa zabodza kapena chifukwa chakuti amadana ndi ntchito yawo yolalikira. Komabe dziwani kuti Mboni za Yehova zimagwira ntchito imeneyi chifukwa chokonda anthu. Mbonizo zimadziwa kuti “aliyense woitana pa dzina la Yehova adzapulumuka.”—Aroma 10:13.
Kodi Mboni za Yehova ndi gulu lachikhristu? Kodi gulu lawo langokhala gulu la anthu amakani kapena ampatuko?
Mboni za Yehova ndi gulu lachikhristu chifukwa ziphunzitso zawo zimachokera m’Baibulo. Koma Mboni za Yehova zimasiyana ndi matchalitchi ena chifukwa zimaona kuti zinthu zina zimene matchalitchi enawo amaphunzitsa si za m’Baibulo. Mwachitsanzo, Baibulo siliphunzitsa kuti Mulungu, yemwe ndi wachikondi kwambiri, amazunza anthu kwamuyaya kumoto. Siliphunzitsanso kuti anthu ali ndi mzimu umene sumafa komanso silivomereza kuti Akhristu azilowa ndale.—Ezekieli 18:4; Yohane 15:19; 17:14; Aroma 6:23. *
Komanso, Mboni za Yehova ndi gulu lachikhristu chifukwa anthu ake amatsatira Khristu pa moyo wawo. Mwachitsanzo, Khristu ndiponso Akhristu oyambirira sankalowerera ndale. M’malomwake, ankalalikira za Ufumu wa Mulungu. (Luka 4:43; Yohane 15:19; 17:14) Potsatira chitsanzo chimenechi, Mboni za Yehova sizilowa ndale ndipo siziumiriza anthu kutsatira maganizo awo pogwiritsa ntchito ndale kapena zinthu zina. M’malomwake, iwo amakambirana ndi anthu potsatira zimene Akhristu oyambirira ankachita. Nthawi zambiri amakambirana ndi munthu aliyense payekha, ndipo amafotokoza mfundo zokhala ndi maziko enieni.—Machitidwe 19:8.
Gulu lampatuko ndi gulu limene limachita zinthu motsutsana ndi anthu ena m’chipembedzo chomwecho, kapena gulu limene limachoka m’chipembedzo n’kukayambitsa chipembedzo china. Mboni za Yehova sizinachokere m’chipembedzo chilichonse. Choncho, si gulu lampatuko.
Kodi pamisonkhano ya Mboni za Yehova pamachitika zotani?
Pamisonkhano yawo amagwiritsa ntchito kwambiri Baibulo ndipo nthawi zambiri anthu onse amakhala ndi mwayi wolankhula. Alendo amakhala olandiridwa. Msonkhano umodzi umene umachitika mlungu uliwonse, umatchedwa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Msonkhanowu umathandiza anthu onse mumpingo kuti azitha kuwerenga, kuphunzitsa, ndiponso kufufuza nkhani. Pamsonkhano wina, pamakhala nkhani ya m’Baibulo yomwe imakambidwa kwa mphindi 30. Nkhani zimene zimakambidwa zimakhudza aliyense, ngakhale anthu omwe si Mboni. Nkhaniyi ikatha, anthu amaphunzira Baibulo pogwiritsa ntchito magazini 2 Akorinto 8:12.
a Nsanja ya Olonda. Misonkhanoyi imayamba ndiponso kutha ndi nyimbo komanso pemphero. Pamisonkhanoyi, anthu sakakamizidwa kupereka ndalama ndipo sipayendetsedwa mbale ya zopereka.—Kodi Mboni za Yehova zimapeza kuti ndalama zimene zimagwiritsa ntchito?
Ndalama zoyendetsera ntchito yawo zimachokera kwa anthu amene amapereka mwa kufuna kwawo. Mboni za Yehova sizilipiritsa anthu ndalama zikachititsa mwambo wa ubatizo, ukwati, maliro kapena mwambo wina uliwonse. Ndiponso siziuza anthu kuti azipereka chakhumi. Aliyense amene akufuna kupereka ndalama pamisonkhano yawo amakaponya m’bokosi limene limakhala kumbuyo m’Nyumba ya Ufumu. A Mboni za Yehova amapanga okha mabuku ofotokoza Baibulo amene amagwiritsa ntchito ndipo zimenezi zimathandiza kuti asamawononge ndalama zambiri. Komanso Nyumba za Ufumu ndi maofesi awo nthawi zambiri amamangidwa ndi anthu ongodzipereka.
Kodi a Mboni za Yehova akadwala, amapita kuchipatala?
Inde amapita. Ndipo amayesetsa kwambiri kuti iwo komanso anthu a m’banja mwawo alandire chithandizo chabwino kwambiri. Komanso, pali a Mboni za Yehova ambiri amene ndi manesi, madokotala komanso othandiza anthu pangozi. Komabe, Mboni za Yehova sizilola kupatsidwa magazi chifukwa Baibulo limatilangiza “kupewa . . . magazi.” (Machitidwe 15:28, 29) N’zosangalatsa kuti madokotala ambiri akuona kuti chithandizo cha mankhwala chosagwiritsa ntchito magazi ndi chabwino kwambiri chifukwa magazi amayambitsa matenda ambiri.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 5 Zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhani zimenezi ndi zinanso zambiri mungazipeze m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 7]
AMAKHALA MOGWIRIZANA
Tawuni ya Bejucal de Ocampo imene ili kum’mwera m’dziko la Mexico ndi yodabwitsa kwambiri. Nyuzipepala ina inati: “Anthu ambiri m’tawuniyi ndi a Mboni za Yehova. Ndipo chipembedzo ndi boma zimachita zinthu mogwirizana. . . . Anthu ambiri m’tawuniyi anasiya kumwa mowa ndi kusuta fodya ndipo masiku ano amakonda kuimba nyimbo ndi kuwerenga Baibulo. Amalemekezanso akuluakulu a boma.”—Inatero nyuzipepala ya Excélsior.
Nyuzipepalayi inanenanso kuti ngakhale kuti m’tawuniyi muli zipembedzo zosiyanasiyana, “anthu azipembedzo zonsezi amakhala mogwirizana. Sipakhala udani ndipo kusiyana kwa zipembedzo sikuchititsa kuti azilephera kupatsana moni . . . Banja lililonse lili ndi ufulu wopembedza mmene likufunira koma zimenezi sizichititsa kuti anthu asamagwirizane. Anthu a m’tawuniyi sadandaula kuti muli anthu a Mboni za Yehova ambiri.” Ndiponso mphunzitsi wina wa pasukulu ina ya sekondale kumeneko ananena kuti ana a Mboni za Yehova ‘amavala modzilemekeza, amakhoza bwino m’kalasi, ndipo ali ndi khalidwe labwino.’