Zochitika Padzikoli
Zochitika Padzikoli
Kodi Kukhala ndi Mfuti N’kothandizadi?
Bungwe Lofufuza za Matenda a Khansa Padziko Lonse lati lasintha chenjezo lake lokhudza kugwiritsa ntchito makina odetsera khungu. Makinawa amagwiritsa ntchito mphamvu yamagetsi imene imachititsa kuti khungu la munthu lizida ngati kuti anali padzuwa. Poyamba bungweli linachenjeza kuti makinawa “akhoza kuyambitsa khansa,” koma panopa chenjezoli likunena kuti makinawa “amayambitsa khansa.”—THE LANCET ONCOLOGY, BRITAIN.
Ku Argentina, pa akazi 10 alionse oyembekezera, akazi 9 amakhala oti sankafuna kukhala ndi pakati.—CLARÍN, ARGENTINA.
“Asayansi amatulukira nyama ndi zomera zatsopano tsiku lililonse. Tsiku lililonse, asayansiwa akutulukira zamoyo zatsopano zokwana 50. M’chaka cha 2006 chokha, anatulukira zomera ndi nyama zatsopano zokwana 17,000. Zimenezi zikuimira 1 peresenti ya zamoyo 1.8 miliyoni zimene azitulukira kale.”—TIME, U.S.A.
Kodi anthu amene amayenda ndi mfuti imawathandizadi akaukiridwa ndi munthu winawake? Kafukufuku amene yunivesite ina ku United States inachita, anasonyeza kuti nthawi zambiri sithandiza. Kupatulapo anthu amene amawomberedwa ndi apolisi, amadziwombera okha, ndiponso amawomberana mwangozi, ochita kafukufukuwa anapeza kuti, “pa anthu 5 alionse amene amawomberedwa, 4 amakhala kuti amayenda ndi mfuti.” Ochita kafukufukuwo anavomereza kuti anthu ena amene ali ndi mfuti amatha kudziteteza bwinobwino ndi mfuti yawoyo akaukiridwa, koma nthawi zambiri satha kutero. Lipoti limene ochita kafukufukuwo analemba linati maganizo akuti mfuti “zimateteza munthu ku zigawenga ayenera kuonedwanso ndi kusinthidwa.”
Ansembe Achibuda Akudzipenta Milomo
Ansembe aamuna achibuda amene angoyamba kumene unsembe ku Thailand “akuipitsa dzina la chipembedzo chachibuda, chimene chili ndi ziphunzitso zokhwima.” Ansembewa akumapenta milomo yawo, kuvala mikanjo yothina kwambiri, “kugwedeza kwambiri chiuno poyenda komanso kunyamula zikwama zachikazi zam’manja,” inatero nkhani ina munyuzipepala inayake ya ku Bangkok. Atsogoleri ena achipembedzo akuda nkhawa ndi zimene akuchita anthu ongolowa kumene unsembe amene amagonana amuna okhaokha. Choncho akuganiza zophunzitsanso ansembe atsopanowa khalidwe. Mlaliki wina wotchuka wachibuda anati ansembe achibuda saletsedwa kugonana amuna okhaokha, “chifukwa akanakhala kuti amaletsa, theka la ansembewa akanachotsedwa unsembe.”
Sitima Zokwera Akazi Okhaokha
Kwa zaka zambiri, akazi amene amakwera sitima ku India, zimene zimakhala zodzaza kwambiri, akhala akuvutitsidwa ndi amuna. Amunawa amawagwiragwira, kuwatsina, kuwayang’anitsitsa, kapena kuwavutitsa m’njira zina. Nyuzipepala yotchedwa The Telegraph ya ku Calcutta inanena kuti chifukwa chakuti madandaulo oterewa amachuluka, boma laganiza zoti amuna asamakwere sitima zina. Choncho m’mizinda ikuluikulu inayi ya ku India, yomwe ndi New Delhi, Mumbai, Chennai, ndi Calcutta, boma lakhazikitsa sitima zingapo zokwera akazi okhaokha. Akazi amene akwerapo sitima zimenezi akuti akusangalala kwambiri.