Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Bwanji Mulungu Osangomuwononga Mdyerekezi?

Bwanji Mulungu Osangomuwononga Mdyerekezi?

Zimene Baibulo Limanena

Bwanji Mulungu Osangomuwononga Mdyerekezi?

MUTAKHALA ndi mphamvu zothetsa mavuto a munthu wina, kodi mungawathetse? Anthu ogwira ntchito zopulumutsa anthu, nthawi zambiri amathamangira kudera kumene kwachitika tsoka linalake kuti akapulumutse anthu omwe sakuwadziwa n’komwe. Choncho, anthu ena angafunse kuti, ‘Nanga n’chifukwa chiyani Mulungu akuchedwa kuwononga Mdyerekezi, amene anayambitsa mavuto adzaoneni omwe anthu ali nawo?’

Kuti tiyankhe funso limeneli, yerekezerani kuti mwapita kukhoti kukamvetsera mlandu wa munthu yemwe wapha mnzake. Munthu amene akuimbidwa mlanduyo akufuna kuti asokoneze mlanduwo, ndipo akunena kuti woweruzayo ndi wokondera ndiponso anthu amene asankhidwa kuti agamule mlanduwo apatsidwa ziphuphu ndi woweruzayo. Choncho, woweruzayo akuitana mboni zambirimbiri kuti zidzapereke umboni wawo n’cholinga choti chilungamo chidziwike.

Woweruzayo akudziwa kuti kuitanitsa mboni zambirimbiri kutalikitsa mlanduwo ndipo zimenezi zikhoza kubweretsa mavuto ena. Choncho akufuna kuyesetsa kuti mlanduwo usatenge nthawi yaitali kwambiri. Koma iye akudziwanso kuti mbali zonse ziwiri zikufunika kupatsidwa nthawi yokwanira kuti zipereke umboni wawo, n’cholinga choti chigamulo chake chikhale choyenera, choti anthu angamadzachitsatire m’tsogolo pakakhala mlandu wofanana ndi umenewu.

Chitsanzo chimenechi chikufanana ndi mlandu umene Mdyerekezi, yemwe amatchedwanso kuti “njoka,” ndi “Satana,” anayambitsa. Iye anaimba mlandu Yehova, yemwe ndi “Wam’mwambamwamba, wolamulira dziko lonse lapansi.” (Chivumbulutso 12:9; Salimo 83:18) Kodi Mdyerekezi ndi ndani kwenikweni? Nanga kodi iye anaimba Yehova Mulungu mlandu wotani? Ndiponso, kodi Mulungu adzamuwononga liti?

Pakufunika Chigamulo Choti Chingadzatsatiridwe M’tsogolo

Poyamba, Mdyerekezi anali cholengedwa chauzimu changwiro, mmodzi wa angelo a Mulungu. (Yobu 1:6, 7) Iye anadzisandutsa yekha Mdyerekezi pamene anayamba kulakalaka kwambiri kuti anthu azimulambira. Ananena kuti Mulungu si woyenera kulamulira komanso si woyenera kuti ena azimumvera. Iye ananenanso kuti anthu amangotumikira Mulungu chifukwa chakuti amawadalitsa, ndipo atakhala kuti anthuwo ali pa mavuto akhoza ‘kutukwana’ Mlengi wawo.—Yobu 1:8-11; 2:4, 5.

Zimene Satana ananenazi sizikanayankhidwa pongogwiritsa ntchito mphamvu. Ndipo Mulungu akanangopha Mdyerekezi m’munda wa Edeni, ena akanaganiza kuti mwina Mdyerekeziyo amanena zoona. Choncho Mulungu, yemwe ali ndi ulamuliro wonse, anayamba kuweruza mlanduwo kuti nkhani zimenezi zitheretu m’maganizo a aliyense amene amaidziwa nkhaniyi.

Potsatira mfundo komanso chilungamo chake, Yehova Mulungu anasonyeza kuti mbali iliyonse ikuyenera kukhala ndi mboni zoti zipereke umboni wawo pa mlanduwo. Nthawi imene yadutsayi yapatsa mpata ana a Adamu wopereka umboni wawo wotsimikizira kuti ali kumbali ya Mulungu. Iwo achita zimenezi mwa kusankha kukhala okhulupirika kwa Mulungu chifukwa chomukonda, ngakhale akukumana ndi mavuto.

Kodi Mdyerekezi Akhalapobe Mpaka Liti?

Yehova Mulungu akudziwa bwino kuti pa nthawi imene mlanduwu uli mkati, anthu akupitirizabe kuvutika. Komabe, iye akufunitsitsa kuti mlanduwu uthe pa nthawi yoyenerera, popanda kuchedwa ngakhale pang’ono. Baibulo limafotokoza kuti Mulungu ndi “Tate wachifundo chachikulu ndi Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse.” (2 Akorinto 1:3) N’zachidziwikire kuti “Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse,” sadzalola kuti Mdyerekezi akhalepobe pambuyo poti nkhaniyi yathetsedwa, ndipo adzathetsa mavuto onse amene Mdyerekezi anayambitsa. Komabe, Mulungu sadzawononga Mdyerekezi nthawi yake isanakwane. Adzaonetsetsa kuti mlandu uja uthe kaye.

Nkhanizi zikadzathetsedwa, zidzakhala zitaoneka bwinobwino kuti Yehova ndi woyenera kulamulira. Chigamulo chimene Satana adzapatsidwe chidzakhala chitsanzo kwa onse kwamuyaya. Ngati wina m’tsogolo atadzaimbanso Mulungu mlandu wofanana ndi umenewu, adzapatsidwa chigamulo chofanana ndi chimene Satana adzapatsidwe, koma popanda kudikiranso kuti papite nthawi.

Nthawi ikadzakwana, Yehova Mulungu adzauza Mwana wake kuti awononge Mdyerekezi komanso kuti akonzenso zinthu zonse zimene Mdyerekeziyo anawononga. Baibulo limati m’tsogolomu, Khristu “adzapereka ufumu kwa Mulungu wake ndi Atate wake, atathetsa maboma onse, ulamuliro wonse, ndi mphamvu zonse. Pakuti ayenera kulamulira monga mfumu kufikira Mulungu ataika adani onse pansi pa mapazi ake. Imfa nayonso, monga mdani womalizira, idzawonongedwa.”—1 Akorinto 15:24-26.

N’zosangalatsa kuti Baibulo limanena kuti dziko lonse lapansi lidzakhala Paradaiso. Anthu azidzakhala m’paradaiso ameneyu mwamtendere, ngati mmene Mulungu ankafunira poyamba. Baibulo limati: “Anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.” Inde, “olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”—Salimo 37:11, 29.

Taganizirani zinthu zosangalatsa zimene Baibulo limafotokoza kuti zidzachitikira atumiki a Mulungu. Limati: “Taonani! Chihema cha Mulungu chili pakati pa anthu. Iye adzakhala pamodzi nawo, ndipo iwo adzakhala anthu ake. Zoonadi, Mulunguyo adzakhala nawo. Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”—Chivumbulutso 21:3, 4.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

● Kodi ndi mabodza otani amene Mdyerekezi wanenera Mulungu ndi anthu?Yobu 1:8-11.

● Kodi ndi makhalidwe ati a Mulungu amene amatitsimikizira kuti pa nthawi yake, iye adzawononga Mdyerekezi?—2 Akorinto 1:3.

● Kodi Baibulo limatipatsa chiyembekezo chotani?—Chivumbulutso 21:3, 4.

[Chithunzi patsamba 10]

Kuti paperekedwe chigamulo choyenera, chimene chingadzatsatiridwe m’tsogolo pa mlandu wofanana ndi womwewo, anthu a mbali zonse ayenera kupatsidwa nthawi yokwanira kuti apereke umboni wawo