Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndimagwiritsira Ntchito Foni, TV, Kompyuta Kapena Intaneti Mopitirira Malire?

Kodi Ndimagwiritsira Ntchito Foni, TV, Kompyuta Kapena Intaneti Mopitirira Malire?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Ndimagwiritsira Ntchito Foni, TV, Kompyuta Kapena Intaneti Mopitirira Malire?

Kodi achinyamata atatuwa akufanana bwanji?

“Ndimakonda kwambiri kutumiza mauthenga a pa foni. Palibenso china chimene chimandisangalatsa kuposa kuchita zimenezi. Mwina ndingangoti sindingathe kukhala popanda kutumiza mauthenga a pa foni.”—Anatero Alan. *

“Mayi anga atandigulira TV n’kuiika kuchipinda kwanga, ndinasangalala kwambiri. Koma usiku m’malo moti ndizigona ndinkangokhalira kuonera TV. Ndinkakonda kuonera TV m’malo mocheza ndi abale anga kapena anzanga.”—Anatero Teresa.

“Kwa nthawi yaitali ndithu, ndikapita kulikonse kapena ndikamachita chilichonse ndinkangokhalira kudzifunsa ngati munthu wina wandilembera kapena kundiikira zinazake pamalo anga a pa Intaneti. Ndikadzuka pakati pa usiku ndinkapita pa Intaneti. Ndikangopeza mpata uliwonse, ndinkalemba zinthu zatsopano pamalo angawo.”—Anatero Anna.

Kodi ndi wachinyamata uti pa achinyamata atatuwa amene inuyo mukuona kuti ankagwiritsira ntchito foni, TV kapena kompyuta mopitirira malire?

Alan Teresa Anna

MAKOLO anu ali achinyamata, chinthu chomwe chinali chofala ndi mawailesi basi. Nthawi imeneyo mafoni omwe analiko anali a m’nyumba okha ndipo sanali apamwamba. Anali ongogwiritsira ntchito polankhulana basi. Mwina zimenezi zikumveka zachilendo kwambiri kwa inu, si choncho? Mtsikana wina dzina lake Anna ananena kuti: “Makolo anga ali achinyamata zinthu zinali zotsalira kwambiri, moti iwo ayamba kumene kudziwa kugwiritsa ntchito zinthu zina ndi zina za mufoni yawo ya m’manja.”

Masiku ano, mungagwiritse ntchito foni kuti mulankhule ndi anzanu, mumvere nyimbo, muonere filimu, muchite masewera enaake, mutumize imelo, mujambule zithunzi komanso kuti mufufuze zinthu pa Intaneti. Mwina chifukwa chokula ndi zinthu zimenezi, mungaone ngati kuzigwiritsa ntchito nthawi zonse kulibe vuto. Koma makolo anu angaone kuti mukuzigwiritsa ntchito mopitirira malire. Ngati atakuuzani nkhawa yawo, musanyalanyaze. Mfumu ya nzeru Solomo inati: “Munthu aliyense woyankhira nkhani asanaimvetsetse n’ngopusa.”—Miyambo 18:13.

Kodi mukudziwa chifukwa chake makolo anu angade nkhawa? Onani zinthu zotsatirazi kuti mudziwe ngati mukugwiritsa ntchito foni, TV, kompyuta kapena Intaneti mopitirira malire.

‘Kodi Sinditha Kukhala Popanda Kugwiritsa Ntchito Foni, TV, Kompyuta Kapena Intaneti?’

Kodi mungadziwe bwanji kuti muli ndi chizolowezi choipa pa nkhani yogwiritsa ntchito foni, TV, kompyuta kapena Intaneti? Buku lina linanena kuti mungadziwe zimenezi ngati “mumachita zinthuzo kwa nthawi yaitali komanso mobwerezabwereza n’kumalephera kuzisiya kapena kukana kuzisiya, ngakhale zotsatira zake zitakhala zoipa.” Mogwirizana ndi zimene bukuli linanena, achinyamata onse atatu amene tawagwira mawu kumayambiriro kwa nkhani ino amagwiritsira ntchito foni, TV, kompyuta kapena Intaneti mopitirira malire. Kodi inunso muli ndi vuto limeneli? M’munsimu, muli zina za zizindikiro zosonyeza kuti munthu akuchita zinthu mopitirira malire zimene buku lija linafotokoza. Werengani zimene anzanu anena ndipo onani ngati inunso munanenapo kapena kuchita zinthu zofanana ndi zimenezi. Kenako lembani mayankho anu.

Kuchita zinthu nthawi yaitali. “Ndinkatha nthawi yaitali ndikuchita masewera a pa kompyuta. Nthawi zambiri ndinkagona mochedwa komanso ndinkasowa nthawi yocheza ndi anthu ena. Sindinkacheza kwambiri ndi anthu a m’banja lathu komanso maganizo anga onse ankangokhala pa zinthu zongoyerekezera zomwe ndinkaona m’masewerawo.”—Anatero Andrew.

Kodi inuyo mukuona kuti muyenera kuthera nthawi yochuluka bwanji pa masewera a pa kompyuta? ․․․․․

Kodi makolo anu amafuna kuti muzitha nthawi yochuluka bwanji? ․․․․․

Kodi tsiku lililonse mumatha nthawi yochuluka bwanji mukutumiza mauthenga pa foni, kuonera TV, kulemba zinthu kapena kuika zithunzi pa Intaneti, kuchita masewera pa kompyuta, ndi zina zotero? ․․․․․

Malinga ndi zimene mwayankha, kodi mukuona kuti muli ndi chizolowezi chogwiritsa ntchito foni, TV, kompyuta kapena Intaneti mopitirira malire?

□ Inde □ Ayi

Kulephera kapena kukana kusiya. “Makolo anga akandiona ndikulemba uthenga pa foni, amandiuza kuti ndayamba kuchita zimenezi mopitirira malire. Koma ndikayerekezera ndi anzanga, ndimaona kuti ineyo sinditumiza mauthenga n’komwe. N’zoona kuti kuyerekezera ndi makolo anga, ine ndimatumizadi mauthenga ambiri. Koma sindingadziyerekezere ndi makolo anga chifukwa kuchita zimenezi kuli ngati kuyerekezera zinthu zosiyana, monga maapozi ndi malalanje. Iwo ali ndi zaka 40 pamene ine ndili ndi zaka 15.”—Anatero Alan.

Kodi makolo anu komanso anzanu akuuzanipo kuti mumawononga nthawi yambiri pa foni, TV, kompyuta kapena pa Intaneti?

□ Inde □ Ayi

Kodi mumalephera kusiya kapena simufuna kusiya kugwiritsa ntchito kwambiri zinthu zimenezi?

□ Inde □ Ayi

Kuipa kwake. “Anzanga amakonda kulemba uthenga pa foni nthawi ina iliyonse ngakhale pamene akuyendetsa galimoto. Koma ndimaona kuti zimenezi n’zoopsa!”—Anatero Julie.

“Nditangopeza foni ya m’manja, ndinkangokhalira kuimbira anthu foni ndi kuwatumizira uthenga. Ndinkalephera kuchita zinthu zina. Zimenezi zinachititsa kuti ndisamagwirizane ndi makolo ndi abale anga, ngakhalenso anzanga ena. Panopa ndimaona kuti ndikamacheza ndi anzanga, nthawi zambiri amandiuza kuti: ‘Taima ndiyankhe kaye, wina wanditumizira uthenga.’ N’chifukwa chake sindigwirizana kwambiri ndi anzanga oterowo.”—Anatero Shirley.

Kodi mumawerenga kapena kutumiza uthenga wa pa foni uku mukuyendetsa galimoto kapena muli m’kalasi?

□ Inde □ Ayi

Mukamalankhula ndi anthu a m’banja lanu kapena anzanu, kodi nthawi zambiri mumawadula mawu kuti muyankhe imelo, foni kapena kulemba uthenga pa foni?

□ Inde □ Ayi

Kodi kugwiritsa ntchito foni, TV, kompyuta kapena Intaneti kumakupangitsani kuti musamagone mokwanira kapena kumakusokonezani kuwerenga?

□ Inde □ Ayi

Zimene Mungachite Kuti Musamazigwiritse Ntchito Mopitirira Malire

Ngati mumagwiritsa ntchito foni, TV, kompyuta kapena Intaneti, dzifunseni mafunso anayi omwe ali m’munsiwa. Kutsatira mfundo za m’Baibulo komanso kutsatira malangizo ena kungakuthandizeni kudziwa zinthu zoyenera ndi zosayenera kuchita pamene mukugwiritsa ntchito zinthu zimenezi, n’cholinga choti musamazigwiritse ntchito mopitirira malire.

1. Kodi nkhani zake ndi zotani ? “Zinthu zilizonse zoona, zilizonse zofunika kwambiri, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zachikondi, zilizonse zoyamikirika, khalidwe labwino lililonse, ndi chilichonse chotamandika, pitirizani kuganizira zimenezi.”—Afilipi 4:8.

Muzicheza ndi anzanu komanso anthu a m’banja lanu. Muzikambirana nkhani ndi zinthu zina zolimbikitsa.—Miyambo 25:25; Aefeso 4:29.

Musamafalitse miseche, musamatumizire anthu ena mauthenga oipa pa foni kapena zithunzi zolaula, musamaonere mavidiyo kapena mapulogalamu oipa pa TV.—Akolose 3:5; 1 Petulo 4:15.

2. Kodi ndimazigwiritsa ntchito nthawi yanji ? “Chilichonse chili ndi nthawi yake.”—Mlaliki 3:1.

Mudziikire malire a nthawi imene muzithera polankhula pa foni, potumiza mauthenga a pa foni, kuonera TV, kapena kuchita masewera a pa kompyuta. Pofuna kusonyeza ulemu, muzithimitsa foni yanu mukakhala pa zochitika zofunika monga pa misonkhano ya ku mpingo. Mukhoza kudzawerenga mauthenga a pa foni nthawi ina.

Musalole kuti foni, TV, kapena kompyuta zikudyereni nthawi imene mwakonza kuti mucheze ndi anzanu kapena achibale anu, nthawi yoti muwerenge, kapena yoti muchite zinthu zauzimu.—Aefeso 5:15-17; Afilipi 2:4.

3. Kodi ndikugwirizana ndi ndani ? “Musasocheretsedwe. Kugwirizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.”—1 Akorinto 15:33.

Muzigwiritsira ntchito foni kapena kompyuta polimbitsa ubwenzi wanu ndi anthu amene amakulimbikitsani kukhala ndi makhalidwe abwino.—Miyambo 22:17.

Musadzinamize. Dziwani kuti mudzatengera mfundo, kalankhulidwe ndi kaganizidwe ka anthu amene mumagwirizana nawo kudzera pa kompyuta, pa foni, TV, mavidiyo kapena pa Intaneti.—Miyambo 13:20.

4. Kodi ndikuwononga nthawi yambiri bwanji? “Muzitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.”—Afilipi 1:10.

Muziwerengetsera nthawi imene mumathera pa kompyuta, foni kapena TV.

Musamanyalanyaze zimene anzanu kapena makolo anu akunena zakuti mukuthera nthawi yambiri pa foni, TV, kompyuta kapena pa Intaneti.—Miyambo 26:12.

Pa nkhani yogwiritsa ntchito foni, TV, kompyuta kapena Intaneti mwanzeru, Andrew amene tinamutchula koyambirira uja, anati: “Kugwiritsa ntchito foni, TV, kompyuta kapena Intaneti kumasangalatsa ngati munthu ukuzigwiritsa ntchito kwa nthawi yochepa chabe. Ndimayesetsa kuti zinthu zimenezi zisandilepheretse kucheza ndi achibale kapena anzanga.”

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.mt1130.com.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Tasintha mayina ena m’nkhani ino.

[Bokosi/Zithunzi patsamba 25]

ZIMENE ACHINYAMATA ANZANU AMANENA

“Makolo anga ankandiuza kuti, ‘Iwetu umakonda kwambiri kugwiritsa ntchito foni ya m’manja. Mwina tingomatirira manja akowo kufoniyo.’ Poyamba ndinkaganiza kuti akungonena zocheza, koma kenako ndinaona kuti ndilidi ndi vuto. Masiku ano ndinachepetsa nthawi imene ndimathera polemba mauthenga pa foni, ndipo ndikuona kuti tsopano ndine wosangalala kwambiri.”

“Kale ndinkaganiza kuti nthawi iliyonse imene ndapeza mwayi wopita pa Intaneti, ndiyenera kupitapo n’kukawerenga mauthenga amene abwera. Zimenezi zinkachititsa kuti ndisamalembe homuweki komanso kuti ndisamawerenge mokwanira. Koma tsopano sindipitapita pa Intaneti, ndipo ndikumva ngati kuti chimtolo cholemetsa chimene chinali pamapewa panga, chachotsedwa. Chinsinsi chake chagona pa kuchita zinthu mosapitirira malire.”

[Zithunzi]

Jovarny

Mariah

[Bokosi patsamba 26]

“NDINKANGOKHALIRA KUCHEZA PA INTANETI”

“Zaka zingapo zapitazo banja lathu linasamukira kudera lina. Ndinkafuna kuti ndizichezabe ndi anzanga ndipo iwo anandiuza kuti ndilowe gulu lawo lomaika zithunzi pa Intaneti. Ndinaona kuti imeneyi ingakhale njira yabwino yopitirizira kucheza ndi anzangawo. Ndinkaganiza kuti palibe vuto lililonse limene lingakhalepo chifukwa ndizicheza ndi anthu oti ndikuwadziwa kale, osati achilendo.

“Poyamba zonse zinkayenda bwino. Kamodzi pa mlungu uliwonse ndinkapita pa Intaneti n’kumaona zithunzi za anzangawo n’kuthirirapo ndemanga pa zithunzizo. Ndinkawerenganso ndemanga zimene iwowo alemba zokhudza zithunzi zimene ineyo ndinkaikapo. Koma kenako ndinayamba kuthera nthawi yambiri pa zimenezi. Pasanapite nthawi zinafika poti nthawi zonse ndinkangokhalira pa Intaneti. Popeza ndinkakhala pa Intaneti nthawi yaitali, anzawo ena a anzangawo anayamba kundidziwa ndipo anandipempha kuti ndikhalenso mnzawo. Nthawi zambiri mnzako amakuuza kuti mnzake wina ndi wochezeka ndipo uyambe kucheza naye, ndipo umapezeka kuti wayambadi kucheza naye. Kenako umapezeka kuti uli ndi anzako 50 a pa Intaneti.

“Patapita nthawi ndinaona kuti nthawi zonse ndinkangoganizira zokhala pa Intaneti. Ngakhale nthawi imene ndinali pa Intanetipo ndinkangoganizira kuti ndibweranso liti kuti ndidzaone zinthu zatsopano zimene zaikidwapo komanso kuti ndikuyenera kuikapo zithunzi zatsopano. Ndikakhala pa Intanetipo, ndinkawerenga mauthenga ndiponso kuika zithunzi za vidiyo, ndipo mosadziwa ndinkapezeka kuti ndakhalapo maola ambirimbiri.

“Ndinakhala ndikuchita zimenezi kwa chaka chimodzi ndi theka, koma kenako ndinazindikira kuti ndayamba kukhala pa Intaneti mopitirira malire. Panopa ndimadziletsa kuti ndisamakhale nthawi yaitali pa Intaneti komanso ndimakonda kucheza pamasom’pamaso ndi anthu amene ndikudziwa kuti angandilimbikitse kukhala ndi makhalidwe abwino. Anzanga ena sakumvetsa chifukwa chimene ndasinthira koma ineyo ndikuona kuti zinthu sizinali bwino.”—Anatero Ellen, wazaka 18.

[Bokosi patsamba 26]

YESANI KUFUNSA MAKOLO ANU

Nthawi zina mungadabwe ndi zimene makolo anu anganene ngati mutakambirana nawo nkhani yokhudza zinthu zosangalatsa. Mtsikana wina dzina lake Cheryl anati: “Nthawi ina bambo anga ankaganiza kuti CD yanga inayake ili ndi nyimbo zoipa. Choncho, ndinawapempha kuti timvetsere limodzi CD yonseyo. Iwo anavomera. Kenako, anandiuza kuti akuona kuti ili bwino.”

Lembani pansipa funso limene inuyo mungakonde kufunsa makolo anu lokhudza kugwiritsira ntchito foni, TV, kompyuta kapena Intaneti.

[Bokosi patsamba 27]

MAWU KWA MAKOLO

Kodi mwana wanu amathera nthawi yambiri pa Intaneti? Kodi amatumiza ndi kulandira mauthenga ambirimbiri pa foni? Kapenanso kodi amamvetsera nyimbo pa wailesi yake ya MP3 kwa nthawi yaitali kwambiri kuposa nthawi imene amathera akucheza ndi inuyo? Ngati ndi choncho, kodi mungatani?

Mwina mungaganize kuti ndi bwino kungomulanda kompyuta, foni, kapena wailesiyo. Koma si bwino kuganiza kuti zinthu zonse zoterezi n’zoipa. N’kutheka kuti ngakhalenso inuyo mumagwiritsa ntchito zinthu zina zamakono zimene kunalibe pa nthawi ya makolo anu. Mwina mungamulande patakhala chifukwa chomveka. Koma nthawi zambiri ndi bwino kungomuphunzitsa kugwiritsa ntchito zinthu zimenezi mwanzeru komanso mosapitirira malire. Kodi mungachite bwanji zimenezi?

Patulani nthawi yokambirana ndi mwana wanuyo. Choyamba, muuzeni zimene zikukudetsani nkhawa. Chachiwiri, mvetserani zimene iye akunena. (Miyambo 18:13) Chachitatu, kambiranani naye mmene mungathetsere vutolo. Musachite mantha kumuikira malire. Komabe muyenera kuchita zinthu momuganizira. (Afilipi 4:5) Ellen amene tamutchula kale uja, anati: “Pa nthawi yomwe ndinali ndi vuto lomangotumizira anzanga mauthenga pa foni, makolo anga sanandilande foniyo, koma anangondiuza mfundo zoti ndizitsatira. Zimenezi zinandithandiza kuchepetsa kutumiza mauthenga pafoni, ngakhale pa nthawi yomwe iwo palibe.”

Koma bwanji ngati mwana wanu atanena kuti akuona kuti sakulakwitsa? Zikatero, musafulumire kuganiza kuti mwana wanuyo ndi wosamva. M’malomwake, lezani mtima ndipo m’patseni nthawi yoti aganizire nkhaniyo. N’kutheka kuti mumtima mwake akuona kuti zimene mukunena ndi zoona ndipo akhoza kusintha m’kupita kwa nthawi. Achinyamata ambiri ali ngati Hailey, yemwe anati: “Poyamba makolo anga atandiuza kuti ndimagwiritsa ntchito kompyuta mopitirira malire, ndinakwiya kwambiri. Koma kenako nditaiganizira mofatsa nkhaniyo, ndinaona kuti akunena zoona.”

[Chithunzi patsamba 27]

Kodi zipangizo zamakono zimakulamulirani kapena inuyo ndi amene mumazilamulira?