Buku Limene Mungathe Kulikhulupirira—Gawo 7
Buku Limene Mungathe Kulikhulupirira—Gawo 7
Zimene Baibulo Limanena Zokhudza Ufumu Womaliza Kulamulira Dziko Lonse
Ino ndi nkhani yomaliza pa nkhani 7 zotsatizana zimene zakhala zikulembedwa m’magazini a “Galamukani!” Nkhanizi zikufotokoza za maufumu 7 otchulidwa m’Baibulo amene akhala akulamulira dziko lonse. Cholinga cha nkhanizi n’kusonyeza kuti Baibulo ndi lodalirika komanso kuti linauziridwa ndi Mulungu. Cholinga chinanso ndi kusonyeza kuti uthenga wa m’Baibulo umatipatsa chiyembekezo chakuti mavuto onse amene ulamuliro wa anthu wabweretsa, adzatha.
NTHAWI imene tikukhalayi ndi yapadera komanso yofunika kwambiri. Nthawi imeneyi ndi imene ufumu womaliza wa nambala 7 wotchulidwa m’Baibulo ukulamulira dziko lonse. Ndipo ndi ufumu wokhawo umene Baibulo linautchula ngati ulosi, chifukwa maufumu enawo linawatchula atalamulira kale ndipo umodzi ukulamulira. Ponena za maufumu 7 amenewa, kapena kuti “mafumu,” Baibulo limati: “Palinso mafumu 7. Asanu agwa, imodzi ilipo, inayo sinafikebe. Koma ikafika, ikufunika kudzakhala kanthawi kochepa.” *—Chivumbulutso 17:10.
Pa nthawi imene mawu amenewa ankalembedwa, zaka zoposa 1,900 zapitazo, maufumu asanu pa maufumu 7 aja anali ‘atagwa.’ Maufumu amenewa ndi Iguputo, Asuri, Babulo, Mediya ndi Perisiya, komanso Girisi. Mawu akuti mfumu “imodzi ilipo,” ankanena za ufumu wa Roma. Koma ufumu umenewu sunali woti udzakhala mpaka kalekale. Kunafunika kubweranso ufumu, kapena kuti mfumu ina, koma ponena za mfumu imeneyi, ulosiwu unanena kuti: “[Mfumu] inayo sinafikebe.” Mogwirizana ndi zimene Baibulo linaloserazi, mfumu ya nambala 7 inayambadi kulamulira padziko lonse. Kodi ufumu umenewu ndi uti? Kodi udzalamulira mpaka kalekale? Ngati sudzalamulira mpaka kalekale, kodi udzatha bwanji? Baibulo limafotokoza zimene zidzachitikire ufumu umenewu.
Ulosi Wodalirika
Ufumu wa nambala 7 unayamba pamene dziko la England, lomwe linali kumpoto chakumadzulo kwa ufumu wa Roma, linayamba kukula mphamvu. Pofika m’zaka za m’ma 1760, dziko lapachilumba limeneli, linakhala Ufumu wamphamvu wa Britain. Ufumuwu unapitirizabe kukhala ndi mphamvu komanso chuma chambiri, ndipo m’zaka za m’ma 1800, dziko la Britain linali lolemera komanso lamphamvu kwambiri padziko lonse. Buku lina limati: “Ufumu wa Britain unali waukulu kwambiri kuposa ufumu wina uliwonse umene unakhalapo m’mbuyomu. Ufumuwu unali ndi anthu okwana 372 miliyoni, ndipo unatenga dera lalikulu loposa mahekitala 2.8 biliyoni.”
Koma pa nthawi ya nkhondo yoyamba “Mgwirizano Wapadera.”
yapadziko lonse (yomwe inayamba mu 1914 n’kutha mu 1918) dziko la Britain linapanga ubale wapadera ndi dziko la United States, lomwe poyamba linkalamulidwa ndi ufumu wa Britain. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Dziko lonse linayamba kulamulidwa ndi ufumu wa Britain ndi America. Mayiko amenewa akupitirizabe kulamulira dziko lonse mpaka pano, ndipo amagwirizana pa zinthu zambiri.—Onani bokosi lakutiUlosi umene umapezeka pa Chivumbulutso 17:10 umagwirizana ndi ulosi wina umene umapezeka m’buku la Danieli. Danieli analemba za “chifaniziro chinachake chachikulu kwambiri” chimene mfumu Nebukadinezara anaona m’masomphenya amene Mulungu anamuonetsa. (Danieli 2:28, 31-43) Danieli anauza mfumuyo kuti mbali zosiyanasiyana za chifanizirocho zinkaimira maufumu osiyanasiyana otsatizana, kuyambira ndi ufumu wa Babulo, womwe unkalamulira dziko lonse pa nthawiyo. (Maufumu awiri, wa Iguputo ndiponso wa Asuri, anali atalamulira kale). Tikawerenga zimene akatswiri a mbiri yakale amanena, timaona kuti zimagwirizana ndi zimene Baibulo limanena, kuti:
Mutu wagolide umaimira ufumu wa Babulo.
Chifuwa ndi manja zasiliva zimaimira ufumu wa Mediya ndi Perisiya.
Mimba ndi ntchafu zamkuwa zimaimira ufumu wa wakale wa Girisi.
Miyendo yachitsulo imaimira ufumu wa Roma.
Mapazi achitsulo chosakanikirana ndi dongo amaimira kusagwirizana kwa anthu pa nkhani za ndale ndi pa nkhani zina, pa nthawi imene ufumu wa America ndi Britain ukulamulira.
Lemba la Chivumbulutso 17:10, limasonyeza kuti ufumu wa nambala 7 ‘ukufunika kudzakhala kanthawi kochepa.’ Kodi nthawi imeneyi ndi yaitali bwanji? Kodi ufumu umenewu udzatha bwanji? Ndipo kodi n’chiyani chidzachitike pambuyo pake? Buku la Danieli limayankha mafunso amenewa.
Chiyembekezo Chodalirika
Atafotokoza za chifaniziro chimene tachitchula chija, Danieli analemba kuti: “Mwala unadulidwa kuphiri koma osati ndi manja a munthu. Mwalawo unamenya chifanizirocho kumapazi ake achitsulo chosakanizika ndi dongo ndipo unawapera.” (Danieli 2:34) Kodi zimenezi zinkatanthauza chiyani?
Danieli anapitiriza kuti: “M’masiku a mafumu [omaliza] amenewo, Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa ku nthawi zonse. Ufumuwo sudzaperekedwa kwa mtundu wina uliwonse wa anthu, koma udzaphwanya ndi kuthetsa maufumu ena onsewo [a padziko lapansi], ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.” * (Danieli 2:44, 45) Taonani mfundo zofunika izi:
1. Ufumu wamphamvu umenewu, womwe ukuimiridwa ndi mwala waukulu, ‘udzakhazikitsidwa’ ndi Mulungu, osati ndi ‘manja a anthu.’ N’chifukwa chake ufumu umenewu umatchedwa kuti Ufumu wa Mulungu.
2. Ufumu wa Mulungu “udzaphwanya” maboma onse a anthu, kuphatikizapo ufumu wa nambala 7. N’chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti maboma amenewa sadzafuna kugonjera ulamuliro wa Mulungu. Choncho Mulungu adzawagonjetsa pa nkhondo yaikulu imene idzamenyedwere kumalo ophiphiritsa otchedwa Haramagedo, kapena kuti Aramagedo. Baibulo limanena momveka bwino kuti nkhondo imeneyi idzakhudza “mafumu a dziko lonse lapansi.”—3. Mosiyana ndi maulamuliro a anthu amene sakhalitsa, Ufumu wa Mulungu “sudzawonongedwa ku nthawi zonse.” Ufumu umenewu udzalamulira padziko lonse lapansi.—Danieli 2:35, 44.
Ulosi wa pa Genesis 3:15 womwe tinautchula m’gawo 1 la nkhani zino, udzakwaniritsidwa mochititsa chidwi Mulungu akamadzawononga adani ake onse. Mbewu ya mkazi, yomwe ikuimira Yesu Khristu, idzaphwanya mutu wa njoka yophiphiritsa, yomwe imaimira Satana ndi mbewu yake. (Agalatiya 3:16) Mbewu ya Satana, imaphatikizapo anthu onse amene amatengera zochita zake zoipa ndiponso amene safuna kulamulidwa ndi Mulungu komanso Khristu.—Salimo 2:7-12.
Zimenezi zikutichititsa kudzifunsa funso lofunika kwambiri lakuti, ‘Kodi Satana ndi anthu ake adzawonongedwa liti?’ Kapena kuti, ‘Kodi “mwala,” umene umaimira Ufumu wa Mulungu, udzaphwanya liti maboma a anthu?’ Baibulo limayankha funso limeneli pofotokoza “chizindikiro” cha masiku otsiriza.—Mateyu 24:3.
“Chizindikiro” cha Masiku Otsiriza
Chizindikiro cha masiku otsiriza chikuphatikizapo zinthu monga nkhondo, “zivomezi zamphamvu,” ndiponso “njala” yoopsa. (Luka 21:10, 11; Mateyu 24:7, 8; Maliko 13:8) Komanso kuipa kwa makhalidwe a anthu ndi kusakonda Mulungu ndi mbali ya chizindikiro cha “masiku otsiriza.” (2 Timoteyo 3:1-5) Kodi zinthu “zonsezi” zikuchitika? (Mateyu 24:8) Inde zikuchitika, ndipo anthu ali ndi mantha kuti kutsogoloku kuchitika zotani. Nyuzipepala ina (The Globe and Mail) inati: “Ena mwa anthu amene amaonedwa kuti ndi anzeru pa nkhani za sayansi ndi chikhalidwe, akuchenjeza anthu kuti zinthu zafika poipa kwambiri ndipo zimenezi zikapitirira, palibe ngakhale munthu mmodzi amene angadzakhale ndi moyo.”
Anthu amenewa akunena zoona, kungoti akulakwitsa chinthu chimodzi: Anthu onse sadzatheratu padzikoli chifukwa Ufumu wa Mulungu udzalowererapo. Ponena za chizindikiro cha mapeto, Yesu Khristu anati: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.” (Mateyu 24:14) Kodi ulosi umenewu ukukwaniritsidwa bwanji?
Panopa, Mboni za Yehova zikulengeza za Ufumu wa Mulungu m’mayiko oposa 230. Ndipotu magazini yawo yofalitsidwa kwambiri imadziwika ndi dzina lakuti Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova ndipo dzina lakuti Yehova ndi dzina lenileni la Mulungu. (Salimo 83:18) Ntchito ya Mboni za Yehova yophunzitsa anthu Baibulo ikuthandiza anthu ambiri zedi kusiya moyo wawo wakale n’kukhala anthu amakhalidwe abwino komanso okonda mtendere, ngati mmene Mulungu amafunira. (1 Akorinto 6:9-11) Chifukwa cha zimenezi, anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse sakayikira zoti Mulungu adzawapulumutsa Ufumu wake ukamadzawononga anthu oipa.
Anthu amenewa adzaona ndi maso awo kukwaniritsidwa kwa pemphero lachitsanzo la Khristu, limene limatchedwanso kuti Pemphero la Ambuye. M’pempheroli muli mawu akuti: “Ufumu wanu Mateyu 6:10, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu) Kodi munayamba mwaganizirapo kuti zinthu zidzakhala bwanji padzikoli pakadzatsala anthu okonda Mulungu okhaokha? Malemba otsatirawa akuthandizani kumvetsa chifukwa chake uthenga umene ukulalikidwa padzikoli umatchedwa kuti “uthenga wabwino.”
udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.” (Chifuniro cha Mulungu Chikadzachitika Padziko Lapansi . . .
● Sikudzakhalanso nkhondo ndipo kudzakhala mtendere weniweni. “Yehova . . . akuletsa nkhondo mpaka kumalekezero a dziko lapansi. Wathyola uta ndi kuduladula mkondo. Ndipo watentha magaleta pamoto.” (Salimo 46:8, 9) “Anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.”—Salimo 37:11.
● Anthu onse adzakhala ndi chakudya chochuluka. “Padziko lapansi padzakhala tirigu wambiri. Pamwamba pa mapiri padzakhala tirigu wochuluka.”—Salimo 72:16.
● Anthu adzakhala ndi thanzi labwino. “Palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’”—Yesaya 33:24.
● Aliyense adzakhala ndi nyumba yabwino. “Iwo adzamanga nyumba n’kukhalamo. Adzabzala minda ya mpesa n’kudya zipatso zake. Sadzamanga wina n’kukhalamo. Sadzabzala wina n’kudya.”—Yesaya 65:21, 22.
● Mavuto onse adzatha. “Chihema cha Mulungu chili pakati pa anthu. . . . Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”—Chivumbulutso 21:3, 4.
Kodi mukufuna mudzaone malonjezo amenewa akukwaniritsidwa? Ngati ndi choncho, Mboni za Yehova zikukulimbikitsani kuti muziwerenga kwambiri Baibulo. Zimenezi zingakuthandizeni kuona umboni wowonjezereka wosonyeza kuti ulamuliro wankhanza wa anthu watsala pang’ono kutha. Mudzaonanso kuti Baibulo ndi buku limene mungathe kulikhulupirira chifukwa linauziridwa ndi Mulungu.—2 Timoteyo 3:16. *
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 4 Chifukwa chakuti maufumu amene amatchulidwa m’Baibulo ankalamulidwa ndi mafumu, maufumuwo amatchulidwanso kuti “mafumu.”—Danieli 8:20-22.
^ ndime 18 Mukafuna kudziwa zambiri zokhudza Ufumu wakumwamba wa Mulungu, onani mutu 8 ndi 9 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
^ ndime 35 Ngati mukufuna kuphunzira zinthu zambiri zokhudza Baibulo, kambiranani ndi Mboni za Yehova za m’dera lanu. Kapena lembani kalata pogwiritsa ntchito adiresi yoyenera pa maadiresi amene ali patsamba 5. Kapenanso mungapite pa malo athu a pa Intaneti pogwiritsa ntchito adiresi iyi: www.mt1130.com.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 17]
MGWIRIZANO WAPADERA
M’mwezi wa July 2010, pulezidenti wa dziko la America, Barack Obama, ndi nduna yaikulu ya dziko la Britain, David Cameron, anachititsa msonkhano wa atolankhani. Pamsonkhanowo, pulezidenti Obama anati: “Mfundo imeneyi ndi yosatsutsika. Mgwirizano umene ulipo pakati pa dziko la America ndi dziko la Britain ndi wapadera kwambiri. Takhala tikuchitira limodzi zinthu kuyambira kale kwambiri. Timayendera mfundo zofanana. . . . Ndipotu koposa zonse, ubale wathu umayenda bwino chifukwa chakuti timakonda zinthu zofanana. . . . Dziko la America ndi la Britain likamachitira zinthu limodzi, anthu athu, komanso anthu apadziko lonse lapansi, amakhala otetezeka kwambiri, ndipo zinthu zimawayendera bwino. Mwachidule tingati dziko la America lilibe dziko linanso limene limagwirizana nalo kwambiri kuposa dziko la Britain.”
[Chithunzi patsamba 16]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Babulo
Mediya ndi Perisiya
Girisi
Roma
Britain ndi America
[Chithunzi patsamba 18]
Baibulo limalonjeza kuti Ufumu wa Mulungu ukamadzalamulira, padziko lapansi padzakhala mtendere weniweni
[Mawu a Chithunzi patsamba 15]
Time line: Egyptian wall relief and bust of Nero: Photograph taken by courtesy of the British Museum; Persian wall relief: Musée du Louvre, Paris