Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Uchi wa Nyerere Chakudya cha M’chipululu

Uchi wa Nyerere Chakudya cha M’chipululu

Uchi wa Nyerere Chakudya cha M’chipululu

YUMINIYA, yemwe amakhala m’dera la kuchipululu ku Australia, anatitengera kumpoto kwa dera linalake lotchedwa Alice Springs n’cholinga chokationetsa nyerere zinazake zimene zimakhala ndi uchi. Titafika, iye anayamba kufufuza mofatsa mumchenga. Kenako anapeza una wa nyererezo pansi pa mtengo wa kesha.

Iye anakumba mpaka pansi kwambiri pamchengawo motsatira una wa nyererezo. Pasanapite nthawi yaitali, anakumba dzenje lakuya mita imodzi ndipo pakamwa pake panali papakulu, poti munthu n’kukwanapo. Ali m’dzenjemo, mayiyo anatiuza kuti: “Timatha kukumba nyererezi nthawi ina iliyonse, koma nthawi yozizira ndi yabwino kwambiri chifukwa kunja kumakhala kusakutentha kwambiri.” Ifeyo tinkangomuyang’anitsitsa mwachidwi pamene iye amaganizira za una woti atsatire. Iye anati: “Umafunika kudziwa una womwe ungapezeko chisa cha nyerere.”

Pasanapite nthawi, Yuminiya anapeza chisa cha nyererezo. Mkati mwake munali nyerere zokwana 20 ndipo iliyonse inali ndi kamimba kakakulu ngati tizipatso ta masawu. Mkati mwa kamimbaka munali modzaza timadzi tooneka tachikasu. Nyererezi zinangokakamira ku una wawo osasuntha chifukwa cha kulemera kwa mimba zawo. M’kanthawi kochepa, Yuminiya anatolera nyerere zokwana 100 kuchokera m’mauna osiyanasiyana. Kenako iye anati: “Uchi wa tinyerere timeneti ndi chimodzi mwa zakudya zokoma kwambiri zimene timadya m’chipululu muno.”

Timimba ta Uchi

Pali mitundu ya nyerere yopitirira 10,000 yomwe ndi yodziwika bwino. Koma nyerere zimene tikukambiranazi zili m’gulu la nyerere zochititsa chidwi kwambiri. Mosiyana ndi njuchi, zimene zimasunga uchi wake m’malesa, nyererezi zimasunga uchi wawo m’timimba ta nyerere zina pagulu lawo. Ndiyeno nyerere zina zonse zikasowa chakudya, zimangopita kukatunga uchiwo.

Nyererezi zikafuna kuika kapena kutunga uchi, zimamenyetsa tinyanga tawo pa kanyanga ka nyerere imene ikusunga uchiwo. Ndiyeno nyerere inayo imatsegula pakamwa pake n’cholinga choti kamimba ka uchi kaja katseguke. Kamimbaka kamakhala ndi chitseko chapadera chimene chimatha kutseguka kuti uchi utuluke kapena kutseka kuti uchiwo usatuluke. Pa zaka zingapo zimene nyererezi zimakhala ndi moyo, nyerere zinazo zimatha kudzaza kamimbako ndi uchi kapena kuudyamo wonse, ndipo zimachita zimenezi maulendo angapo.

Nyerere zosunga uchizo siziyendayenda. Izo zimakonda kukhala ku una, komwe zimakhala zotetezeka ku dzuwa komanso ku tizilombo tina tomwe timakonda kudya nyerere. Pofuna kudziteteza ku mabakiteriya ndi tizilombo tina tomwe timapezeka pansi pa nthaka, nyererezi zimatulutsa timadzi tinatake n’kudzipopera thupi lonse. Timadzi timeneti timapha tizilomboto.

Kodi uchi wa nyererezi umachokera kuti? Uchiwu umachokera ku timadzi timene timapezeka m’maluwa a mitengo ya kesha. Popeza kuti timadzi timeneti timatsekemera, tizilombo tinatake timayamwa timadziti. Kenako nyerere zimayamwa timadzi totsekemerato kuchokera kwa tizilomboto kapena kuchokera ku mitengo ija. Pomalizira penipeni, nyererezi zimakapereka timadzito kwa nyerere zosunga uchi zija. Popeza kuti nyerere zosunga uchizi sizifuna chakudya chambiri m’thupi mwawo, timadzi tambiri timangosungidwa m’timimba tawoto.

Ndiyeno kodi tizilombo tomwe timayamwa timadzi kuchokera ku mitengo ija timangogwira ntchito yabule? Ayi, chifukwa nyererezi sizitenga uchi wonse. Komanso, tizilomboto timatetezedwa ndi nyererezi kuti tisadyedwe ndi zilombo zina. Choncho, pa mgwirizano umenewu, palibe amene amadyera mnzake masuku pamutu, chifukwa aliyense amapindula.

Baibulo limati: “Pita kwa nyerere . . . ukaone mmene imachitira zinthu kuti ukhale wanzeru. Ngakhale kuti ilibe mtsogoleri, kapitawo, kapena wolamulira, imakonza chakudya chake m’chilimwe. Imasonkhanitsa zakudya zake pa nthawi yokolola.” (Miyambo 6:6-8) Mawu amenewa ndi oona chifukwa kunena zoona nyerere n’zochititsa chidwi. Zimagwira ntchito mogwirizana, mwadongosolo komanso mwakhama. Timachitanso chidwi tikaganizira za uchi wokoma kwambiri umene nyererezi zimapanga ngakhale kuti zimakhala m’chipululu.

[Chithunzi patsamba 11]

M’kamimba ka nyererezi mumakhala uchi wokoma kwambiri

[Mawu a Chithunzi patsamba 11]

Pages 10, 11, top: M Gillam/photographersdirect.com; page 11: © Wayne Lynch/age fotostock