Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Baibulo Lili ndi Uthenga Wotani?

Kodi Baibulo Lili ndi Uthenga Wotani?

Kodi Baibulo Lili ndi Uthenga Wotani?

● Baibulo ndi buku limene lakhala likufalitsidwa kwambiri kuyambira kalekale. Anthu a m’mayiko osiyanasiyana amaona kuti uthenga wake ndi wolimbikitsa ndiponso wopatsa chiyembekezo. Amaonanso kuti m’Baibulo muli malangizo othandiza pa moyo watsiku ndi tsiku. Komabe, anthu ambiri masiku ano sakulidziwa bwino Baibulo.

Kabuku kokongola ka mutu wakuti Kodi Baibulo Lili ndi Uthenga Wotani? kangakuthandizeni kumvetsa Baibulo. Zigawo ziwiri zoyambirira za kabukuka zimafotokoza za paradaiso amene Mulungu anaikamo anthu komanso zimene zinachitika kuti anthuwo asakhalenso m’paradaiso. Kenako kakufotokoza za cholinga cha Mlengi chobwezeretsa paradaiso kudzera mu Ufumu wake, womwe ndi boma lakumwamba lolamulidwa ndi Yesu Khristu.

Zigawo zina zapakati zikufotokoza za utumiki, zozizwitsa, imfa ndiponso kuukitsidwa kwa Yesu. Zigawozi zikufotokozanso za otsatira a Yesu oyambirira ndi mabuku amene analemba, omwe masiku ano ndi mbali ya Baibulo.

Kabuku ka zigawo 26 kameneka kakumaliza ndi mutu wabwino kwambiri wakuti, “Dziko Lapansi Lidzakhalanso Paradaiso.” Tsamba lomaliza la kabukuka lili ndi zithunzi zokongola ndipo mutu wake ndi wakuti: “Onani Uthenga wa M’Baibulo Mwachidule.” Tsamba limeneli likufotokoza mwachidule zinthu 7 zofunika kwambiri pa kukwaniritsidwa kwa cholinga cha Mulungu chokhudza dziko lapansi.

Ngati mukufuna kuitanitsa kabuku ka masamba 32 kameneka, lembani zofunika m’munsimu n’kutumiza ku adiresi yoyenera pa maadiresi amene ali patsamba 5 m’magazini ino.

□ Ndikupempha kuti munditumizire kabukuka.

□ Nditumizireni munthu kuti ayambe kuphunzira nane Baibulo kwaulere.