Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Mungachite Ngati Mwapezeka ndi Khansa ya M’mawere

Zimene Mungachite Ngati Mwapezeka ndi Khansa ya M’mawere

Zimene Mungachite Ngati Mwapezeka ndi Khansa ya M’mawere

MAYI wina dzina lake Conchita sankasonyeza zizindikiro zilizonse zoti ali ndi khansa. * Anali ndi zaka 40, ankaoneka wathanzi komanso analibe wachibale amene anadwalapo khansa ya m’mawere. Nthawi zonse akapita kokayezetsa matendawa, madokotala sankamupeza ndi vuto lililonse. Koma tsiku lina akusamba, anapeza kuti bere lake lili ndi chotupa. Atakayezetsa kuchipatala anapeza kuti ndi khansa. Conchita ndi mwamuna wake anasowa chochita dokotala akuwafotokozera zimene angachite.

Kale mzimayi akapezeka ndi khansa, chimene madokotala ankachita ndi kumuchita opaleshoni yochotsa bere lonselo, tinthu tinatake tokhala ngati totupa timene timapezeka kukhwapa ndi pachifuwa, komanso minyewa ya pachifuwa. Kenako ankamupatsa mankhwala amphamvu kwambiri amene ankamuchititsa kumva ululu kwa nthawi yaitali. M’pake kuti anthu ambiri ankaopa mankhwala a matendawa kuposa matenda enieniwo.

Kwa nthawi yaitali, ntchito yolimbana ndi matenda a khansa ya m’mawere yakhala yovuta kwambiri chifukwa chakuti pamafunika kuthana ndi zinthu zambiri nthawi imodzi. Choyamba, pamafunika kuthana ndi matendawo mwachangu. Chachiwiri, kuyesetsa kupewa opaleshoni yosafunikira komanso kuonetsetsa kuti mankhwala amene munthuyo akulandira sakubweretsa mavuto ena. Monga mmene zinalili ndi Conchita, masiku ano anthu amene amapezeka ndi khansa ya m’mawere amakhala ndi mwayi wosankha mankhwala komanso njira zosiyanasiyana zochizira matenda awo. * Ndipo kafukufuku wosiyanasiyana amene akatswiri achipatala akuchita komanso malipoti amene ofalitsa nkhani akulemba, akusonyeza kuti pali chiyembekezo chakuti njira yabwino kwambiri yochizira matendawa ipezeka. Akusonyezanso kuti m’tsogolo muno zidzatheka kudziwiratu ngati munthu angadwale matendawa kapena ayi, komanso zakudya zimene angamadye kuti asadwale matendawa.

Ngakhale kuti ntchito zachipatala zapita patsogolo, azimayi ambiri akumwalirabe ndi khansa ya m’mawere. * Kumayiko olemera a ku America ndi ku Ulaya n’kumene kuli chiwerengero chachikulu cha anthu odwala matendawa. Komabe chiwerengero cha anthu odwala matendawa chayamba kuchulukanso ku Asia ndi ku Africa. Ndipotu tikayerekezera chiwerengero cha anthu odwala ndi omwalira, ku Asia ndi ku Africa n’kumene anthu ambiri amafa ndi matendawa. Dokotala wina wa ku Africa, ananena kuti izi zili choncho chifukwa chakuti “matendawa amapezedwa mochedwa kwambiri. Anthu ambiri amabwera kuchipatala matendawa atakula kale.”

Matendawa amakonda kugwira anthu achikulire. Anthu pafupifupi 80 pa 100 alionse amene amapezeka ndi matendawa amakhala azaka zoposa 50. Koma chosangalatsa n’chakuti, khansa ya m’mawere ili ndi mankhwala. Pa azimayi 100 alionse amene anapezeka ndi khansa ya m’mawere zaka zisanu zapitazo khansayo isanafalikire, azimayi 97 adakali ndi moyo. Conchita panopa wakwanitsa zaka zisanu kuchokera pamene anapezeka ndi khansa.

Zoti Mudziwe Zokhudza Khansa ya M’mawere

Monga mmene zinalili ndi Conchita, nthawi zambiri anthu amatha kudziwa kuti ali ndi khansa ya m’mawere akapezeka ndi chotupa. Koma sikuti nthawi zonse munthu akapezeka ndi chotupa m’thupi mwake ndiye kuti ali ndi khansa. Akuti pa anthu 100 alionse amene apezeka ndi chotupa, anthu 80 amakhala ndi chotupa wamba.

Kuti khansa iyambe, zimakhala kuti selo lina lasokonekera ndipo selo limenelo limapanganso maselo ena osokonekera. Ndipo m’kupita kwa nthawi maselo onsewo amapanga chotupa. Kenako maselo amenewa amayamba kuwononga ziwalo zina m’thupi. Zotupa zina zimakula mwachangu, pamene zina zimatenga nthawi yaitali mwina zaka 10 kuti munthu azitulukire.

Kuti adziwe kuti Conchita ali ndi khansa, dokotala wake anapopa timadzi ta pachotupacho n’kukatiyeza. Dokotalayo anapeza kuti timadzito tinali ndi maselo a khansa. Choncho anamupanga opaleshoni yochotsa chotupacho komanso maselo ena owonongeka. Cholinga chinanso cha opaleshoniyo chinali kudziwa kuti khansayo yafika potani.

Pambuyo pa opaleshoni, odwala ambiri amapatsidwa mankhwala ena n’cholinga choti khansayo itheretu komanso kuti isafalikire thupi lonse. Maselo ena amene ali ndi khansa akhoza kuchoka pachotupa n’kudutsa m’magazi n’kukayamba kukula pamalo ena. Khansa ikafalikira ku ubongo, chiwindi, m’mafupa, kapena m’mapapo zimakhala zovuta kwambiri kuchira.

Conchita anamupatsa mankhwala amphamvu kwambiri opha maselo a khansa pamalo amene panatuluka chotupacho komanso m’thupi lonse. Komanso chifukwa cha mtundu wa khansa yake, iye ankamwa mankhwala oletsa maselo atsopano kuchita khansa.

Masiku ano achipatala apeza mankhwala osiyanasiyana a khansa amene amawapereka kwa munthu mogwirizana ndi msinkhu wake, thanzi lake, mtundu wa khansa yake komanso kukula kwa khansa yake. Mwachitsanzo, adokotala atayeza mayi wina dzina lake Arlette, anapeza kuti khansa yake yangoyamba kumene ndipo sinafalikire bere lonse. Choncho, anangomuchotsa chotupa chokhacho m’malo mochotsa bere lonselo. Mayi wina, dzina lake Alice, asanamuchite opaleshoni, anayamba ndi kuotcha chotupa chake ndi mankhwala kuti chotupacho chiphwere. Mayi wina, dzina lake Janice, anamuchotsa chotupa ndiponso kachotupa kachibadwa kamene kamapezeka pafupi ndi bere. Popeza kuti chotupacho chinalibe maselo a khansa, madokotala sanachotse totupa tachibadwa tambiri. Zimenezi zinathandiza kuti Janice apewe mavuto ena monga kutupa mkono, kumene nthawi zambiri kumachitika ngati munthu amuchotsa totupa tachibadwa tija.

Panopa madokotala akudziwa zambiri zokhudza mmene khansa ya m’mawere imafalikirira, koma iwo sakudziwabe chenicheni chimene chimachititsa kuti khansayo iyambe.

Kodi N’chiyani Chimayambitsa Matendawa?

Mpaka pano madokotala sakudziwa kwenikweni chimene chimayambitsa khansa ya m’mawere. Anthu ena amanena kuti madokotala amataya nthawi yaitali akufufuza njira zodziwira komanso zochizira matendawa chifukwa zimawabweretsera ndalama zambiri, koma sathera nthawi yokwanira akufufuza chimene chimayambitsa matendawa ndi mmene anthu angawapewere. Komabe asayansi atulukira zinthu zina zimene zingathandize kudziwa chimene chimayambitsa matendawa. Ena akuganiza kuti khansayi imayamba motere: Selo limodzi losokonekera limachititsa kuti maselo ena azichita zinthu mosokonekeranso. Mwachitsanzo, lingachititse kuti maselo enawo azichulukana kwambiri, aziukira ndi kuwononga ziwalo zina m’thupi, komanso kuwononga maselo amene amateteza thupi ku matenda.

Kodi maselo osokonekerawa amachokera kuti? Anthu ena amachita kubadwa nawo. Mwachitsanzo, pa azimayi 100 alionse, azimayi 5 kapena 10 amachita kubadwa nawo. Choncho, azimayi oterewa amatha kudzadwala khansa ya m’mawere nthawi inayake pa moyo wawo. Zikuoneka kuti nthawi zambiri, maselo abwinobwino amatha kuwonongedwa ndi zinthu zina monga kujambulidwa kuchipatala komanso mankhwala ena amphamvu. Koma zimenezi panopa n’zosatsimikizirika kwenikweni.

Akuti chinthu chinanso chimene mwina chimayambitsa mitundu ina ya khansa ya m’mawere ndi timadzi ta m’thupi timene mzimayi amatulutsa akakhala kuti watsala pang’ono kusamba. Choncho, mzimayi amatha kudzadwala khansa ngati anayamba kusamba adakali wamng’ono kwambiri kapena ngati wasiya kusamba mochedwerapo. Mzimayi amathanso kudwala khansayi ngati anayamba kubereka mochedwa kapena ngati sanaberekepo, kapenanso ngati amamwa mankhwala enaake amphamvu. Azimayi achikulire omwe ndi onenepa akhoza kudwala mosavuta matendawa chifukwa chakuti mafuta akachuluka m’thupi amachititsanso kuti timadzi ta m’thupi tija tichuluke. Zinthu zinanso zimene zimachititsa kuti mzimayi adwale matendawa ndi monga kuchuluka kwa timadzi tinatake ta m’thupi totchedwa insulin komanso kuchepa kwa timadzi tinatake tochedwa melatonin, timene thupi limatulutsa munthu akamagona. Vuto losowa timadzi timeneti limakhudza kwambiri anthu amene amagwira ntchito usiku.

Kodi madokotala adzatulukira njira yabwino kwambiri yochizira matenda a khansa ya m’mawere popanda wodwalayo kumva ululu kwambiri? Mwina zidzatheka chifukwa panopa akatswiri akufufuza njira zosiyanasiyana zabwino zochizira matendawa. Zina mwa njirazi zikuphatikizapo kugwiritsa ntchito chitetezo cha m’thupi komanso mankhwala oletsa khansa kufalikira m’mbali zosiyanasiyana za thupi. Pakali pano madokotala ayamba kale kugwiritsa ntchito njira zowathandiza kuti azitha kuunika malo okhawo amene ali ndi vuto.

Asayansi akuyesetsanso kuchita zinthu zina monga kumvetsa mmene khansa imafalikira, kuthana ndi maselo amene samva mankhwala, kudziwiratu maselo amene angadzayambitse khansa n’kuthana nawo, komanso kungolimbana ndi maselo okhawo amene ali ndi vuto.

Komabe, tiyenera kudziwa kuti nthawi yathu ino matenda ndi imfa sizingatheretu. (Aroma 5:12) Ndi Mlengi wathu yekha amene angathetseretu matenda. Koma kodi iye adzawathetsadi? Baibulo limanena kuti adzatero. Limanena kuti nthawi idzafika yoti “palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’” * (Yesaya 33:24) Imeneyi idzakhala nthawi yosangalatsa kwambiri.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Tasintha mayina ena m’nkhaniyi.

^ ndime 4 Galamukani! sisankhira munthu thandizo la mankhwala.

^ ndime 5 Khansa ya m’mawere imathanso kugwira amuna, ngakhale kuti zimenezi sizichitika kawirikawiri.

^ ndime 21 Mukafuna kumva zambiri zokhudza lonjezo limeneli, werengani buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Bukuli ndi lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Bokosi/Chithunzi pamasamba 24, 25]

ZIZINDIKIRO ZIMENE MUYENERA KUSAMALA NAZO

Kutulukira khansayi mwachangu n’kofunika kwambiri. Koma kafukufuku wina akusonyeza kuti zizindikiro zina zodziwira kuti munthu ali ndi khansa ya m’mawere, zimakhala zosalondola kwenikweni, makamaka kwa azimayi achitsikana. Nthawi zina zimenezi zingachititse kuti mzimayiyo apatsidwe mankhwala osayenera komanso akhale ndi nkhawa yosafunikira. Komabe, akatswiri azachipatala amalimbikitsa azimayi kuti azionetsetsa ngati mabere awo ali ndi kotupa kalikonse kachilendo. Zizindikiro zotsatirazi zingakuthandizeni kuzindikira mwachangu ngati muli ndi khansa ya m’mawere:

● Kotupa kalikonse pabere kapena kukhwapa

● Timadzi tilitonse (kupatulapo mkaka) totuluka kuchokera kunsonga ya bere

● Kusintha kwa khungu (mtundu wake kapena kulimba kwake)

● Kansonga ka bere kakafewa kapena kakalowa mkati mwachilendo

[Bokosi patsamba 25]

NGATI MWAPEZEKA NDI KHANSAYI

● Muziyembekezera kuti mungathe kukhala chaka chonse mukudwala komanso kulandira mankhwala.

● Ngati zingatheke, pezani dokotala wodziwa bwino ntchito yake, yemwe angatsatire zosankha zanu ndiponso kulemekeza mfundo za m’Baibulo zimene mumatsatira.

● Kambiranani ndi banja lanu za anthu amene muyenera kuwauza komanso nthawi yoyenera kuwauza. Zimenezi zingathandize kuti anzanuwo apeze njira zosonyezera chikondi chawo komanso kukupemphererani.—1 Yohane 3:18.

● Muziwerenga Baibulo, muzisinkhasinkha komanso kupemphera, n’cholinga choti musamakhale ndi nkhawa kwambiri.—Aroma 15:4; Afilipi 4:6, 7.

● Mungacheze ndi anthu amene anadwalapo matendawa n’cholinga choti akulimbikitseni.—2 Akorinto 1:7.

● Musamade nkhawa kwambiri ndi zimene zingadzachitike kutsogolo. Yesu ananena kuti: “Musamade nkhawa za tsiku lotsatira, chifukwa tsiku lotsatira lidzakhala ndi zodetsa nkhawa zakenso.”—Mateyu 6:34.

● Musamatope kwambiri ndipo muzionetsetsa kuti mukupuma mokwanira.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 26]

KUKAMBIRANA NDI DOKOTALA

● Yesetsani kuphunzira zinthu zina ndi zina zimene anthu amanena akamafotokoza za khansa.

● Musanakaonane ndi dokotala, lembani mafunso amene mungakamufunse ndiponso pemphani munthu woti akuperekezeni, kaya mwamuna wanu kapena mnzanu, n’cholinga choti azikalemba mfundo zofunika.

● Ngati dokotala wanena zinthu zimene simunazimvetse, mupempheni kuti afotokozenso.

● M’funseni dokotalayo ngati anathandizapo anthu amene anali ndi vuto ngati lanulo.

● Ngati zingatheke, pitani zipatala zingapo kuti mumve maganizo a madokotala angapo.

● Ngati zimene madokotalawo akunena zikutsutsana, onani kuti ndi dokotala uti amene amadziwa bwino matendawo. Apempheni madokotalawo kuti akambirane za vuto lanulo.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 27]

NGATI MANKHWALA AKUYAMBITSA MAVUTO ENA

Mavuto ena amene mankhwala a khansa angabweretse ndi monga nseru, kuthothoka tsitsi, kumva kutopa kwambiri, kuphwanya m’thupi, kumva kubayabaya m’manja, m’mikono, m’miyendo ndi m’mapazi komanso dzanzi, kapena kutuluka tizilonda pakhungu. Zinthu zotsatirazi zingachepetse mavuto amenewa:

● Muzidya zakudya zoyenera kuti thupi lanu likhale ndi chitetezo champhamvu.

● Muzilemba zinthu zimene zikukuchititsani kuti muzikhala wofooka komanso zakudya zimene mukudana nazo.

● Onani ngati mankhwala, masaji kapena kubaya thupi lanu ndi timasingano zingachepetse nseru ndi ululu.

● Muzichitako masewera olimbitsa thupi n’cholinga choti mukhale ndi mphamvu, musanenepe kwambiri komanso kuti thupi lanu likhale ndi chitetezo champhamvu. *

● Muzigona mokwanira koma muzidziwanso kuti kugona kwambiri kungachititse kuti muzimva kutopa.

● Muzionetsetsa kuti khungu lanu lisamakhale louma kwambiri. Musamavale zovala zothina. Muzisamba madzi otentha.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 57 Muyenera kufunsa dokotala wanu musanayambe kuchita masewera alionse olimbitsa thupi.

[Bokosi patsamba 28]

NGATI MNZANU KAPENA WACHIBALE ALI NDI KHANSA

Kodi mungatani ngati mnzanu kapena wachibale wapezeka ndi khansa? Mungachite bwino kutsatira mfundo ya m’Baibulo iyi: “Sangalalani ndi anthu amene akusangalala. Lirani ndi anthu amene akulira.” (Aroma 12:15) Musonyezeni munthuyo kuti mumamukonda. Mungachite zimenezi pomuimbira foni, kumulembera kalata kapena imelo, kumutumizira khadi, kapena kupita kukamuona. Mungapemphere naye komanso kumuwerengera malemba olimbikitsa. Mwachitsanzo, Beryl, yemwe mwamuna wake amayendera mipingo ya Mboni za Yehova, anati: “Musamamuuze za anthu amene anafa ndi khansa koma m’malomwake muzimuuza za anthu amene anachira.” Janice, yemwe anadwalapo khansa, anapereka malangizo akuti: “Nthawi zina ndi bwino kungomukumbatira, osalankhula chilichonse. Ngati iyeyo akufuna, akhoza kukuuzani zambiri za vuto lakelo.” Mkazi akapezeka ndi khansa, mwamuna wake ayenera kumutsimikizira kwambiri kuti amamukonda.

Geoff, yemwe mkazi wake anali ndi khansa, anati: “Masiku ena tinkasankha kuti tisakambe chilichonse chokhudza khansa. Mkazi wanga sankafuna ngakhale pang’ono kuti matenda akewo azitilepheretsa kuchita zinthu zina zofunika. M’malomwake tinkakambirana zinthu zosangalatsa zimene zachitika pa moyo wathu. Pa masiku amenewo tinkaiwaliratu za matendawo.”

[Bokosi patsamba 28]

ZIMENE ENA ANENAPO

Atangouzidwa Kuti Ali Ndi Matendawa

Sharon: Ndinaona ngati moyo wanga wasintha mwadzidzidzi. Ndinanena kuti: “Basi ndikumwalira.”

Pamene Ankavutika Kwambiri ndi Matendawa

Sandra: Ndinkavutika kwambiri ndi nkhawa kuposa mankhwala a matendawa.

Margaret: Nditamaliza mtundu wachiwiri wa mankhwala, ndinadziuza kuti, ‘Sindikufunanso mankhwala alionse.’ Koma ndinafunikabe kupitiriza kumwa mankhwalawo.

Zokhudza Anzawo

Arlette: Tinauza anzathu za vuto lathu kuti azitipempherera.

Jenny: Ndinkayamikira kwambiri anzanga akandimwetulira kapena akandipatsa moni.

Zimene Amuna Awo Anachita

Barbara: Ndinameta tsitsi langa lonse chifukwa ndinkadziwa kuti m’kupita kwa nthawi liyamba kuthothoka. Mwamuna wanga Colin, atandiona anati: “Ukuoneka bwino kwambiri!” Nthabwala ngati zimenezi zinkachititsa kuti ndizimva bwino.

Sandra: Ngakhale kuti kaonekedwe kanga kanasintha kwambiri, tonse tikayang’ana pagalasi, Joe ankaoneka kuti sanakhumudwe ndi mmene ndikuonekera.

Sasha: Mwamuna wanga Karl akamauza anzake za matenda anga, ankanena kuti: “Tili ndi khansa.”

Jenny: Geoff sanasiye kundikonda ndipo sanabwerere m’mbuyo pa nkhani ya zinthu zauzimu. Zimenezi zinkandilimbikitsa kwambiri.

[Chithunzi patsamba 27]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Maselo ogwidwa ndi khansa amachulukana mofulumira kwambiri komanso amalimbana ndi maselo ena

[Chithunzi]

Maselo abwinobwino ndiponso njira yodutsa mkaka

Selo logwidwa ndi khansa lili pamalo pake

Selo la khansa likulimbana ndi maselo ena

[Chithunzi patsamba 28]

Chinthu chofunika kwambiri kwa anthu odwala khansa ndi kuwakonda