Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingadziwe Bwanji Anzanga Enieni?

Kodi Ndingadziwe Bwanji Anzanga Enieni?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Ndingadziwe Bwanji Anzanga Enieni?

“Ndili ndi mnzanga dzina lake Cori, amene wandithandiza kudziwa zinthu zambiri. Ndikakhala naye, amandithandiza kudziwana ndi anthu ambiri, ndimachita zinthu zina zatsopano, ndipo timasangalala kulikonse kumene tingapite. Cori wandichitira zambiri pa moyo wanga.”—Anatero Tara. *

Kodi mukuona kuti n’zosatheka kupeza mnzanu ngati ameneyu? Ngati panopa mulibe mnzanu wotereyu, musadandaule chifukwa m’kupita kwa nthawi mudzamupeza. Nkhaniyi ingakuthandizeni kupeza anzanu odalirika.

‘NDIMACHEZA ndi anthu ambirimbiri koma pa anthu amenewa palibe amene ndinganene kuti ndi mnzanga weniweni.’ Mawu amenewa ananenedwa ndi mtsikana wina wazaka 21, dzina lake Shayna. Zimenezi zimachitikira kwambiri anthu amene amapeza anzawo pamalo ochezera a pa Intaneti. Mtsikana wina wazaka 22, dzina lake Serena, ananena kuti: “Mukhoza kukhala ndi mayina ambirimbiri a anzanu n’kumaoneka kuti ndinu wodziwika kwambiri, koma anthuwo atha kukhala kuti si anzanu odalirika.” *

Kodi inuyo mungasankhe chiyani pakati pa kucheza ndi anthu ambirimbiri ndi kukhala ndi anzanu ochepa koma odalirika? Ngakhale kuti zonsezi zili ndi ubwino wake, anzanu odalirika amakuthandizani pa mavuto komanso amakuthandizani kukhala ndi makhalidwe abwino. (1 Akorinto 16:17, 18) Gwiritsani ntchito mfundo zotsatirazi kuti muone ngati anzanu amene muli nawo ali ndi makhalidwe amene anzanu abwino ayenera kukhala nawo.

MNZANU WENIWENI AMAKHALA WODALIRIKA

“Ndinali ndi mnzanga amene ankandiuza zinsinsi zake, ndiye nanenso ndinayamba kumuuza zinsinsi zanga. Tsiku lina ndinamuuza kuti ndikukanika kugona tulo chifukwa cha mnyamata winawake. Koma ndinalakwitsa kwambiri chifukwa nthawi yomweyo anayamba kuuza anthu ena nkhaniyi.”—Anatero Beverly.

“Ndili ndi mnzanga Alan amene amati ndikamuuza chilichonse, sauzanso anthu ena.”—Anatero Calvin.

Kodi pa anthu awiriwa, ndi uti amene ali ndi mnzake wodalirika? Kodi ndi uti amene mungafune kumuuza zinsinsi zanu? * Baibulo limanena kuti “bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse.”—Miyambo 17:17.

Lembani pansipa mayina awiri a anzanu amene mumawaona kuti ndi odalirika kwambiri.

1 ․․․․․

2 ․․․․․

MNZANU WENIWENI AMADZIPEREKA KUTI AKUTHANDIZENI

“Munthu ukakhala ndi mnzako imafika nthawi yoti iye akuthandize kapena iweyo umuthandize. Mnzako weniweni amadziwa nthawi imene zinthu sizikukuyendera bwino ndipo amakuthandiza msangamsanga. Nayenso amadziwa kuti mulimonse mmene zingakhalire, iwenso udzamuthandiza.”—Anatero Kellie.

“Mmene mayi anga ankamwalira n’kuti nditapeza mnzanga winawake. Ngakhale kuti tinali tisanayambe kucheza kwambiri, tinakonza zoti tsiku lina tidzapite limodzi ku ukwati. Koma pa tsiku limeneli ndi pamenenso tinkakaika mayi anga m’manda. Ndinadabwa kwambiri kuti mnzangayo anabwera kumaliroko m’malo mopita ku ukwati. Zimenezi zinandisonyeza kuti iye ndi mnzanga weniweni.”—Anatero Lena.

Kodi ndi mnzanu uti amene amadzipereka kuti akuthandizeni? Mnzanu weniweni samangofuna “zopindulitsa iye yekha basi, koma zopindulitsanso wina.”—1 Akorinto 10:24.

Lembani m’munsimu mayina awiri a anzanu amene asonyeza kuti amadzipereka kuti akuthandizeni.

1 ․․․․․

2 ․․․․․

MNZANU WENIWENI AMAKUTHANDIZANI KUKHALA NDI MAKHALIDWE ABWINO

“Anzanga ena amayembekezera kuti ndizingogwirizana nawo pa chilichonse, ngakhale zinthu zotsutsana ndi mfundo zimene ndimatsatira komanso chikumbumtima changa. Ndimaona kuti anthu otere si anzanga enieni.”—Anatero Nadeine.

“Ine ndi mchemwali wanga timagwirizana kwambiri. Iye amandithandiza kuchita zinthu zimene ndimaona kuti sindingakwanitse komanso amandithandiza kuti ndizimasuka kucheza ndi anthu. Amandiuza zoona zokhazokha popanda kuopa kuti andikhumudwitsa.”—Anatero Amy.

“Pa nthawi yomwe zinthu sizinkandiyendera, anzanga enieni ankandipatsa malangizo osapita m’mbali, pamene ena ankangodikira kuti mavutowo ndithane nawo ndekha kapena ndingowanyalanyaza. Iwo ankachita zinthu ngati kuti zonse zili bwino.”—Anatero Miki.

“Ndili ndi mnzanga amene amadziwa bwino kwambiri zinthu zimene ndingakwanitse kuchita, ndipo amandilimbikitsa kuti ndiyesetse kukwaniritsa zolinga zanga. Iye nthawi zonse amandiuza chilungamo chokhachokha. N’chifukwa chake ndimamukonda.”—Anatero Elaine.

Kodi anzanu amadziwa zinthu zimene mungakwanitse kuchita panokha n’kukulimbikitsani kuzichita, kapena amangofuna kuti muzitsatira maganizo awo? Lemba la Miyambo 13:20 limati: “Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru, koma wochita zinthu ndi anthu opusa adzapeza mavuto.”

Lembani m’munsimu mayina awiri a anzanu amene amakuthandizani kuti mukhale ndi makhalidwe abwino.

1 ․․․․․

2 ․․․․․

Onaninso mayina a anzanu amene munalemba m’zigawo zitatu zapitazi. Ngati pali mnzanu wina amene dzina lake likupezeka m’zigawo zonse zitatu, ameneyo ndiye mnzanu weniweni. Komabe, ngati mukuona kuti palibe mnzanu aliyense amene dzina lake mungalilembe m’zigawo zonsezo, musakhumudwe. Pali anthu ambiri amene akhoza kukhala anzanu odalirika, ndipo m’tsogolomu mukhoza kupeza anzanu oterewa. * Panopa mungofunika kuyesetsa kukhala munthu wabwino. Mtsikana wina wazaka 20, dzina lake Elena, ananena kuti: “Ndimayesetsa kuchita chilichonse chimene anzanga akufunikira. Akafuna kuchita zinazake ndimawathandiza, akamalankhula ndimawamvetsera, akamalira ndimawatonthoza.”

N’zoona kuti kucheza ndi anthu ambiri n’kwabwino kusiyana ndi kumangocheza ndi anthu omweomwewo. (2 Akorinto 6:13) Koma kodi si bwino kukhalanso ndi anzanu enaake ochepa odalirika amene ‘angakuthandizeni pakagwa mavuto?’ (Miyambo 17:17) Mtsikana wina wazaka 20, dzina lake Jean, anati: “N’zoona kuti ndi bwino kudziwana ndi anthu ambiri. Komabe zimenezi zili ngati kukhala ndi zovala zambirimbiri zokongola koma zomwe zina sizingakukwaneni. Munthu amavala zovala zokhazo zimene zimamukwana. Ndi mmenenso zilili ndi anzanu, mumafunika kukhala ndi anzanu odalirika omwe ngati mutavutika, angakuthandizeni.”

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.mt1130.com.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Tasintha mayina ena m’nkhani ino.

^ ndime 5 Kuti mudziwe zambiri zokhudza malo ochezera a pa Intaneti, onani nkhani ya “Zimene Achinyamata Amadzifunsa” mu Galamukani! ya July ndi August 2011.

^ ndime 10 Koma dziwani kuti nthawi zina si bwino kusunga chinsinsi. Mwachitsanzo, ngati mnzanu wachita tchimo, ali ndi maganizo ofuna kudzipha kapena ngati wayamba khalidwe linalake lotayirira, muyenera kuuza anthu ena. Kuti mudziwe zambiri zokhudza nkhani imeneyi, onani Galamukani! ya December 2008, tsamba 19 mpaka 21, ndi Galamukani! ya May 2008, tsamba 26 mpaka 29.

[Bokosi patsamba 20]

CHIPHASO CHOPEZERA ANZANU ENIENI

1. Mukhale ndi anzanu ochepa koma abwino. “Ndi bwino kudziwana ndi anthu ambiri, komabe pamafunika kukhalanso ndi anzanu amene mungamagwirizane nawo kwambiri.”—Anatero Karen.

2. Muzidalirika. “Ndimafuna kuti anzanga akhale anthu okhulupirika komanso odalirika, ndiye inenso ndimayesetsa kuchita zomwezo.”—Anatero Evelyn.

3. Muzimuyamikira. “Ndikamagwirizana ndi mnzanga winawake, ndimamuyamikira pomutumizira khadi kapena mphatso.”—Anatero Kellie.

[Bokosi patsamba 20]

FUNSANI MAKOLO ANU

Kodi muli wachinyamata, munakumana ndi zotani pa nkhani ya anthu ocheza nawo? Kodi mnzanu winawake anakukhumudwitsanipo? Ndiye munaphunzirapo zotani? Kodi munali ndi anzanu enaake amene anali odalirika kwambiri? Kodi munawapeza bwanji?

[Bokosi patsamba 21]

CHINSINSI CHOKHALA NDI ANZANU ABWINO

Kuti mukhale ndi anzanu abwino, inuyo ndi anzanuwo muyenera kumayendera mfundo zofanana. Iwonso ayenera kukhala anthu okonda zinthu zauzimu komanso amakhalidwe abwino.

Chinanso, muyenera kudziwa kuti sikuti inuyo ndi anzanuwo mukufunikira kukhala ndi makhalidwe ofanana ndendende.

Ndipo nthawi zambiri kukonda zinthu zofanana sikofunika kwambiri. Mukhoza kukhala ndi mnzanu amene amakonda masewera osiyana ndi amene inu mumakonda komanso amene ali ndi luso losiyana ndi lanu.

Chenjezo: Pewani kumangocheza ndi anthu chifukwa chakuti mumakonda zinthu zofanana basi. Ngati mnzanuyo satsatira mfundo zimene inuyo mumatsatira, ubwenzi wanu sungapitirire komanso mukhoza kugwa m’mavuto.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 21]

ZIMENE ACHINYAMATA ANZANU AMANENA

“Ngati mumafuna kupeza anzanu abwino kwambiri, si bwino kuchulukitsa malamulo chifukwa iwo sangakwanitse kuchita zonse zimene mumafuna. Komanso ngati simutsatira mfundo iliyonse posankha anthu ocheza nawo, aliyense akhoza kukhala mnzanu, ndipo zimenezi si zabwinonso.”

“Anthu ena amangofuna kukhala ndi anzawo ambirimbiri pamalo awo ochezera a pa Intaneti koma saganizira zoti anzawowo ndi otani. Ngati mukufuna kukhala ndi anzanu abwino, ndi bwino kuganizira kwambiri za khalidwe lawo m’malo mongofuna kukhala ndi anzanu ambiri.”

“Ngati mnzanga akunena anthu ena miseche, ndimadziwa kuti akhozanso kundinena miseche. Zikatero ndimaona kuti ndi bwino kusiya kucheza naye. Mnzako wabwino sanena miseche.”

[Zithunzi]

Dominique

Lianne

Brieanne