Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Luso la Zopangapanga la Anthu a ku Russia

Luso la Zopangapanga la Anthu a ku Russia

Luso la Zopangapanga la Anthu a ku Russia

● Anthu ambiri akapita ku Russia amakonda kugula zinthu zimene anthu aluso la zopangapanga akumeneko amapanga, monga tizidole tinatake totchedwa matryoshka. Kale kwambiri, zinthu zimenezi zinkapangidwa kuchokera ku mitengo ndi anthu a m’midzi ya ku Russia. Zinthuzi zimapentedwa mwaluso kwambiri ndipo luso limeneli limatchedwa kuti khokhloma.

Kwa zaka zambirimbiri anthu a ku Russia akhala akudyera mbale, masipuni, makapu ndi zinthu zina zotero zopangidwa kuchokera ku mitengo zimene amazipenta mwaluso kwambiri. Pa zinthu zimenezi ankakonda kujambulapo zomera ndi nyama zosiyanasiyana. Ku Russia kunkapezeka midzi ina imene ntchito yawo inali kupanga zinthu zimenezi basi.

Anthuwa ankakonda kupanga zinthu zimenezi m’nyengo yozizira, yomwe imakhala yaitali kwambiri, chifukwa pa nthawi imeneyi ntchito yakumunda inkakhala itacheperapo. Kale kwambiri, mwina zaka zoposa 200 zapitazo, anthu a m’matawuni ndi m’midzi ina ku Russia ankapanga ndalama kwambiri chifukwa cha luso limeneli. Akuti pa nthawi ina anthu onse a m’mudzi wina wotchedwa Semënov anasiyiratu kulima n’kuyamba kupanga mbale, mabeseni, makapu, ndi masipuni. Zinthu zonse zimene iwo anapanga chaka chimodzi chokha zinakwana 2 miliyoni.

Anthu akufupi ndi tawuni ya Nizhniy Novgorod anatulukira njira yothandiza kuti penti ndi vanishi zisamachoke zikapakidwa pa zinthu zimene asema. Iwo anayamba kupanga penti ndi vanishi woti sangasungunuke ndi moto. Zinthuzo akazipaka penti kapena vanishi wotereyu ankaziika mu uvuni. Chinthu chooneka chasiliva amati akachiika mu uvuni, chinkatuluka chikuoneka chagolide. Njirayi imagwiritsidwabe ntchito masiku ano m’mafakitale a ku Nizhniy Novgorod.

Kuti zinthu zimene apanga zioneke zokongola kwambiri, amajambulapo mbalame, nsomba komanso maluwa ndi mitengo yosiyanasiyana zopezeka m’nkhalango za ku Russia. Amajambulaponso udzu, masamba a mitengo komanso zipatso, monga mphesa zamitundu yosiyanasiyana. Zinthu zimenezi amakonda kuzipaka penti yofiira, yakuda, yagolide, kapena yobiriwira. Masiku ano luso limeneli lafalikira m’mayiko ambiri, moti anthu a m’mayiko osiyanasiyana ali ndi mipando yojambulidwa mwaluso yosonyeza zinthu zosiyanasiyana za ku Russia.