Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungatani Kuti Mudziwe Mulungu Woona?

Kodi Mungatani Kuti Mudziwe Mulungu Woona?

Kodi Mungatani Kuti Mudziwe Mulungu Woona?

● Kuyambira kale kwambiri anthu akhala akufunafuna Mulungu woona. Zimenezi zachititsa kuti akhale ndi maganizo osiyanasiyana okhudza Mulungu. N’chifukwa chake masiku ano pali zipembedzo zambiri. Komano kodi mungatani kuti mudziwe Mulungu woona?

Buku lakuti Mankind’s Search for God lingakuthandizeni. Munthu wina wa ku Mexico, yemwe amalemba mabuku, anati: “Ngakhale kuti bukuli ndi laling’ono moti munthu akhoza kungoliika m’thumba, lili ndi mfundo zothandiza kwambiri. Bukuli litaikidwa mu laibulale pamodzi ndi mabuku ena osiyanasiyana okwana 90,000, munthu akhoza kusankha kuwerenga buku limeneli.”

Mukhoza kuitanitsa buku la masamba 384 limeneli polemba zofunika m’mizere ili m’munsiyi ndi kutumiza ku adiresi yoyenera pa ma adiresi amene ali patsamba 5 m’magazini ino.

□ Ndikupempha kuti munditumizire bukuli.

□ Nditumizireni munthu kuti ayambe kuphunzira nane Baibulo kwaulere.