Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | KULERA ANA

Zimene Mungachite Kuti Mwana Wanu Azikumverani

Zimene Mungachite Kuti Mwana Wanu Azikumverani

VUTO LIMENE LIMAKHALAPO

Tiyerekeze kuti munauza mwana wanu kuti azithimitsa foni yake ikakwana 10 koloko usiku. Koma nthawi zambiri mumamumva akulankhula pa foni 10 koloko itadutsa. Tiyerekezenso kuti munauza mwana wanu kuti ikamakwana 6 koloko madzulo azikhala atafika pakhomo. Koma nthawi zambiri akumafika pakhomo cha m’ma 7.

Choyamba, muyenera kudziwa chifukwa chimene mwana wanuyo samvera malamulo amene munakhazikitsa. Zimenezi zingakuthandizeni kudziwa mmene mungamuthandizire m’malo mongomuona kuti ndi wosamva.

ZIMENE ZIMACHITITSA

Kusapereka chilango. Ana ambiri achinyamata samvera dala malamulo a makolo awo chifukwa amangofuna kuona zimene makolo awo angachite akapanda kumvera. Mwachitsanzo, ngati kholo lanena kuti mwana aliyense wobwera mochedwa pakhomo azikwapulidwa, nthawi ina wachinyamata angachedwe dala kuti aone ngati makolo ake amukwapuledi. Kodi tinganene kuti mwana ameneyu ndi wosamva? Ayi. Chofunika kuchita pamenepa ndi kungopereka chilango chimene munanena kuti muzipereka mwana akafika mochedwa pakhomo. Ngati mutalephera kuchita zimenezi, mwana wanu wachinyamata angasiye kumvera malamulo anu chifukwa choona kuti simumapereka chilango.

Kuchulukitsa malamulo. Makolo ena amaikira ana awo malamulo ambirimbiri. Mwanayo akapanda kumvera malamulowo, makolowo amakwiya n’kumuwonjezera malamulo ena. Koma kawirikawiri zimenezi zimangowonjezera mavuto. Mukamapanikiza mwana wanu ndi malamulo ambirimbiri, amayamba kudana ndi lamulo lililonse limene mwamuikira. Kupanikiza mwana wanu ndi malamulo n’cholinga choti azikumverani tingakuyerekezere ndi kumasula nati yadzimbiri. Mukamaikakamiza imatha kuduka kapena mazinga amatha kunyenyeka. Njira yabwino ndi kupaka girisi kapena kuthira oyilo kuti ifewe.

Choncho, muyenera kupatsa mwana wanu chilango choyenera. Simuyenera kumpatsa chilango n’cholinga chofuna kumukhaulitsa, koma muzimpatsa chilango n’cholinga chomuthandiza kuti akhale ndi khalidwe labwino. Kodi mungachite bwanji zimenezi?

 ZIMENE MUNGACHITE

Muzipereka malamulo omveka bwino. Ana amafunika kudziwa malamulo amene ayenera kutsatira komanso chilango chimene mungawapatse akapanda kumvera. —Lemba lothandiza: Agalatiya 6:7.

Yesani izi: Lembani malamulo onse amene munakhazikitsa panyumba panu. Ndiyeno dzifunseni kuti: ‘Kodi sindinachulutse malamulowa? Kapena m’pofunika kuwonjezera? Kodi pali malamulo ena ofunika kuwachotsa? Kodi m’pofunika kusintha malamulo ena chifukwa chakuti mwana wanga wakula?’

Musamasinthesinthe. Achinyamata amasokonezeka akaona kuti mukuwalanga pa zinthu zimene nthawi ina atachita zomwezo simunawalange.—Lemba lothandiza: Mateyu 5:37.

Yesani izi: Muzipereka chilango chogwirizanadi ndi zimene mwanayo walakwitsa. Mwachitsanzo, ngati munamuuza mwana wanu kuti azikhala atafika pakhomo 6 koloko, iye n’kubwera m’ma 9 koloko usiku, mungam’patse chilango choti azibwera 5 koloko.

Muzikhala ololera. Mwana akayamba kuchita zabwino muzimuchotsera malamulo ena ndipo zimenezi zingasonyeze kuti ndinu ololera.—Lemba lothandiza: Afilipi 4:5.

Yesani izi: Kambiranani ndi mwana wanu malamulo amene munakhazikitsa. Mungam’patsenso mwayi woti asankhe yekha chilango chomwe akuona kuti n’choyenera akalakwitsa zinazake. Ana ambiri savutika kumvera malamulo ngati anapanga nawo malamulowo.

Muziwathandiza kukhala ndi makhalidwe abwino. Mukamaika malamulo, cholinga chanu chisamakhale choti mwanayo azingomvera malamulowo, koma kumuthandiza kuti akhale ndi chikumbumtima chabwino choti chizimuthandiza kudziwa chabwino ndi choipa. (Onani bokosi lakuti, “Athandizeni Kuti Akhale ndi Makhalidwe Abwino”)—Lemba lothandiza: 1 Petulo 3:16.

Yesani izi: Muzitsatira mfundo a m’Baibulo chifukwa muli “malangizo amene amathandiza munthu kuzindikira” komanso nzeru zake n’zothandiza kuti “munthu wosadziwa akhale wochenjera, kuti wachinyamata akhale wodziwa zinthu ndiponso kuti azitha kuganiza bwino.”—Miyambo 1:1-4.