GALAMUKANI! October 2014 | Kodi Mumaonera Chiyani Kuti Munthu Zikumuyendera?
Kodi ndi kungotsatira maloto anu? Kapena kuyesetsa kupeza chilichonse chimene mtima wanu ukufuna? Nanga kumatanthauza chiyani makamaka?
NKHANI YAPACHIKUTO
Kodi Mumaonera Chiyani Kuti Munthu Zikumuyendera?
Zimakhala zopanda phindu ngati munthu akungoganiza kuti zinthu zikumuyendera koma zisakumuyendera
NKHANI YAPACHIKUTO
Ndani Amene Mungati Zinthu Zikumuyenderadi?
Dziwani ngati mumatha kusiyanitsa ngati munthu zikumuyenderadi kapena ayi, pogwiritsa ntchito zitsanzo 4.
NKHANI YAPACHIKUTO
Kodi Mungatani Kuti Zinthu Zizikuyenderani Bwino?
Mfundo 5 zimene zingakuthandizeni kuti zinthu zizikuyenderani bwino.
Zochitika Padzikoli
Nkhani zake ndi monga: kuipa kopereka malowolo ochepa, zigawenga zapamadzi komanso mbalame zimene zimauluka mtunda wautali.
MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA
Mungatani Kuti Musamagonje Mukakumana ndi Mayesero?
Mwamuna komanso mkazi weniweni amatha kupewa mayesero. Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zinthu 6 zimene zingakuthandizeni kusagonja mukamayesedwa komanso kuti musakhale ndi nkhawa chifukwa chodziwa kuti mwagonja.
ANTHU NDI MAYIKO
Dziko la Belize
Dziko la Belize ndiye loyambirira kukhala ndi malo otetezera nyama za ngati akambuku ndipo ndi dziko lachiwiri lomwe lili ndi zomera za mtundu wa coral reef zazikulu kwambiri.
Alimi Odziwa Kusamalira Nkhalango
Mileme ya m’nkhalango, yomwe imadziwikanso kuti nkhandwe zouluka, imathandiza kuti nkhalango zisathe.
ZIMENE BAIBULO LIMANENA
Zifaniziro
Kodi Akhristu oyambirira ankagwiritsa ntchito zifaniziro polambira?
KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?
Miyendo ya Hatchi
N’chifukwa chiyani akatswiri sangathe kutengera miyendo yake?