Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | ACHINYAMATA

Mungatani Kuti Musamagonje Mukakumana ndi Mayesero?

Mungatani Kuti Musamagonje Mukakumana ndi Mayesero?

VUTO LIMENE LIMAKHALAPO

“Atsikana ena amandiuza kuti ndiwapatse nambala yanga ya foni komanso amandifunsira. Koma ineyo ndimakana ndipo ndimangochokapo. Komabe pansi pa mtima ndimaganiza kuti, ‘mwinadi ndikanam’patsa nambala yanga.’ Ndisaname, ena mwa atsikanawa ndi okongola kwambiri. Nthawi zina ndimadzifunsa kuti: ‘N’chifukwa chiyani ndikuwakana?’”—Carlos, * wazaka 16.

Kodi nanunso mumakumana ndi mayesero ngati amenewa? Ngati n’choncho, dziwani kuti n’zotheka kusagonja mukamayesedwa.

ZIMENE MUYENERA KUDZIWA

Kugonja pa mayesero kungachititse kuti mukhale ndi nkhawa chifukwa chodziwa kuti mwachita zolakwika

Aliyense amakumana ndi mayesero, ngakhale munthu wamkulu. Anthufe timakumana ndi mayesero osiyanasiyana. Mtumwi Paulo nayenso ankakumana ndi mayesero ngakhale kuti anali wamkulu. Iye analemba kuti: “Ndimasangalala kwambiri ndi chilamulo cha Mulungu, koma ndimaona chilamulo china m’ziwalo zanga chikumenyana ndi chilamulo cha m’maganizo mwanga n’kundipanga kukhala kapolo wa chilamulo cha uchimo chimene chili m’ziwalo zanga.” (Aroma 7:22, 23) Ngakhale kuti Paulo ankakumana ndi mayesero amenewa, iye sanagonje. Inunso mungathe kuchita chimodzimodzi. Zimenezi zingachititse kuti musakhale kapolo wa zilakolako za thupi lanu. (1 Akorinto 9:27) Kusagonja pa mayesero kungachititse kuti musamakhale ndi nkhawa yomwe munthu amakhala nayo akachita zolakwika. Kungachititsenso kuti mukhale ndi makhalidwe amene angadzakuthandizeni mukadzakula.

Zinthu zimene timamvetsera komanso kuonera zingapangitse kuti tigwere m’mayesero. Baibulo limanena za “zilakolako zaunyamata,” ndipo zilakolako zimenezi zimakhala zamphamvu. (2 Timoteyo 2:22) Koma zinthu monga mafilimu, mapulogalamu a pa TV, mabuku komanso nyimbo zimene amalonda amapanga, zimachititsa kuti achinyamata aziganiza kuti kuchita chiwerewere si kulakwa. Mwachitsanzo, m’filimu mukakhala kuti muli mnyamata ndi mtsikana omwe ali pa chibwenzi, penapake filimuyo imasonyeza anthuwo akugonana. Koma Baibulo limasonyeza kuti mwamuna komanso mkazi weniweni ndi amene amatha ‘kupewa zilakolako za thupi.’ (1 Petulo 2:11) Zimenezi zikusonyeza kuti inunso mungathe kupewa mayesero. Koma kodi mungachite bwanji zimenezi?

 ZIMENE MUNGACHITE

Muzidziwa zofooka zanu. N’kutheka kuti pali zinthu zina zimene mumaona kuti zingakugwetsereni m’mayesero mosavuta. Choncho mungachite bwino kumayesetsa kupewa zinthu zoterozo, chifukwa fisi amalowera pavunda khola.—Lemba lothandiza: Yakobo 1:14.

Muzidziwiratu zimene mungachite mutakumana ndi mayesero. Ganizirani malo komanso nthawi imene mungakumane ndi mayesero. Kenako ganizirani zimene mungachite kuti musagonje mukakumana ndi mayeserowo.—Lemba lothandiza: Miyambo 22:3.

Khalani ndi cholinga choti musagonje zivute zitani. Baibulo limanena kuti pamene Yosefe ankayesedwa kuti achite chiwerewere, ananena kuti: “Ndingachitirenji choipa chachikulu chonchi n’kuchimwira Mulungu?” (Genesis 39:9) Mawu akuti “ndingachitirenji” akusonyeza kuti Yosefe anatsimikiza mtima kupewa kuchita zoipa, zivute zitani. Kodi nanunso mumatero?

Muzicheza ndi anthu a makhalidwe abwino. Mungapewe mayesero ambiri ngati mutamacheza ndi ndi anthu a makhalidwe abwino. Baibulo limati: “Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru.”—Miyambo 13:20.

Muzipewa kuchita zinthu zomwe zingakulowetseni m’mayesero. Mwachitsanzo:

  • Muyenera kupewa kukhala nokhanokha ndi munthu yemwe si mwamuna kapena mkazi mnzanu.

  • Pewani kugwiritsa ntchito Intaneti pa nthawi komanso malo amene angapangitse kuti muonere zolaula.

  • Pewani kucheza ndi anthu amene amalankhula komanso kuchita zoipa. Anthu oterewa angakupangitseni kuti muyambe kuona kuti si kulakwa kuchita zoipa.

Kodi ndi mfundo ziti zimene mukufuna muzitsatira, zomwe zingakuthandizeni kuti musagonje mukamayesedwa?—Lemba lothandiza: 2 Timoteyo 2:22.

Muzipempha Mulungu kuti akuthandizeni. Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Pempherani kosalekeza kuti musalowe m’mayesero.” (Mateyu 26:41) Zimenezi zikusonyeza kuti Yehova Mulungu amafuna kuti musagonje mukamayesedwa ndipo ndi wokonzeka kukuthandizani kuti mukwanitse kuchita zimenezi. Baibulo limanena kuti Mulungu “sadzalola kuti muyesedwe kufika pamene simungapirire, koma pamene mukukumana ndi mayeserowo iye adzapereka njira yopulumukira kuti muthe kuwapirira.”—1 Akorinto 10:13.

^ ndime 4 Si dzina lake lenileni.