Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

ZOCHITIKA PADZIKOLI

Nkhani Zokhudza Zipembedzo

Nkhani Zokhudza Zipembedzo

Zipembedzo ziyenera kuthandiza anthu kukhala ogwirizana. Koma n’zomvetsa chisoni kuti zipembedzo zimapangitsa kuti anthu azikangana komanso kuti asamakhulupirirane.

Padziko Lonse

Anthu ambiri amakhala m’mayiko omwe muli malamulo okhwima okhudza zipembedzo. Malamulowa anawakhazikitsa chifukwa cha mfundo zandale komanso chifukwa cha kusagwirizana kwa anthu. M’zaka 5 zapitazi, chiwerengero cha mayiko amene anthu ake amazunzidwa chifukwa choti ali m’zipembedzo za anthu ochepa, chinawonjezeka kwambiri.

TAGANIZIRANI IZI: Kodi ndi zinthu ziti zomwe zimapangitsa anthu ena kuti azidana ndi zipembedzo?—Mateyu 23:27, 28; Yohane 15:19.

England

A Tony Blair omwe anali nduna yaikulu ku England analemba m’nyuzipepala ina kuti zinthu zambiri zomwe zigawenga zikuchita, “zikuchitika m’dzina la chipembedzo. Nkhondo zambiri zimene zikuchitika m’zaka za m’ma 2000 zino, siziyamba pa zifukwa zandale ngati mmene zinalili m’ma 1900. Zambiri zikuchitika chifukwa cha kusagwirizana pa nkhani za chikhalidwe komanso zipembedzo.”—Observer.

TAGANIZIRANI IZI: N’chifukwa chiyani nthawi zambiri zipembedzo zimapangitsa kuti anthu asamagwirizane?—Maliko 7:6-8.

Australia

Kafukufuku wina anasonyeza kuti ku Australia, munthu mmodzi pa 5 alionse amanena kuti alibe chipembedzo. Komanso “anthu ambiri amene ali ndi chipembedzo, sapitako nthawi zonse komanso sachita nawo zinthu zambiri zokhudza chipembedzo chawocho.” Kafukufukuyu anasonyeza kuti amuna 15 okha pa 100 alionse komanso akazi 22 okha pa 100 alionse, ndi amene amalimbikira kuchita nawo zonse zokhudza chipembedzo chawo.

TAGANIZIRANI IZI: Kodi ndi makhalidwe ati oipa omwe anthu azipembedzo zambiri amachita?—Mateyu 7:15-20.