Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO

Kodi Kukhulupirira Zoti Kuli Mulungu N’kothandiza Bwanji?

Kodi Kukhulupirira Zoti Kuli Mulungu N’kothandiza Bwanji?

Anthu ambiri sadziwa ngati Mulungu alipo kapena ayi ndipo ena saona n’komwe kuti imeneyi ndi nkhani yofunika. Mwachitsanzo, Hervé yemwe anakulira ku France, anati: “Sindinganene kuti kuli Mulungu kapena kulibe, koma ineyo sindikhulupirira Mulungu. Ndimaona kuti ukhoza kumangogwiritsa ntchito nzeru zachibadwa n’kumachita zinthu bwinobwino popanda kukhulupirira zoti kuli Mulungu.”

Nayenso John, yemwe amakhala ku United States, anati: “Makolo anga sankakhulupirira zoti kuli Mulungu koma ineyo ndinalibe mbali. Komabe nthawi zina ndinkafuna kudziwa ngati kulidi Mulungu kapena ayi.”

Kodi nanunso munayamba mwaganizapo ngati Mulungu alipo kapena ayi? Komanso kuti ngati alipo, kodi n’kutheka kuti anali ndi cholinga polenga anthufe? Mwina mumaona kuti pali zinthu zina zomwe popanda kukhulupirira kuti kuli Mulungu, n’zovuta kuzimvetsa. Zinthu zake ndi monga umboni woti zamoyo sizinachokere ku zinthu zopanda moyo komanso woti dzikoli lili ndi zonse zofunika ku zinthu zamoyo.—Onani bokosi lakuti, “ Umboni Woti Kuli Mulungu.”

Kudziwa zoona pa nkhani zimenezi kungakuthandizeni kwambiri. Ndipotu mutapeza umboni wosatsutsika woti Mulungu alipo n’kudziwa zambiri za Mulunguyo, mungapindule kwambiri. Taonani mfundo 4 zotsatirazi.

1. MUNGAKHALE PA UBWENZI NDI MULUNGU

Ngati Mulungu anali ndi cholinga polenga anthufe, aliyense angafune atachidziwa n’kudziwanso zoyenera kuchita. Choncho munthu amene sakudziwa kuti Mulungu alipo, sangathenso kudziwa chifukwa chake Mulungu analenga anthufe ndipo sangakhale naye pa ubwenzi.

Baibulo limati Mulungu ndi amene analenga zamoyo zonse. (Chivumbulutso 4:11) Kodi kudziwa zimenezi kungatithandize bwanji? Taonani zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi.

Pa zinthu zonse zimene Mulungu analenga, anthu ndi apadera kwambiri. Baibulo limati anthufe tinalengedwa m’chifaniziro cha Mulungu kuti tizisonyeza makhalidwe ake. (Genesis 1:27) Limaphunzitsanso kuti anthufe tingathe kukhala mabwenzi a Mulungu. (Yakobo 2:23) Palibe chinthu chaphindu kuposa kukhala bwenzi la Mulungu.

Kodi munthu angapindule bwanji ngati atakhala bwenzi la Mulungu? Anthu amene ali pa ubwenzi ndi Mulungu amatha kulankhula naye momasuka m’pemphero, n’kumuuza chilichonse. Ndipo Mulungu amamvetsera mapemphero awo komanso amawathandiza. (Salimo 91:15) Kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu kungatithandizenso kuti tizidziwa maganizo ake pa nkhani zosiyanasiyana ndipo tingapeze mayankho a mafunso ovuta amene timakhala nawo.

Munthu amene sakudziwa kuti Mulungu alipo, sangathenso kudziwa chifukwa chake Mulungu analenga anthufe ndipo sangakhale naye pa ubwenzi

2. ANGAKUTHANDIZENI KUTI MUZIKHALA NDI MTENDERE WAMUMTIMA

Anthu ena zimawavuta kukhulupirira Mulungu akaona mavuto amene akuchitika padzikoli. Amafunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani Mulungu, yemwe ndi wamphamvuyonse, amalola kuti zoipa zizichitika?’

Baibulo limanena kuti cholinga cha Mulungu sichinali choti anthufe tizivutika. Adamu atalengedwa, sankakumana ndi mavuto alionse. Komanso Mulungu sanalenge anthu kuti m’kupita kwa nthawi adzafe. (Genesis 2:7-9, 15-17) Kodi mukuganiza kuti zimenezi ndi zoona kapena ndi nkhambakamwa chabe? Mulungu ndi wamphamvuyonse komanso khalidwe lake lalikulu ndi chikondi. Choncho n’zosakayikitsa kuti polenga anthufe, ankafuna kuti tizikhala mosangalala.

Koma kodi mavuto onsewa anayamba bwanji? Baibulo limasonyeza kuti Mulungu analenga anthu ndi ufulu wosankha zochita. Iye sanatilenge ngati maloboti kuti tizingochita chilichonse chomwe akufuna. Makolo athu oyambirira anagwiritsa ntchito ufulu wosankhawu molakwika ndipo anasankha kuti asamatsogoleredwe ndi Mulungu. (Genesis 3:1-6, 22-24) Ndiye chifukwa choti ndife ana awo, tonse timakumana ndi mavuto chifukwa cha kusamvera kwawo.

Kudziwa kuti mavuto amene timakumana nawowa sichinali cholinga cha Mulungu polenga anthu, kungakuthandizeni kuti muzikhala ndi mtendere wamumtima. Komabe tonsefe tikakumana ndi mavuto timafuna kulimbikitsidwa. Timafunanso kukhala ndi chiyembekezo cham’tsogolo.

3. ANGAKUTHANDIZENI KUKHALA NDI CHIYEMBEKEZO

Adamu ndi Hava atangochimwa, Mulungu analonjeza kuti cholinga chake polenga anthu chidzakwaniritsidwa. Popeza iye ndi wamphamvuyonse, palibe chimene chingalepheretse cholinga chakechi. (Yesaya 55:11) Posachedwapa, Mulungu athetsa mavuto onse amene anabwera chifukwa cha kusamvera kwa makolo athu. Kenako anthu adzayamba kukhala ndi moyo wosangalala komanso dzikoli lidzakhala paradaiso.

Kodi ndi zinthu ziti zosangalatsa zomwe zidzachitike padzikoli? Taonani malonjezo awiri opezeka m’Baibulo awa.

  • PADZIKO LONSE PADZAKHALA MTENDERE NDIPO OIPA ADZAWONONGEDWA. “Patsala kanthawi kochepa, woipa sadzakhalakonso. Udzayang’ana pamene anali kukhala, ndipo sadzapezekapo. Koma anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.”—Salimo 37:10, 11.

  • SIPADZAKHALANSO MATENDA NDI IMFA. “Palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’” (Yesaya 33:24) “Iye adzameza imfa kwamuyaya ndipo Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, adzapukuta misozi pankhope zonse za anthu.”—Yesaya 25:8.

N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira malonjezo amenewa? N’chifukwa choti pali maulosi ambirimbiri omwe analembedwa m’Baibulo ndipo anakwaniritsidwa ndendende. Koma mwina mungaganize kuti ngakhale kuti tili ndi chiyembekezo choti zinthu zidzakhala bwino m’tsogolo, panopa timakumanabe ndi mavuto. Ndiye kodi Mulungu amatithandiza bwanji panopa?

4. ANGAKUTHANDIZENI MUKAFUNA KUSANKHA ZOCHITA KOMANSO MUKAKHALA NDI MAVUTO

Mulungu amatipatsa malangizo amene angatithandize tikakumana ndi mavuto komanso kuti tizisankha zinthu mwanzeru. Zosankha zina zimakhala zing’onozing’ono. Koma nthawi zina timafunika kusankha zinthu zomwe zingakhudze moyo wathu wonse. Palibe munthu amene angatipatse malangizo anzeru kuposa Mlengi wathu. Izi zili choncho chifukwa ndi amene anatilenga komanso amadziwa mavuto amene tingakumane nawo ngati titasankha molakwika. Choncho tinganene kuti Mulungu amadziwa zimene tingachite kuti zinthu zizitiyendera bwino.

Mulungu anagwiritsa ntchito anthu kulemba Baibulo ndipo anthuwa analemba maganizo ake mothandizidwa ndi mzimu woyera. Choncho tingadziwe maganizo a Mulungu ngati titamawerenga Baibulo. N’chifukwa chake limati: “Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino, amene ndimakuchititsani kuti muyende m’njira imene muyenera kuyendamo.”—Yesaya 48:17, 18.

Mulungu ali ndi mphamvu zopanda malire ndipo ndi wokonzeka kugwiritsa ntchito mphamvu zakezo potithandiza. Baibulo limanena kuti Mulungu ali ngati bambo wachikondi amene amafunitsitsa kutithandiza. Limati: “Atate wakumwamba . . . adzapereka mowolowa manja mzimu woyera kwa amene akum’pempha.” (Luka 11:13) Choncho Yehova angagwiritse ntchito mzimu wake potitsogolera ndi kutithandiza.

Ndiye kodi mungatani kuti Mulungu akuthandizeni ndi mzimu wake woyera? Baibulo limati: “Aliyense wofika kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti iye alikodi, ndi kuti amapereka mphoto kwa anthu omufunafuna ndi mtima wonse.” (Aheberi 11:6) Kuti munthu asamakayikire zoti kuli Mulungu ayenera kufufuza umboni wosonyeza kuti Mulungu alipodi.

PHUNZIRANI BAIBULO KUTI MUDZIWE ZAMBIRI ZOKHUDZA MULUNGU

Pamatenga nthawi kuti munthu adziwe zoona zokhudza Mulungu. Koma kuchita zimenezi kungakuthandizeni kwambiri. Xiujin Xiao anabadwira ku China koma panopa amakhala ku United States. Iye ananena kuti: “Ndinkakhulupirira kuti zinthu zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina. Komabe ndinkafuna nditadziwa zambiri zokhudza Baibulo. Choncho ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova. Nditafika chaka chomaliza kukoleji ndinasiya kuphunzira Baibulo chifukwa ndinkatanganidwa kwambiri. Koma nditasiya kuphunzirako, sindinkasangalala kwenikweni. Patapita nthawi ndinayambiranso kuphunzira Baibulo ndipo ndinayambanso kukhala wosangalala.”

Kodi mungakonde kudziwa zambiri zokhudza Yehova Mulungu yemwe anatilenga? Tikukulimbikitsani kuti muphunzire Baibulo kuti mudziwe zambiri zokhudza Mulungu ameneyu.