“Mulungu Akutithandiza Kuti Tiiwale Zakale”
PA 1 SEPTEMBER, 2004, mayi wina dzina lake Natalya, ndi mwana wake wamwamuna wazaka 9 dzina lake Aslan, anali muholo yochitira masewera olimbitsa thupi ya pasukulu ina. Pafupi ndi iwowo panali mayi wina dzina lake Zarina ndi mwana wake wamkazi wazaka 12 dzina lake Anzhelika. Muholoyi munalinso ana ndi anthu ena akuluakulu oposa 1,000. Anthuwa anali m’manja mwa zigawenga. Kodi anapezeka bwanji m’manja mwa zigawengazo?
Tsikuli linali Lachitatu, ndipo m’mawa wa tsiku limeneli ana ndi makolo awo anasonkhana panja pa sukulu ya anawa. Ankakonzekera kuti achite mwambo wotsegulira teremu yatsopano. Sukuluyi ili m’tauni ya Beslan, yomwe ili ku Alania, m’dziko la Russia. Mwadzidzidzi gulu la zigawenga zoposa 30 zonyamula mfuti linafika pamalowa n’kuyamba kukuwa komanso kuwombera m’mwamba. Ana ndi makolo aja anachita mantha kwambiri. Gulu la zigawengali linauza anthuwo kuti akalowe muholo yochitira masewera olimbitsa thupi ya pasukuluyi. Anthuwa atalowa muholoyi, zigawengazo zinatchera mabomba kunja konse kwa holoyo.
Zinthu Zinafika Poipa Kwambiri
Kenako panafika gulu la asilikali a boma, koma sanayambe kulimbana ndi zigawengazo. Mayi Natalya, omwe pa nthawiyi ankaphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova ananena kuti: “Ndinapemphera kwambiri kuti Mulungu andithandize, ndipo aka kanali koyamba kuti ndipemphere kwambiri chonchi.”
Inali nthawi yotentha, choncho muholomo munkatentha kwambiri. Anthuwa anakhala muholo momwemo mpaka m’mawa wa tsiku lotsatira. Koma pa tsiku lachiwirili, zigawengazo zinasiya kuwapatsa chakudya ndi madzi. Pamene linkafika tsiku lachitatu, anthuwo anali atafookeratu ndi njala komanso ludzu. Choncho, anayamba kumwa mikodzo komanso kudya maluwa omwe ana anatenga kuti apereke kwa aphunzitsi awo ngati mphatso. Mayi Natalya anati: “Mnyamata wina amene ndinakhala naye pafupi anandipatsa tsamba la maluwa. Ndinalidula pakati n’kupereka hafu kwa Anzhelika ndipo hafu inayo ndinam’patsa Aslan.”
Koma chakumadzulo kwa tsiku lachitatuli, kunayambika chipwirikiti. Mayi Natalya anati: “Kunaphulika mabomba ndipo ine ndinagwa pansi. Muholomo munadzaza utsi ndipo asilikali a boma aja anayamba kuomberana ndi zigawengazo.” Kuomberanaku kuli mkati, Natalya ndi Aslan anayenda chokwawa n’kuchoka pakati pa gulu la anthu lija. Kenako, munthu wina wa kudera lomwelo, dzina lake Alan, anawakoka n’kupita nawo kumalo abwinoko. Koma anthu ambiri analephera kuthawa.
Zotsatira Zake
Ana komanso akuluakulu ambiri anafa, kuphatikizapo Anzhelika. Kwa milungu yambiri m’tauni ya Beslan munkamveka mfuu, anthu akulira maliro a abale awo. Aslan ankachitabe mantha chifukwa cha zomwe zinachitikazi. Nyumba ya Mayi Natalya ili pafupi ndi sukulu ija. Pafupi ndi nyumba yawo panamangidwanso sukulu ina, koma Aslan ankakana kupitako chifukwa cha mantha. Ankakananso kutuluka panja kukasewera ndi anzake. Mayi Natalya anati: “Tinapemphera kwa Yehova kuti amuthandize Aslan kuti asakhalenso ndi mantha.” Patapita nthawi Aslan anayambanso kupita kusukulu.
Nawonso Mayi Natalya ankachita mantha kupita ku Nyumba ya Ufumu kukasonkhana ndi a Mboni. Mayiwa anati: “Ndikakhala pagulu la anthu ambiri, ndinkaopa kuti kukhoza kubwera zigawenga n’kutigwira. Zimenezi zinkandichitikiranso ndikapita ku Nyumba ya Ufumu ndipo ndinkapemphera kuti kusabwere zigawenga. Koma ndinkachitabe mantha moti patapita nthawi ndinasiya kupita ku Nyumba ya Ufumu. Ndinkavutikanso maganizo ndikaganizira za anthu amene anaphedwa aja.”
Akuyesetsa Kuiwala Zakale
Mayi Natalya ananenanso kuti: “Ndikuthokoza a Mboni amene ndimasonkhana nawo chifukwa anandithandiza kwambiri. Mwachitsanzo, mayi wina dzina lake Tatyana, ankabwera kwathu pakatha masiku atatu alionse kudzandilimbikitsa. Tsiku lina anabwera ndi mayi ena a Mboni, dzina lawo a Ulyana. Mayiwa anali achifundo komanso ankalankhula mokoma mtima ndipo ankalidziwa bwino Baibulo. Ankandiyamikira chifukwa cha zabwino zimene ndinkachita ndipo ankandimvetsera ndikamalankhula.”
“Panopa ndimatha kufotokoza zimene zinatichitikira popanda kuchita mantha”
A Natalya ananenanso kuti: “Mayi Ulyana anandiwerengera mawu a mtumwi Paulo amene amapezeka pa 2 Akorinto 1:9. Chifukwa cha mavuto amene anakumana nawo ku Asia, Paulo anati: ‘Tinali kumva ngati talandira chiweruzo cha imfa.’ Anandiwerengeranso lemba la Yesaya 40:31 lomwe limati, ‘anthu odalira Yehova adzapezanso mphamvu. Iwo adzaulukira m’mwamba ngati ali ndi mapiko a chiwombankhanga.’ Malembawa komanso mawu olimbikitsa amene a Ulyana ndi a Mboni ena ankandiuza, anandithandiza kuti ine ndi ana anga tiyambirenso kupita ku Nyumba ya Ufumu. Komabe sikuti mantha aja anatheratu.”
Mayi Zarina nawonso anakhala a Mboni za Yehova ndipo akuyembekezera kudzakumananso ndi Anzhelika akadzaukitsidwa. Pa nthawi imeneyo, Ufumu wa Mulungu ndi umene uzidzalamulira dziko lonse lapansi ndipo padzikoli padzakhala mtendere. (Mateyu 6:9, 10; Machitidwe 24:15) A Natalya ndi ana awo anabatizidwa mu 2009. Amakhalabe pafupi ndi holo yomwe zigawenga zinawatsekeramo ija koma akuyesetsa kuiwala zimene zinawachitikirazi. Mayiwa anati: “Panopa ndimatha kufotokoza zimene zinatichitikira popanda kuchita mantha. Mulungu akutithandiza kuti tiiwale zakale.”