ZOMWE ANACHITA POLIMBANA NDI MAVUTO
Nkhani ya Ricardo ndi Andres
Maphunziro a m’Baibulo ali ndi mphamvu yotha kusintha makhalidwe a anthu. Mwachitsanzo, tiyeni tione zimene zinachitikira Ricardo ndi Andres.
RICARDO: Ndili ndi zaka 15, ndinalowa m’gulu la achinyamata ochita zauchigawenga. Zochita za anzangawa zinandilowerera kwambiri moti ndinali ndi cholinga choti ndidzakhale m’ndende kwa zaka 10. Mwinatu mukudabwa. Koma kwathuko anthu amene akhala m’ndende kwa nthawi yaitali, anthu ena ankawasirira komanso kuwalemekeza moti inenso ndinkafuna kukhala ngati iwowo.
Monga mmene zimakhalira ndi gulu lililonse la zigawenga, ineyo ndi anzangawo tinkachitanso zachiwawa, zachiwerewere komanso tinkapezeka ndi mankhwala osokoneza bongo. Usiku wina tinawomberana ndi gulu lina la zigawenga. Ndinkangoti basi ndiphedwa moti ndinabwerera lokumbakumba. Zimenezi zitachitika, ndinayamba kuganizira kwambiri za moyo wanga komanso tsogolo langa ndipo ndinaganiza kuti ndisinthe. Koma kodi ndikanakwanitsa bwanji kuti ndisinthe ndipo ndani akanandithandiza?
Achibale anga nawonso ankalimbana ndi mavuto ambiri moti sankakhala osangalala. Komabe ankolo anga ena anali ndi banja labwino kwambiri. Anali anthu abwino kwambiri ndipo ndinkadziwa kuti ankatsatira mfundo za m’Baibulo. Ndimakumbukira kuti nthawi ina anandiphunzitsapo kuti dzina la Mulungu ndi Yehova. Ndiye patangopita nthawi yochepa kuchokera pamene tinawomberana ndi zigawenga zija, ndinapemphera kwa Mulungu mochita kumutchula dzina kuti andithandize. Ndinadabwa kwambiri kuti tsiku lotsatira wa Mboni wina anagogoda pakhomo langa ndipo kenako anayamba kundiphunzitsa Baibulo.
Pasanapite nthawi ndinakumana ndi vuto lina lalikulu. Anzanga akale aja anayamba kumandiimbira foni kuti ndiyambirenso kucheza nawo. Komabe ndinakana ngakhale kuti sizinali zophweka. Ndinapitiriza kuphunzira Baibulo ndipo ndikusangalala kuti ndinasankha kuchita zimenezi. Moyo wanga unasintha kwambiri ndipo ndinayamba kukhala munthu wosangalala.
Ndikukumbukira kuti nthawi ina ndinapemphera kwa Yehova. Ndinamufotokozera kuti popeza ndinkafuna nditakakhala m’ndende kwa zaka 10, andilole kuti ndimutumikire kwa zaka zokwaniranso 10 kuti ndithandizenso ena ngati mmene ena anathandizira ineyo. Iye anayankhadi pemphero langa, moti ndakhala ndikuchita utumiki wanthawi zonse kwa zaka 17 tsopano ndipo ndingaonjezere kuti mpaka pano sindinamangidwepo.
Anzanga ambiri omwe ndinali nawo m’kagulu kaja panopa atha zaka zambiri ali m’ndende ndipo ena anafa. Ndikaganizira mmene moyo wanga unalili m’mbuyomu, ndimathokoza kwambiri banja la ankolo anga. Iwo ankalolera kukhala moyo wosiyana ndi ena onse chifukwa chotsatira mfundo za m’Baibulo. Panopa ndimawalemekeza kwambiri kuposa mmene ndinkalemekezera anzanga a m’kagulu kaja.
Koposa zonse, ndimathokoza kwambiri Mulungu chifukwa chondithandiza kukhala ndi moyo wabwino kwambiri.ANDRES: Ndinabadwira komanso kukulira m’dera linalake losauka. M’derali, kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, umbanda, kuphana komanso uhule zinali zofala kwambiri. Bambo anga anali chidakwa komanso ankagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo a cocaine. Nthawi zambiri iwowo ndi mayi anga ankakhalira kutukwanizana komanso kumenyana.
Ndinayamba kumwa mowa komanso kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo ndili wamng’ono. Nthawi zambiri ndinkapezeka m’misewu, kubera anthu komanso kugulitsa zomwe ndaba. Pamene ndinkakula bambo anga anandiphunzitsa mmene ndingamazembetsere komanso kugulitsa mankhwala osokoneza bongo ndi zinthu zina zoletsedwa ndi boma. Ngakhale kuti zimene ankandiphunzitsazi zinali zolakwika, iwo anachita zimenezi n’cholinga choti tizigwirizana. Tsiku lina kunyumba kwanga kunabwera apolisi kudzandigwira pamlandu wofuna kupha munthu ndipo kenako ndinagamulidwa kuti ndikakhale kundende kwa zaka 5.
Tsiku lina m’mawa kundendeko kunabwera a Mboni za Yehova ndipo tinamva chilengezo choitanitsa akaidi kuti tikaphunzire Baibulo. Ndinapitadi ku msonkhanowo ndipo zomwe ndinamva kumeneko zinandigwira mtima. Choncho ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi Amboni. Pondiphunzitsa sankabisa chilichonse ndipo anandithandiza kumvetsa mfundo za Mulungu zokhudza makhalidwe abwino.
Patapita kanthawi ndinaona kuti ndikufunika winawake kuti andithandize kusintha moyo wanga. Izi zinali choncho chifukwa akaidi anzanga omwe sankasangalala kundiona ndikuphunzira Baibulo, anayamba kundiopseza. Ndiye ndinapemphera kuti Mulungu andithandize kukhala wolimba mtima komanso kuchita zinthu mwanzeru ndipo anandithandizadi. Ndinkatha kulimba mtima n’kumauza akaidi ena zomwe ndinkaphunzira m’Baibulo.
Nthawi yoti nditulutsidwe itakwana, ndinachita mantha kuti ndikayambira pati ndikatuluka moti ndinkafuna kumangokhalabe kundendeko. Pamene ndinkanyamuka, akaidi angapo anandibayibitsa ndipo ena ankandiuza mokoma mtima kuti, “Yendani bwino abusa.”
Sindikudziwa kuti ndikanakhala munthu wotani ndikanapanda kulola kuti Mulungu andiphunzitse. Ndimathokoza kwambiri Mulungu kuti sanandione ngati munthu woti sindingathe kusintha. *
^ Kuti mupeze nkhani zina zosonyeza mmene Baibulo limasinthira anthu, pitani pawebusaiti ya jw.org. Pitani pomwe alemba kuti LAIBULALE, ndipo fufuzani nkhani za mutu wakuti “Baibulo Limasintha Anthu.”