MAVUTO A M’DZIKOLI
3 | Muziteteza Ubwenzi Wanu ndi Anzanu
CHIFUKWA CHAKE ZILI ZOFUNIKA
Mavuto a m’dzikoli akumachititsa kuti anthu ambiri azikhala ndi nkhawa. Chifukwa cha zimenezi, mosadziwa, anthu ena akumachita zinthu zosonyeza kuti sakonda anzawo.
-
Anthu ena amadzipatula kuti azichita zinthu paokha.
-
Anthu ena apabanja sakumachedwa kuyambana.
-
Chidwi cha makolo ena pa ana awo chachepa, pomwe ena sakumaganizira n’komwe nkhawa zimene ana awo amakhala nazo.
Zimene Muyenera Kudziwa
-
Kukhala ndi anzathu n’kwabwino, chifukwa amatithandiza kukhala ndi moyo wabwino komanso amatilimbikitsa makamaka pa nthawi imene takumana ndi mavuto.
-
Nkhawa zimene zimabwera chifukwa cha mavuto a m’dzikoli, zingachititse kuti musamagwirizane m’banja mwanu m’njira zimene simunkaziganizira.
-
Ana anu akamamvetsera pa wailesi kapena kuonera nkhani zoopsa pa TV, zingawasokoneze kwambiri.
Zimene Mungachite Panopa
Baibulo limanena kuti: “Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse, ndipo bwenzilo ndi m’bale amene anabadwira kuti akuthandize pakagwa mavuto.”—Miyambo 17:17.
Ganizirani za munthu amene angakuthandizeni komanso amene angakupatseni malangizo othandiza kenako m’pempheni. Kudziwa kuti winawake amakuganizirani kungakulimbikitseni kupirira mavuto amene mumakumana nawo.