Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tsankho Lidzatha

Tsankho Lidzatha

Anthu mamiliyoni ambiri amagwiritsa ntchito mfundo zimene takambirana munkhani zapitazi ndipo zawathandiza kuzula maganizo atsankho m’mitima mwawo. Komabe, anthufe sitingathetseretu mtima watsankho. Ndiye kodi tsankho lidzathadi padzikoli?

Tikufunikira Boma Labwino

Maboma a anthu alephera kuthetsa tsankho padzikoli. Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti palibe boma lomwe lingakwanitse kuthetseratu tsankho?

Kuti boma likwanitse kuthetsa tsankho liyenera

  1. 1. Kulimbikitsa anthu kuti asinthe maganizo komanso mmene amaonera anthu ena.

  2. 2. Kuthandiza anthu kuiwala mavuto amene anakumana nawo m’mbuyomo omwe amawachititsa kuti azivutika kuona anthu ena moyenera.

  3. 3. Kukhala ndi olamulira abwino omwe angalamulire anthu onse mwachilungamo.

  4. 4. Kugwirizanitsa anthu amitundu yonse.

Baibulo limanena kuti Mulungu anakhazikitsa boma lomwe lingakwanitse kuchita zimenezi. Boma limeneli limatchedwa “Ufumu wa Mulungu.”​—Luka 4:43.

Taonani zimene boma limeneli lidzachitire anthu.

1. Lidzaphunzitsa Anthu Makhalidwe Abwino

“Anthu okhala panthaka ya dzikolo adzaphunzira chilungamo.”—YESAYA 26:9.

“Ntchito ya chilungamo chenicheni idzakhala mtendere, ndipo zochita za chilungamo chenicheni zidzakhala bata ndi mtendere mpaka kalekale.”—YESAYA 32:17.

Kodi malembawa akutanthauza chiyani? Ufumu wa Mulungu udzaphunzitsa anthu kuti azichita zinthu zoyenera. Anthu akadzaphunzira kusiyanitsa zoyenera ndi zosayenera, komanso zachilungamo ndi zopanda chilungamo, adzayamba kuona anzawo moyenera. Aliyense adzazindikira kuti ayenera kumakonda anthu amitundu yonse.

2. Lidzathetsa Zinthu Zopanda Chilungamo

Mulungu “adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”—CHIVUMBULUTSO 21:4.

Kodi lembali likutanthauza chiyani? Ufumu wa Mulungu udzathetsa zopweteka zonse zomwe zimabwera chifukwa cha zinthu zopanda chilungamo. Zimenezi zidzathandiza kuti anthu omwe anachitiridwapo zopanda chilungamo asamadane ndi anthu amene anawachitira zopanda chilungamowo.

3. Wolamulira Wake Adzakhala Wabwino Kwambiri

“Sadzaweruza potengera zimene wangoona ndi maso ake, kapena kudzudzula potengera zimene wangomva ndi makutu ake. Adzaweruza mwachilungamo anthu onyozeka ndipo adzadzudzula anthu mowongoka mtima, pothandiza ofatsa a padziko lapansi.”​—YESAYA 11:3, 4.

Kodi lembali likutanthauza chiyani? Yesu Khristu, yemwe ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, azidzalamulira dziko lonse lapansi mwachilungamo komanso mosakondera. Yesu amakonda mitundu yonse mofanana ndipo adzaonetsetsa kuti anthu padziko lonse akutsatira malamulo ake olungama.

4. Lidzathandiza Kuti Anthu Onse Azigwirizana

Ufumu wa Mulungu udzathandiza anthu kukhala “ndi maganizo amodzi, ndi chikondi chofanana.” Udzawathandizanso kukhala “ogwirizana mu mzimu umodzi, ndi mtima umodzi.”—AFILIPI 2:2.

Kodi lembali likutanthauza chiyani? Anthu amene azidzalamuliridwa ndi Ufumu wa Mulungu azidzagwirizana kwambiri ndipo sazidzachita zimenezi mwachiphamaso. Anthu onse adzakhala “ogwirizana mu mzimu umodzi” chifukwa azidzakondana ndi mtima wonse.