Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI N’ZOTHEKA KUSINTHA ZOMWE MUNAZOLOWERA?

1 N’zosatheka Kusintha Lero ndi Lero

1 N’zosatheka Kusintha Lero ndi Lero

Nthawi zina munthu angamafune kusiya makhalidwe oipa nthawi imodzi. Mwina anganene kuti, ‘Mlungu uno ndikufuna kusiya kusuta, kutukwana komanso kugona mochedwa. Ndipo ndikufuna ndiyambe kuchita masewera olimbitsa thupi, kudya zakudya zopatsa thanzi ndiponso kuimbira foni achibale anga.’ Komatu ngati munthu atayeseradi kuchita zinthu zonsezi nthawi imodzi, palibe chomwe angakwanitse.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Nzeru zimakhala ndi anthu odzichepetsa.”Miyambo 11:2.

Munthu wodzichepetsa amangochita zimene angakwanitse. Amadziwa kuti sangakwanitse kuchita chilichonse chifukwa chosowa nthawi, mphamvu komanso zinthu zina. Munthu wotereyu amasintha zinthu pang’onopang’ono.

Munthu akamayesera kusintha zinthu zonse nthawi imodzi, palibe chomwe angakwanitse

ZIMENE MUNGACHITE

Muziyesa kaye kukwaniritsa chinthu chimodzi kapena ziwiri. Kuti zimenezi zitheke tayesani kuchita izi:

  1. Lembani zinthu zabwino zimene mukufuna kuzolowera kumachita komanso zinthu zoipa zomwe munazolowera ndipo mukufuna kuzisiya. Yesetsani kulemba zinthu zambiri ndithu.

  2. Polembapo muyambe ndi zinthu zomwe mukuona kuti ndi zofunika kwambiri.

  3. Ndiyeno pa zinthu zabwino ndi zoipa zimene munalemba zija, musankhepo chinthu chimodzi kapena ziwiri ndipo muziyesetsa kumachita zabwinozo komanso kusiya zoipazo. Zikatheka, yeserani zina mpaka zitathekanso.

Kuti musavutike kuzolowera, muzichita zinthu zabwino pa nthawi yomwe munkachita zinthu zoipa. Mwachitsanzo, ngati pa zinthu zomwe mukufuna kusiya munalembapo vuto loonera kwambiri TV, ndipo pa zinthu zomwe mukufuna mutamachita munalembapo kuti muziimbira foni achibale, mungalembe izi: ‘M’malo mongofikira kuyatsa TV ndikafika pakhomo, ndiziyamba kuimbira foni achibale.’