Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Kodi khonde la kachisi wa Solomo linali lalitali bwanji?
Pakhondeli ndi pomwe panali khomo lolowera ku Malo Oyera a kachisi. Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lomwe linafalitsidwa chisanafike chaka cha 2023, limanena kuti “khonde lakutsogolo linali mikono 20 mulitali ndipo linkafanana ndi mulifupi mwa nyumbayo. Kuchoka pansi kufika pamwamba, khondelo linali lalitali 120.” (2 Mbiri 3:4) Mabaibulo enanso amanena kuti khondeli linali lalitali “mikono 120” kutanthauza mamita 53 kupita m’mwamba.
Koma ponena za kachisi wa Solomo, Baibulo la Dziko Latsopano losindikizidwa mu 2023 limanena kuti khondelo “linali lalitali mikono 20” kutanthauza mamita 9. a Tiyeni tione zifukwa zimene zachititsa kuti pakhale kusinthaku.
Lemba la 1 Mafumu 6:3 silitchula kutalika kwa khondeli. Pavesili, Yeremiya analemba za mulitali ndi mulifupi mwa khondeli koma osati kupita m’mwamba. Ndiyeno muchaputala chotsatira, iye anafotokoza zinthu zina zambiri zokhudza kachisiyu monga zokhudza thanki yosungira madzi, zotengera 10 ndi zipilala ziwiri za kopa. (1 Maf. 7:15-37) Ngati khondelo linalidi lalitali mamita oposa 50 komanso lalitali kuposa kachisiyo, ndiye n’chifukwa chiyani Yeremiya sananene zimenezi? Ndiponso zaka zambiri pambuyo pake, olemba a Chiyuda sanasonyezeko kuti khondelo linali lalitali kuposa kachisi yense.
Akatswiri amakayikira kuti zipilala zazitali mikono 120 zingaime bwinobwino osagwa pamakoma a kachisiyo. Zipilala za miyala kapena njerwa zomwe zinkamangidwa kale zinkakhala zazikulu pansi n’kumachepa kumwamba. Chitsanzo ndi zipilala zomwe zinkakhala pamageti a kachisi ku Iguputo. Koma si mmene zinalili ndi kachisi wa Solomo. Akatswiri amanena kuti kukula kwa khoma lake sikunkapitirira mikono 6 kapena kuti mamita 2.7. Choncho Theodor Busink yemwe ndi katswiri wa mbiri ya zomangamanga ananena kuti: “Tikaganizira kukula kwa khomali n’zosatheka kuti zipilala za khondelo zikhale zazitali mikono 120.”
N’kutheka kuti analakwitsa pokopera mawu a palemba la 2 Mbiri 3:4. Ngakhale kuti mipukutu ina ili ndi “120” pavesili, mabuku ena odalirika monga Codex Alexandrinus la m’ma 400 C.E., komanso Codex Ambrosianus la m’ma 500 C.E. ali ndi “mikono 20.” Kodi mwina n’chiyani chomwe chinachititsa kuti wokoperayo alembe “120”? Mu Chiheberi, mawu amene anawamasulira kuti “handiredi” amafanana ndi mawu amene anawamasulira kuti “mikono.” Choncho n’kutheka kuti wokoperayo analemba “handiredi” m’malo molemba “mikono.”
N’zoona kuti timafuna kumvetsa mmene kachisi wa Solomo analili koma timaganizira kwambiri za kachisi wamkulu wauzimu amene ankaimiridwa ndi kachisi wa Solomo. Timayamikira kwambiri kuti Yehova waitana atumiki ake onse kuti azimulambira m’kachisi wamkuluyu.—Aheb. 9:11-14; Chiv. 3:12; 7:9-17.
a Mawu a m’munsi a palembali akusonyeza kuti “m’mipukutu ina muli ‘120,’ pomwe m’mipukutu ina ndi Mabaibulo ena muli ‘mikono 20.’”