NKHANI YOPHUNZIRA 25
Tizidalira Yehova Tikakhala ndi Nkhawa
“Ine ndine . . . wopsinjika maganizo.”—1 SAM. 1:15.
NYIMBO NA. 30 Atate Wanga, Mulungu Wanga Ndiponso Bwenzi Langa
ZIMENE TIPHUNZIRE *
1. N’chifukwa chiyani tiyenera kumvera chenjezo la Yesu?
MU ULOSI wake wokhudza masiku otsiriza, Yesu ananena kuti: “Samalani kuti mitima yanu isalemedwe ndi . . . nkhawa za moyo.” (Luka 21:34) N’chifukwa chiyani tiyenera kumvera chenjezoli? Chifukwa chakuti nafenso panopa timakumana ndi mavuto omwe aliyense amakumana nawo.
2. Kodi abale ndi alongo athu amakumana ndi mavuto otani?
2 Nthawi zina timakumana ndi mavuto ambiri pa nthawi imodzi. Tiyeni tione zitsanzo zingapo pa nkhaniyi. M’bale wina dzina lake John, * yemwe akudwala matenda enaake opha ziwalo, anadandaula kwambiri mkazi wake atamuthawa. Iwo anali atakhala m’banja kwa zaka 19. Kenako ana ake awiri anasiya kutumikira Yehova. M’bale wina dzina lake Bob ndi mkazi wake Linda nawonso anakumana ndi mavuto ena. Onse anachotsedwa ntchito ndipo sakanathanso kukhalabe m’nyumba imene ankakhala. Kuwonjezera pa mavutowo, Linda anapezeka ndi matenda a mtima komanso matenda ena owononga chitetezo cha m’thupi.
3. Malinga ndi Afilipi 4:6, 7, kodi sitiyenera kukayikira za chiyani?
3 Tisamakayikire kuti Atate wathu Yehova, yemwe anatilenga, amadziwa mmene mavuto amatikhudzira. Ndipo amafunitsitsa kutithandiza tikakumana ndi mavuto. (Werengani Afilipi 4:6, 7.) Mawu a Mulungu amafotokoza mavuto amene atumiki ake akale anakumana nawo. Amafotokozanso zimene Yehova anachita powathandiza. Tiyeni tikambirane zitsanzo zina.
‘ELIYA ANALI MUNTHU NGATI IFE TOMWE’
4. Kodi Eliya anakumana ndi mavuto otani, nanga n’chiyani chinamuthandiza?
4 Eliya ankatumikira Yehova pa nthawi yovuta kwambiri ndipo anakumana ndi mavuto aakulu. Ahabu, yemwe anali mfumu yosakhulupirika ya Isiraeli, anakwatira mkazi woipa dzina lake Yezebeli yemwe ankalambira Baala. Anthu awiriwa anachititsa kuti anthu ambiri azilambira Baala ndipo anapha aneneri a Yehova ambiri. Koma Eliya anapulumuka. Iye anapulumukanso chilala chifukwa choti ankadalira Yehova. (1 Maf. 17:2-4, 14-16) Eliya anadaliranso Yehova pa nthawi imene ankatsutsana ndi aneneri komanso anthu ena olambira Baala. Pa nthawi imeneyo, iye analimbikitsa Aisiraeli kuti azilambira Yehova. (1 Maf. 18:21-24, 36-38) Eliya anali ndi umboni wamphamvu wakuti Yehova ankamuthandiza pa nthawi yovutayi.
5-6. Malinga ndi 1 Mafumu 19:1-4, kodi Eliya anamva bwanji, nanga Yehova anasonyeza bwanji kuti ankamukonda?
5 Werengani 1 Mafumu 19:1-4. Yezebeli ananena kuti adzapha Eliya ndipo Eliyayo anachita mantha kwambiri moti anathawira ku Beere-seba. Iye anakhumudwa kwambiri mpaka kufika ‘popempha kuti afe.’ N’chifukwa chiyani anamva chonchi? Eliya sanali wangwiro ndipo ‘anali munthu ngati ife tomwe.’ (Yak. 5:17) N’kutheka kuti anafooka chifukwa cha nkhawa komanso kutopa kwambiri. Iye ankaganiza kuti zimene ankachita polimbikitsa kulambira koona sizinaphule kanthu. Ankaonanso kuti palibe chilichonse chimene chasintha mu Isiraeli ndipo mtumiki wa Yehova amene watsala ndi iye yekha. (1 Maf. 18:3, 4, 13; 19:10, 14) Mwina tikhoza kudabwa tikaganizira mmene mneneriyu anamvera. Koma Yehova anamumvetsa.
6 Yehova sanakalipire Eliya chifukwa chofotokoza mmene ankamvera. M’malomwake, anamuthandiza kuti apezenso mphamvu. (1 Maf. 19:5-7) Kenako Yehova anamuthandiza kusintha maganizo ake pomusonyeza mphamvu zake zodabwitsa. Anamuuzanso kuti padakali anthu 7,000 mu Isiraeli amene salambira Baala. (1 Maf. 19:11-18) Apatu Yehova anasonyeza Eliya kuti ankamukonda kwambiri.
YEHOVA ADZATITHANDIZA
7. Kodi nkhani ya Eliya imatilimbikitsa bwanji?
7 Kodi inunso mukukumana ndi mavuto amene akukudetsani nkhawa? N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti Yehova anamvetsa mmene Eliya ankamvera. Izi zimatitsimikizira kuti Yehova amamvetsanso mmene ifeyo timamvera. Iye amadziwa zimene sitingakwanitse, zimene tikuganiza komanso zimene zili mumtima mwathu. (Sal. 103:14; 139:3, 4) Nafenso tikamadalira Yehova, adzatithandiza kupirira mavuto athu.—Sal. 55:22.
8. Kodi Yehova adzakuthandizani bwanji mukakhala ndi nkhawa?
8 Tikakhala ndi nkhawa, tingayambe kuganiza kuti mavuto athu sangathe. Izi zikakuchitikirani, muzikumbukira kuti Yehova adzakuthandizani. Kodi angakuthandizeni bwanji? Iye amakupemphani kuti muzimuuza zimene zikukudetsani nkhawa ndipo amalonjeza kuti adzayankha mapemphero anu. (Sal. 5:3; 1 Pet. 5:7) Choncho muzikonda kupemphera n’kumauza Yehova mavuto anu. Sikuti adzalankhula nanu mwachindunji ngati mmene anachitira ndi Eliya. Koma adzakulankhulani kudzera m’Mawu ake komanso gulu lake. Nkhani za m’Baibulo zingakulimbikitseni komanso kukuthandizani kukhala ndi chiyembekezo. Nawonso abale ndi alongo anu angakulimbikitseni kwambiri.—Aroma 15:4; Aheb. 10:24, 25.
9. Kodi mnzathu wodalirika angatithandize bwanji?
9 Yehova anauza Eliya kuti apereke ntchito zina kwa Elisa. Zimenezi zinathandiza kuti Eliya akhale ndi mnzake yemwe angamulimbikitse. Ifenso tikafotokozera mnzathu wodalirika zinthu zimene zikutidetsa nkhawa, mnzathuyo akhoza kutilimbikitsa. (2 Maf. 2:2; Miy. 17:17) Ngati mumaona kuti mulibe mnzanu amene mungamufotokozere mavuto anu, mungapemphe Yehova kuti akuthandizeni kupeza Mkhristu yemwe angakulimbikitseni.
10. Kodi nkhani ya Eliya imatilimbikitsa bwanji, nanga lonjezo la pa Yesaya 40:28, 29 lingatithandize bwanji?
10 Yehova anathandiza Eliya kuti apirire mavuto ake ndipo anapitiriza kumutumikira mokhulupirika kwa zaka zambiri. Nkhani ya Eliyayi ndi yolimbikitsa kwambiri. Nafenso tikhoza kufooka chifukwa cha nkhawa. Koma tikamadalira Yehova, iye adzatipatsa mphamvu zoti tipitirize kumutumikira.—Werengani Yesaya 40:28, 29.
ANTHU ATATU AMENE ANKADALIRA YEHOVA
11-13. Kodi atumiki atatu a Mulungu anakumana ndi mavuto ati amene ankawadetsa nkhawa?
11 Pali anthu enanso otchulidwa m’Baibulo amene anakumana ndi mavuto. Mwachitsanzo, Hana anali wosabereka ndipo ankavutitsidwa kwambiri ndi mkazi mnzake. (1 Sam. 1:2, 6) Hana ankada nkhawa kwambiri moti ankangolira ndipo sankafuna kudya.—1 Sam. 1:7, 10.
Sal. 40:12) Mwana wake Abisalomu anamuukira kenako anaphedwa. (2 Sam. 15:13, 14; 18:33) Ndipo mnzake wapamtima anamuchitira chiwembu. (2 Sam. 16:23–17:2; Sal. 55:12-14) Masalimo ambiri amene Davide analemba amasonyeza kuti ankakhumudwa koma ankadalira kwambiri Yehova.—Sal. 38:5-10; 94:17-19.
12 Nayenso Mfumu Davide nthawi zina ankavutika ndi nkhawa. Tangoganizirani mavuto ena amene anakumana nawo. Iye ankadziimba mlandu kwambiri chifukwa cha zinthu zolakwika zimene anachita. (13 Munthu winanso amene analemba masalimo anayamba kusirira moyo wa anthu ochita zoipa. N’kutheka kuti munthu ameneyu anali wa m’banja la Asafu ndipo ankatumikira “m’malo opatulika aulemerero a Mulungu.” Munthuyu anada nkhawa kwambiri moti sankasangalala ndipo ankaona kuti zinthu sizikumuyendera. Iye anafika poganiza kuti madalitso amene Yehova amapereka si okwanira.—Sal. 73:2-5, 7, 12-14, 16, 17, 21.
14-15. Kodi tikuphunzira chiyani pa zitsanzo zitatu za m’Baibulo zimene takambiranazi?
14 Atumiki onse atatu amene tatchulawa ankadalira kwambiri Yehova. Iwo ankapemphera kwa iye n’kumuuza zimene zikuwadetsa nkhawa. Ankamufotokozera momasuka zimene zikuwavutitsa maganizo. Ndipo sanasiye kupita kumalo olambirira Yehova.—1 Sam. 1:9, 10; Sal. 55:22; 73:17; 122:1.
15 Yehova anawamvera chisoni ndipo anayankha mapemphero awo. Mwachitsanzo, Hana anapeza mtendere wamumtima. (1 Sam. 1:18) Davide analemba kuti: “Masoka a munthu wolungama ndi ochuluka, koma Yehova amamupulumutsa ku masoka onsewo.” (Sal. 34:19) Wolemba masalimo wina uja anafika poona kuti Yehova ‘wagwira dzanja lake lamanja’ ndipo akumupatsa malangizo othandiza. Iye anaimba kuti: “Kwa ine kuyandikira kwa Mulungu ndi chinthu chabwino. Yehova Ambuye Wamkulu Koposa ndiye pothawirapo panga.” (Sal. 73:23, 24, 28) Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani zimenezi? Nthawi zina tikhoza kukumana ndi mavuto aakulu amene angatidetse nkhawa, koma tikhoza kuwapirira. Chongofunika ndi kuganizira mmene Yehova anathandizira anthu ena, kumudalira, kupemphera kwa iye komanso kuchita zonse zimene amatiuza.—Sal. 143:1, 4-8.
TIKAMADALIRA YEHOVA ZINTHU ZIMATIYENDERA BWINO
16-17. (a) N’chifukwa chiyani sitiyenera kusiyana ndi Yehova komanso anthu ake? (b) Kodi tingapeze bwanji mphamvu?
16 Zitsanzo zitatuzi zimatiphunzitsanso mfundo ina yofunika yakuti sitiyenera kusiyana ndi Yehova komanso anthu ake. (Miy. 18:1) Mlongo wina dzina lake Nancy ankada nkhawa kwambiri mwamuna wake atamuthawa. Iye anati: “Nthawi zambiri sindinkafuna kuonana ndi anthu kapena kucheza nawo. Koma pamene ndinkapewa anthu m’pamene ndinkakhala wokhumudwa kwambiri.” Ndiyeno zinthu zinasintha pamene Nancy anayamba kuyesetsa kuthandiza anthu ena amene ankakumana ndi mavuto. Iye ananena kuti: “Ndinkamvetsera pamene anthuwo ankafotokoza mavuto awo. Ndinazindikira kuti ndikamawamvera chisoni ndinkasiya kudandaula kwambiri za mavuto anga.”
17 Tikhoza kupezanso mphamvu tikamapita kumisonkhano. Tikamasonkhana timapatsa Yehova mipata yoti ‘azitithandiza ndiponso kutilimbikitsa.’ (Sal. 86:17) Yehova amagwiritsa ntchito mzimu wake woyera, Mawu ake komanso anthu ake kuti azitilimbikitsa kumisonkhano. Misonkhano imatipatsanso mwayi woti ‘tizilimbikitsana.’ (Aroma 1:11, 12) Mlongo wina dzina lake Sophia ananena kuti: “Yehova komanso abale ndi alongo athu ndi amene anandithandiza kuti ndipirire. Ndinkaona kuti misonkhano ndi yofunika kwambiri. Ndipo ndazindikiranso kuti ndikamachita zambiri mumpingo komanso mu utumiki, ndimatha kupirira mavuto anga.”
18. Kodi Yehova angatithandize bwanji tikakhumudwa kwambiri?
18 Tikakhala ndi nkhawa, tizikumbukira kuti Yehova analonjeza kuti adzatithandiza panopa kuti tipirire ndipo adzathetsa mavuto athu m’tsogolo. Tikakhumudwa kwambiri, Yehova akhoza kutipatsa mtima wofuna kusintha komanso mphamvu yoti tisinthire.—Afil. 2:13.
19. Kodi lemba la Aroma 8:37-39 limatitsimikizira za chiyani?
19 Werengani Aroma 8:37-39. Zimene mtumwi Paulo analemba zimatitsimikizira kuti palibe chinthu chimene chingatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu. Koma kodi tingathandize bwanji abale ndi alongo athu amene ali ndi nkhawa? Nkhani yotsatira idzafotokoza zimene tingachite potsanzira chifundo cha Yehova komanso pothandiza abale ndi alongo amene ali ndi nkhawa.
NYIMBO NA. 44 Pemphero la Munthu Wovutika
^ ndime 5 Tikamada nkhawa kwambiri kapena kwa nthawi yaitali tikhoza kudwala komanso kusokonezeka maganizo. Ndiye kodi Yehova angatithandize bwanji? Tikambirana zimene Yehova anachita pothandiza Eliya pamene anali ndi nkhawa. Tikambirananso zitsanzo zina za m’Baibulo zimene zingatithandize kuti tizidalira Yehova tikakhala ndi nkhawa.
^ ndime 2 Mayina amunkhaniyi asinthidwa.
^ ndime 53 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Mngelo wa Yehova akudzutsa Eliya ndipo akumupatsa chakudya ndi madzi.
^ ndime 55 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Wolemba masalimo, yemwe anali wa m’banja la Asafu, akusangalala polemba masalimo komanso kuimba limodzi ndi Alevi anzake